1 Ndipo Rehabiamu anamka ku Sekemu, popeza Aisrayeli onse anadza ku Sekemu kumlonga ufumu.
2 Ndipo kunali kuti Yerobiamu mwana wa Nebati anacimva akali m'Aigupto, kumene anathawira kucokera ku maso a Solomo mfumu, pakuti Yerobiamu anakhala ku Aigupto.
3 Ndipo anatuma akukamuitana. Ndipo Yerobiamu ndi msonkhano wonse wa Israyeli anadza, nalankhulana ndi Rehabiamu, nati,
4 Atate wa nu analemeretsa gori lathu, ndipo inu tsono pepuzaniko nchito zosautsa za atate wanu, ndi gori lolemera lace limene anatisenza, ndipo tidzakutumikirani.
5 Ndipo iye anati kwa iwo, Bamukani, mukagone masiku atatu, pamenepo mukabwera kwa ine. Ndipo anthu anamuka.
6 Ndipo mfumu Rehabiamu anafunsira kwa mandoda, amene anaimirira pamaso pa Solomo atate wace, akali moyoiyeyo, nati, Inu mundipangire bwanji kuti ndiyankhe anthu awa?
7 Ndipo iwo anamuuza kuti, Mukakhala inu mtumiki wa anthu awa lero, ndi kuwatumikira ndi kuwayankha ndi kukamba nao mau okoma, tsono iwo adzakhala cikhalire atumiki anu.
8 Koma iye analeka uphungu wa mandodawo, umene anampangirawo, nakafunsira kwa acinyamata anzace oimirira pamaso pace,
9 nati kwa lwo, Kodi inu mundipangire bwanji kuti tiyankhe anthu awa anandiuza ine, kuti, Mupepuze gori limene atate wanu anatisenza ife?
10 Ndipo acinyamata anzace ananena naye, Dati, Mzitero ndi anthu awa adalankhula nanu, nati, Atate wanu analemeretsa gori lathu, koma inu mutipepuzire limenelo; mzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'cuuno mwa atate wanga.
11 Ndipo tsopano, popeza atate wanga anakusenzani gori lolemera, ine ndidzaonjezerapo pa gori lanu, atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.
12 Ndipo Yerobiamu ndi anthu onse anabwera kwa Rehabiamu tsiku lacitatu monga momwe anawauzira mfumu, nati, Bweraninso kwa ine tsiku lacitatu.
13 Ndipo mfumu inayankha anthu mau okalipa, naleka uphungu anampangira mandodawo,
14 nalankhula nao monga mwa uphungu wa acinyamata, nati, Atate wanga analemeretsa gori lanu, koma ine ndidzaonjezerapo pa gori lanu; atate wanga anakukwapulani ndi zikoti, koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira,
15 Potero mfumu siinamvera anthuwo, pakuti kusintha uku kunacokera kwa Yehova, kuti akhazikitse mau ace amene Yehova ananenetsa Abiya wa ku Silo kwa Yerobiamu mwana wa Nebati.
16 Ndipo pakuona Aisrayeli onse kuti mfumu siinawamvera iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tiri naye ciani Davide? inde tiribe colowa m'mwana wa Jese; tiyeni kwathu Aisrayeli inu; yang'aniranitu, nyumba yako, Davide. Momwemo Aisrayeli anacoka kumka ku mahema ao.
17 Kama ana aja a Israyeli akukhala m'midzi ya Yuda, Rehabiamu anakhalabe mfumu yao.
18 Pamenepo mfumu Rehabiamu anatuma Adoramu wamsonkho, ndipo Aisrayeli onse anamponya miyala, nafa. Ndipo mfumu Rehabiamu anafulumira kulowa m'gareta wace kuthawira ku Yerusalemu.
19 Motero Aisrayeli anapandukana ndi nyumba ya Davide kufikira lero.
20 Ndipo kunali, atamva Aisrayeli onse kuti Yerobiamu wabweranso, anatuma kumuitanira iye kumsonkhano, namlonga iye mfumu ya Aisrayeli onse; palibe munthu anatsata nyumba ya Davide koma pfuko lokha la Yuda.
21 Ndipo Rehabiamu anafika ku Yerusalemu, nasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda, ndi pfuko la Benjamini, ankhondo osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, kuyambana nayo nyumba ya Israyeli, kubwezanso ufumu kwa Rehabiamu mwana wa Solomo.
22 Ndipo mau a Mulungu anafika kwa Semaya mneneri wa Mulungu, nati,
23 Lankhula kwa Rehabiamu mwana wa Solomo mfumu ya Yuda, ndi kwa nyumba yonse ya Yuda, ndi Benjamini, ndi kwa anthu otsalawo, nuti,
24 Yehova atero, Musamuka, ndipo musakayambana ndi abale anu ana a Israyeli, bwererani yense kunyumba kwace; popeza cinthuci cacokera kwa Ine. Ndipo iwo anamvera mau a Yehova, natembenuka, nabwerera monga mwa mau a Yehova.
25 Ndipo Yerobiamu anamanga Sekemu m'mapiri a Efraimu, nakhalamo, naturukamo, namanga Penueli.
26 Ndipo Yerobiamu ananena m'mtima mwace, Ufumuwu udzabwereranso ku nyumba ya Davide.
27 Anthu awa akamakwera kukapereka nsembe m'nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, pamenepo mitima ya anthu awa idzatembenukiranso kwa mbuye wao, kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda; ndipo adzandipha, nadzabweranso kwa Rehabiamu mfumu ya Yuda.
28 Potero mfumu inakhala upo, napanga ana a ng'ombe awiri agolidi, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisrayeli inu milungu yanu imene inakuturutsani m'dziko la Aigupto.
29 Ndipo anaimika mmodzi ku Beteli, naimika wina ku Dani.
30 Koma cinthu ici cinasanduka: chimo, ndipo anthu anamka ku mmodziyo wa ku Dani.
31 Iye namanga nyumba za m'misanje, nalonga anthu acabe akhale ansembe, osati ana a Levi ai.
32 Ndipo Yerobiamu anaika madyerero mwezi wacisanu ndi citatu, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi olingana ndi madyerero aja a ku Yuda, napereka nsembe pa guwa la nsembe; anatero m'Beteli, nawaphera nsembe ana a ng'ombe aja anawapanga, naika m'Beteli ansembe a misanje imene anaimanga.
33 Ndipo anapereka nsembe pa guwa la nsembe analimanga m'Beteli, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi wacisanu ndi citatu, m'mwezi umene anaulingirira m'mtima mwa iye yekha, nawaikira ana a Israyeli madyerero, napereka nsembe pa guwa la nsembe, nafukiza zonunkhira.