1 Mafumu 13 BL92

Mneneri adzudzula Yerobiamu

1 Ndipo onani, munthu wa Mulungu anacokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Beteli; ndipo Yerobiamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.

2 Ndipo iye anapfuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m'nyumba ya Davide, dzina lace ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu.

3 Ndipo iye anapatsa cizindikilo tsiku lomwelo, nari, Cizindikilo cimene Yehova ananena ndi ici, Taonani guwali la nsembe lidzang'ambika, ndi phulusa liri pa ilo lidzatayika.

4 Ndipo kunacitika, pa kumva mfumu mau a munthu wa Mulungu amene anawapfuula, kutemberera guwa la nsembe m'Beteli, Yerobiamu anatansa dzanja lace ali ku guwalo, nati, Mgwireni iye. Ndipo dzanja lace analitansira kwa iye linauma, kuti sanatha kulipfunyatitsanso.

5 Ndiponso guwalo linang'ambika, ndi phulusa la pa guwalo linatayika, monga mwa cizindikilo cimene munthu wa Mulungu anapatsa mwa mau a Mulungu.

6 Ndipo mfumu inayankha niti kwa munthu wa Mulungu, Undipembedzere Yehova Mulungu wako, nundipempherere, kuti dzanja langa libwerenso kwa ine. Ndipo munthuyo wa Mulungu anapembedza Yehova, ndipo dzanja la mfumu linabwezedwa kwa iye momwemo mwa kale.

7 Mfumu niti kwa munthu wa Mulungu, Tiye kwathu, ukapumule, ndikupatse mphatso.

8 Ndipo munthu wa Mulungu ananena ndi mfumu, Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowa kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno.

9 Pakuti potero ndinalamulidwa ndi mau a Yehova, ndi kuti, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.

10 Tsono iye anayenda njira yina osabwerera njira yomweyo anaidzera pakudza ku Beteli.

Mneneri wosamverayo aphedwa ndi mkango

11 Ndipo ku Beteli kunakhala mneneri wokalamba, ndipo mwana wace wina anadzamfotokozera macitidwe onse anawacita munthu wa Mulunguyo tsiku lomwelo m'Beteli ndi mau ace anawanena ndi mfumu; inde omwe aja iwo anamfotokozera atate wao.

12 Ndipo atate wao anati kwa iwo, Wapitira njira yiti? popeza ana ace adaona njira analowera munthu wa Mulungu anacokera ku Yudayo.

13 Nanena ndi ana ace, Ndimangireni mbereko pa buru. Namangira iwo mbereko pa buru, naberekekapo iye.

14 Natsata munthu wa Mulungu, nampeza ali, tsonga patsinde pa mtengo wathundu, nanena naye, Kodi ndiwe munthu wa Mulungu amene uja anacokera ku Yuda? Nati, Ndine amene.

15 Tsono ananena naye, Tiye kwathu, ukadye mkate.

16 Nan iye, Sindingabwerere nawe kukalowa kwanu, kapena kudya mkate, kapena kumwa nawe madzi pano;

17 pakuti mau a Yehova anadza kwa ine, nati Usakadye mkate, kapena kumwa madzi kumeneko, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.

18 Ndipo anati kwa iye, Inenso ndine mneneri wonga iwe, ndipo mthenga analankhula ndi ine mwa mau a Yehova, nati, Kambwezere kwanu, kuti akadye mkate, namwe madzi. Koma anamnamiza.

19 Tsono anabwerera naye, nakadya kwao, namwa madzi.

20 Ndipo kunacitika iwo ali cikhalire pagome, mau a Yehova anadza kwa mneneri amene anambwezayo,

21 napfuula iye kwa munthu uja wa Mulungu anacokera ku Yudayo, nati, Atero Yehova, Pokhala sunamvera mau a pakamwa pa Yehova, osasunga lamulo lija Yehova Mulungu wako anakulamulira,

22 koma unabwerera nudya mkate, ndi kumwa madzi paja pomwe iye anakuuza, Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, mtembo wako tsono sudzaikidwa ku manda a atate ako.

23 Ndipo kunacitika, atadya iye mkate, ndi kumwa madzi, anammangira mbereko pa buru mneneri amene anambwezayo.

24 Ndipo atacoka iye, mkango unakomana naye panjira, numupha, ndipo mtembo wace unagwera m'njiramo, buru naima pafupi, mkangonso unaima pafupi ndi mtembo.

25 Ndipo onani, anthu anapitapo naona mtembo wogwera m'njiramo, ndi mkango uli ciimire pafupi ndi mtembo, nadzanena m'mudzi m'mene munakhala mneneri wokalamba uja.

26 Ndipo mneneri amene uja anambweza panjirayo atamva, anati, Ndiye munthu uja wa Mulungu amene sanamvera mau a Yehova; cifukwa cace Yehova wampereka kwa mkango, numkadzula numupha, monga mwa mau a Yehova analankhula nayewo.

27 Iye nanena ndi ana ace, nati, Ndimangireni mbereko pa buru. Namangira mbereko.

28 Namuka iye, napeza mtembo wace wogwera m'njira, ndi buru ndi mkango ziti ciimire pafupi ndi mtembo. Mkango udalibe kudya mtembo, kapena kukadzula buru.

29 Ndipo mneneri ananvamula mtembo wa munthu wa Mulunguyo, nausenza pa buru, nabwera nao, nalowa m'mudzi mneneri wokalamba kumlira ndi kumuika.

30 Ndipo mtembo wace anauika m'manda a iye mwini, namlira iwo maliro, nati, Mayo, mbale wanga!

31 Ndipo kunacitika, atamuika iye, ananena ndi ana ace, nati, Nkadzamwalira ine mudzandiike ine m'manda momwemo mwaikidwa munthu wa Mulunguyo, ikani mafupa anga pafupi ndi mafupa ace.

32 Popeza mau aja anawapfuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe la ku Beteli, ndi kutemberera nyumba zonse za misanje iri m'midzi ya ku Samariya, adzacitika ndithu.

33 Pambuyo pa ici Yerobiamu sanabwerera pa njira yace yoipa, koma analonganso anthu acabe akhale ansembe a misanje, yensewakufuna yemweyu anampatula akhale wansembe wa misanje,

34 Ndimo umu munali chimo la nyumba ya Yerobiamu, limene linaidula ndi kuiononga pa dziko lapansi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22