1 Mafumu 8 BL92

Aika likasa m'Kacisi

1 Pamenepo Solomo anasonkhanitsa akulu a Israyeli, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israyeli, kwa mfumu Solomo m'Yerusalemu, kukatenga likasa la cipangano ca Yehova m'mudzi wa Davide, ndiwo Ziyoni.

2 Ndipo anthu onse a Israyeli anasonkhana kwa mfumu Solomo kukadyereram'mwezi wa Etanimu, ndiwo mwezi wacisanu ndi ciwiri.

3 Ndipo akulu onse a Israyeli anadza, ansembe nanyamula likasa.

4 Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndi cihema cokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m'cihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi.

5 Ndipo mfumu Solomo ndi msonkhano wonse wa Israyeli wosonkhana kwa iye anali naye kulikasa, naphera nkhosa ndi ng'ombe za nsembe zosawerengeka ndi zosadziwika, cifukwa ca unyinji wao.

6 Ndipo ansembe analonga likasa la cipangano ca Yehova kumalo kwace, ku monenera mwa nyumba, ku malo opatulikitsa, munsi mwa mapiko a akerubi,

7 Popeza akerubiwo anatambasula mapiko ao awiri pamwamba pa likasa, ndipo akerubiwo anaphimba pamwamba pa likasa ndi mphiko zace.

8 Ndipo mphikozo zinatalika kuti nsonga za mphiko zidaoneka ku malo opatulika cakuno ca monenera; koma sizinaoneka kubwalo; ndipo zikhala pomwepo mpaka lero lino.

9 Munalibe kanthu m'likasamo koma magome awiri aja amwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israyeli, poturuka iwo m'dziko la Aigupto.

10 Ndipo kunacitika ataturuka ansembe m'malo opatulika, mtambo unadzaza nyumba ya Yehova,

11 ndipo ansembe sanakhoza kuimirira kurumikira cifukwa ca mtambowo, popeza ulemerero wa Yehova unadzazanyumba ya Yehova.

Mau a Saloma popereka Kacisi kwa Mulungu

12 Pamenepo Solomo anati, Yehova ananena kuti adzakhala m'mdima waukuru.

13 Ine ndakumangirani ndithu nyumba yokhalamo Inu, ndiyo malo okhalamo inu nthawi zosatha.

14 Ndipo mfumu inapotoloka nkhope yace, nidalitsa msonkhano wonse wa Israyeli, Ndi msonkhano wonse wa Israyeli unaimirira.

15 Nati iye, Wolemekezeka ndi Yehova Mulungu wa Israyeli amene analankhula m'kamwa mwace ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi dzanja lace, nati,

16 Kuyambira tsiku lakuturutsa Ine anthu anga Aisrayeli m'dziko la Aigupto, sindinasankha mudzi uli wonse mwa mafuko onse a Israyeli kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, koma ndinasankha Davide kukhala mfumu ya anthu anga Aisrayeli.

17 Ndipo Davide atate wanga anafuna m'mtima mwace kumangira dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.

18 Koma Yehova ananena ndi Davide atate wanga, Popeza unafuna m'mtima mwako kumangira dzina langa nyumba, unacita bwino kuti m'mtima mwako unatero.

19 Koma usamange ndiwe nyumbayo, koma mwana wako adzaturuka m'cuuno mwako, iyeyo adzamangira dzina langa nyumba.

20 Ndipo Yehova wakhazikitsa mau ace analankhulawo, ndipo ndauka ndine m'malo mwa Davide atate wanga, ndipo ndikhala pa mpando wacifumu wa Israyeli monga adalonjeza Yehova, ndipo ndamangira dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.

21 Ndipo ndakonzera malo likasalo, m'mene muli cipangano ca Yehova, cimene anapangana ndi makolo athu pamene anawaturutsa m'dziko la Aigupto.

22 Ndipo Solomo anaimirira ku guwa la nsembe la Yehova pamaso pa msonkhano wonse wa Israyeli, natambasulira manja ace kumwamba, nati,

23 Yehova Mulungu wa Israyeli, palibe Mulungu wolingana ndi inu m'thambo la kumwamba, kapena pa dziko lapansi, wakusungira cipangano ndi cifundo akapolo anu akuyenda ndi mtima wonse pamaso panu,

24 wakusungira mtumild wanu Davide atate wanga cimene mudamlonjezaco; munalankhulanso m'kamwa mwanu ndi kukwaniritsa ndi dzanja lanu monga lero lino.

25 Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israyeli, msungireni mtumiki wanu Davide atate wanga cimene cija mudamlonjezaco, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wokhala pa mpando wacifumu wa Israyeli; komatu ana ako acenjere njira yao, kuti akayende pamaso panga monga umo unayendera iwe pamaso panga.

26 Ndipo tsopano, Mulungu wa Israyeli, atsimikizike mau anu amene munalankhula ndi mtumiki wanu Davide atate wanga.

27 Kodi Mulungu adzakhala ndithu pa dziko lapansi? Taonani, thambo ndi m'Mwambamwamba zicepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.

28 Koma muceukire pemphero la kapolo wanu, ndi pembedzero lace, Yehova Mulungu wanga, kumvera kulira ndi kupempha kwace kumene kapolo wanu apempha pamaso panu lero;

29 kuti maso anu atsegukire nyumba yino usiku ndi usana, kumalo kumene munanenako, Dzina langa lidzakhala komweko; kuti mumvere pemphero limene adzapemphera kapolo wanu lolunjika kumalo kuno.

30 Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisrayeli, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu m'Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.

31 Ngati munthu akacimwira mnzace, ndi lumbiro likaikidwa pa iye kumlumbiritsa, ndipo akadzalumbira patsogolo pa guwa la nsembe lanu m'nyumba yino;

32 mverani Inu pamenepo m'mwambamo, ndipo citani, weruzani akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera cimo lace, ndi kulungamitsa wolungamayo kumbwezera monga cilungamo cace.

33 Ndipo anthu anu Aisrayeli akawakantha adani ao cifukwa ca kucimwira Inu, ndipo akabweranso kwa Inu, lodi kubvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedza Inu m'nyumba muno;

34 pamenepo mverani Inu m'Mwambamo, ndi kukhululukira cimo la anthu anu Aisrayeli, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.

35 Pamene kumwamba kwatsekeka, ndipo kulibe mvula cifukwa ca kucimwira Inu, nakapemphera iwo molunjika kumalo kuno, ndi kubvomereza dzina lanu, ndi kutembenuka kusiya zoipa zao, pakuwasautsa Inu;

36 pamenepo mverani Inu m'Mwamba, ndi kukhululukira cimo la akapolo anu, ndi la, anthu anu Aisrayeli; pakuti muwaphunzitsa njira yokoma ayenera kuyendamo, ndi kupatsa mvula pa: dziko lanu, limene munawapatsa anthu anu likhale colowa cao.

37 M'dziko mukakhala odala, mukakhala mliri, mlaza, cinoni, dzombe, kapena kapuci, adani ao akawamangira misasa m'dziko la midzi yao, mukakhala mliri uti wonse, kapena nthenda;

38 tsono pempho ndi pembedzero liri lonse akalipempha munthu ali yense, kapena anthu anu onse Aisrayeli, pakuzindikira munthu yense cinthenda ca mtima wa iye yekha, ndi kutambasulira manja ace ku nyumba yino;

39 pamenepo mverani Inu m'Mwamba mokhala Inu, ndi kukhululukira, ndi kucita, ndi kubwezera munthu yense monga njira zace zonse, amene Inu mumdziwa mtima wace, popeza Inu, Inu nokha, mudziwa mitima ya ana onse a anthu;

40 kuti aope Inu masiku onse akukhala iwowo m'dziko limene Inu munapatsa makolo ao.

41 Ndiponso kunena za mlendo, wosati wa anthu anu Aisrayeli, koma wakufumira m'dziko lakutali cifukwa ca dzina lanu,

42 popeza adzamva za dzina lanu lalikuru ndi dzanja lanu lamphamvu ndi mkono wanu wotambasuka; akabwera iyeyo nadzapemphera molunjika ku nyumba yino;

43 mverani Inu m'Mwamba mokhala Inu, ndipo citani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa Inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu, kuopa Inu, monga amatero anthu anu Aisrayeli, ndi kuti adziwe kuti nyumba yino ndaimangayi yachedwa dzina lanu.

44 Akaturuka anthu anu kukayambana nkhondo ndi adani ao, kumene konse inu mudzawatuma, ndipo akapemphera kwa Yehova molunjika ku mudzi uno munausankha Inu, ndi ku nyumba ndamangira dzina lanu;

45 pamenepo mverani Inu m'Mwamba pempho ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao.

46 Akacimwira Inu, popeza palibe munthu wosacimwa, ndipo mukakwiya nao ndi kuwapereka kwa adani, kuti iwo awatenge ndende kumka nao ku dziko la adani, ngati kutali kapena kufupi,

47 ndipo akakumbukila mitima yao, ali kudziko kumene anatengedwa ukapolo, nakalapa, nakapembedza inu m'dziko la iwo anawatenga ndende, ndi kuti, Tacimwa, ndipo tacita mphulupulu, tacita moipa;

48 ndipo akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, m'dziko la adani ao adawatenga ndendewo, ndipo akapemphera kwa Inu molunjika ku dziko lao munapatsa makolo aolo, ku mudzi munausankha Inu, ndi kunyumba ndamangira dzina lanu;

49 pamenepo mverani Inu pemphero ndi pembedzero lao m'Mwamba mokhala Inumo, ndi kulimbitsa mlandu wao,

50 ndi kukhululukira anthu anu adacimwira Inu ndi mphulupulu zao zonse adaparamula nazo kwa Inu; ndipo muwacititsire cifundo iwo amene anawagwira ndende, kuti awacitire cifundo;

51 pakuti awa ndi anthu anu ndithu, ndi colowa canu cimene munaturutsa m'Aigupto, m'kati mwa ng'anjo ya citsulo;

52 kuti maso anu akatsegukire pembedzero la kapolo wanu ndi pembedzero la anthu anu Aisrayeli, kuwamveram'menemonseakapfuula kwa Inu.

53 Popeza Inu munawapatula pa anthu onse a pa dziko lapansi akhale colowa canu, monga munanena ndi dzanja la Mose mtumiki wanu, pamene munaturutsa makolo athu m'Aigupto, Yehova Mulungu Inu.

Solomo adalitsa Aisrayeli

54 Ndipo kunali kuti atatsiriza Solomo kupemphera kwa Yehova pemphero ndi pembedzero lino lonse, ananyamuka ku guwa la nsembe la Yehova pomwe analikugwada pa mabondo ace, ndi manja ace otambasulira kumwamba.

55 Naimirira, nadalitsa msonkhano wonse wa Israyeli ndi mau okweza, nati,

56 Wolemekezeka ndi Yehova amene anapumulitsa anthu ace Aisrayeli, monga mwa zonse analonjezazo; sanatayika mau amodzi a mau ace onse abwino, amene analankhula ndi dzanja la Mose mtumiki wace.

57 Yehova Mulungu wathu akhale nafe monga umo anakhalira nao makolo athu, asatisiye kapena kutitaya;

58 kuti atitembenuzire kwa iye yekha mitima yathu iyende m'njira zace zonse, ndi kusunga malamulo ace onse ndi malemba ace ndi maweruzo ace, amene anawalamulira makolo athu.

59 Ndipo mau anga amenewa ndapembedzera nao pamaso pa Yehova akhale pafupi ndi Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, kuti alimbitse mlandu wa kapolo wace, ndi mlandu wa anthu ace Aisrayeli, mlandu wa tsiku pa tsiku lace;

60 kuti anthu onse a pa dziko lapansi akadziwe kuti Yehova ndiye Mulungu, palibe wina.

61 Mitima yanu ikhale yangwiro ndi Yehova Mulungu wathu, kuyenda m'malemba ace ndi kusunga malamulo ace, monga lero lino.

62 Ndipo mfumu ndi anthu onse a Israyeli pamodzi naye anaphera nsembe pamaso pa Yehova.

63 Ndipo Solomo anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israyeli onse anapereka nyumbayo ya Yehova.

64 Tsiku lomwelo mfumu inapatulira Mulungu pakati pace pa bwalo la ku khomo la nyumba ya Yehova; pakuti pomwepo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere; popeza guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova lidacepa kulandira nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere.

65 Ndipo nthawi yomweyo Solomo anacita madyerero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndi Israyeli yense pamodzi naye, msonkhano waukuru wakuyambira polowera ku Hamati kufikira ku nyanja ya ku Aigupto, masiku asanu ndi awiri, ndi masiku asanu ndi awiri ena, ndiwo masiku khumi mphambu anai.

66 Tsiku lacisanu ndi citatu anawauza anthu apite; ndipo iwo anadalitsa mfumu, napita ku mahema ao osekera ndi okondwera mtima cifukwa ca zokoma zonse Yehova anacitira Davide mtumiki wace, ndi Israyeli anthu ace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22