1 Koma nyumba ya iye yekha Solomo anaimanga zaka khumi mphambu zitatu, natsiriza nyumba yace yonse.
2 Anamanganso nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano, m'litali mwace munali mikono zana limodzi, kupingasa kwace mikono makumi asanu, ndi msinkhu wace mikono makumi atatu; naisanja pa mizere inai ya mapanda amkungudza, ndi mitanda yamkungudza yotanthalika mapandawo.
3 Ndipo inayalidwa ndi mkungudza pamwamba pa zipinda makumi anai mphambu zisanu zolongosoledwa pa mapanda, mzere umodzi zipinda khumi mphambu asanu.
4 Ndipo panali mazenera m'mizere itatuyo, zenera limodzi lopenyana ndi linzace mizere itatu.
5 Ndipo makomo onse ndi mphuthu zonse zinali zamphwamphwa maonekedwe ace, ndipo zenera limodzi linapenyana ndi linzace mizere Itatu.
6 Ndipo anamanga khumbi la nsanamira, m'litali mwace munali mikono makumi asanu, kupingasa kwace mikono makumi atatu; ndipo panali khumbi lina patsogolo pace, ndi nsanamira ndi mitanda patsogolo pacepo.
7 Ndipo anamanga khumbi la mpando wacifumu loweruziramo iye, ndilo khumbi la mirandu, ndipo linayalidwa ndi mkungudza pansi ndi posanja.
8 Ndipo nyumba yace yakukhalamo iye, m'bwalo lina la m'tsogolo mwa khumbilo, linamangidwa cimodzimodzi. Anammangiranso nyumba mwana wamkazi wa Farao, amene adamkwatira Solomo, yofanafana ndi khumbi limeneli.
9 Izi zonse zinali za miyala ya mtengo wapatali yosemasema, ya muyeso muyeso, yoceka ndi mipeni ya mano mana m'katimo ndi kunjako, kuyambira kumazikokufikira kumutu, momwemonso kunjako ku bwalo lalikuru,
10 Ndipo maziko ace anali a miyala ya mtengo wapatali, ndiyo miyala yaikulu, miyala ya mikono khumi, ndi miyala ya mikono isanu ndi itatu.
11 Ndi pamwamba pace panali miyala ya mtengo wapatali, ndiyo miyala yosemasema monga muyeso wace, ndi mitengo yamkungudza.
12 Ndipo bwalo lalikuru lozingapo linali ndi mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungundza, monga bwalo la pakati pa nyumba ya Yehova, ndi likole la nyumbayo.
13 Ndipo mfumu Solomo anatuma anthu kukatenga Hiramu ku Turo.
14 Iyeyo anali mwana wace wa mkazi wamasiye wa pfuko la Nafitali, atate wace anali munthu wa ku Turo, mfundi wa mkuwa; ndipo iye anadzala ndi nzeru ndi luntha ndi luso kugwira nchito zonse za mkuwa. Ndipo anadza kwa mfumu Solomo namgwirira nchito zace zonse.
15 Popeza iyeyu anaunda nsanamira ziwiri zamkuwa, msinkhu wace wa imodzi unali mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndipo cingwe ca mikono khumi mphambu iwiri cinayesa thupi la nsanamira imodzi.
16 Ndipo anapanga mitu iwiri ya mkuwa wosungunula, kulika pamwamba pa nsanamirazo, msinkhu wace wa mutu wina unali mikono isanu, ndi msinkhu wa mutu unzace mikono isanu.
17 Ndipo panali maukonde olukaluka ndi zoyangayanga, zokolana za pa mitu imene inali pamwamba pa nsanamira; zisanu ndi ziwiri za pa mutu wina, ndi zisanu ndi ziwiri za pa mutu unzace.
18 M'mwemo anapanga nsanamira, ndipo panali mizere iwiri yozungulira ukonde umodzi, kukuta ndi makangaza mituyi inali pamwambapo, nacita momwemo ndi mutu winawo.
19 Ndipo mituyi inali pamwamba pa nsanamira za pa likole inali ngati akakombo malembedwe ace, a mikono inai.
20 Ndipo panalinso mitu pamwamba pa nsanamira ziwirizo, pafupi pa mimbayo, inali m'mbali mwace mwa ukondewo; ndipo makangazawo anali mazana awiri, akukhala mizere yozinga nda nda mutu winawo.
21 Ndipo anaimiritsa nsanamirazi pa likole la Kacisi; naimiritsa nsanamira ya ku dzanja lamanja, nacha dzina lace Yakini; naimiritsa nsanamira yakumanzere, nacha dzina lace Boazi.
22 Ndipo pamwamba pa nsanamirazo panali ngati akakombo malembedwe ace; motero anaitsiriza nchito ya nsanamirazo.
23 Ndipo anayenganso thawale lamkuwa, kukamwa kwace kunali kwa mikono khumi, linali lozunguniza, ndi msinkhu wace unali mikono isanu; ndi cingwe ca mikono makumi atatu cinalizungulira.
24 Ndipo m'khosi mwace munali ngati zikho zozinganiza m'mkono umodzi zikho khumi zakuzinganiza thawalelo; zikhozo zinayengedwa m'mizere iwiri poyengedwa thawalelo.
25 Linasanjikika pa ng'ombe khumi mphambu ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, zitatu kumadzulo, zitatu kumwera, zitatu kum'mawa; ndipo thawalelo linakhazikika pamwamba pa izo; ndipo nkholo zao zinayang'anana.
26 Ndipo kucindikira kwace kunali ngati m'manja mwa munthu, ndipo mlomo wace unasadamuka ngati mlomo wa comwera, ngati maluwa akakombo, analowamo madzi a mitsuko yaikuru zikwi ziwiri.
27 Ndipo anapanga maphaka khumi amkuwa, m'litali mwace mwa phaka limodzi mikono inai, ndi kupingasa kwace mikono inai, ndi msinkhu wace mikono itatu.
28 Ndipo mapangidwe a maphakawo anali otere: anali nao matsekerezo ao, ndipo matsekerezo anali pakati pa mbano.
29 Ndipo pa matsekerezo a pakati pa mbano panali ngati mikango ndi ng'ombe ndi akerubi, ndi pamwamba pa mbano panali cosanjikirapo; ndipo pansi pa mikango ndi ng'ombe panaphatikizika zotsetseremba zoyangayanga zokoloweka.
30 Ndipo phaka lid lonse linali ndi njinga zamkuwa zinai ndi mitanda yamkuwa, ndipo ngondya zace zinai zinali ndi mapewa; pansi pa thawale panali mapewa oyengeka pa mbali pa zophatikizika zonse.
31 Ndipo pakamwa pace m'katimo pamwamba pa cosanjikira, panayesa mkono umodzi; koma pakamwa pace panali posadamuka, monga mapangidwe ace a cosanjikira, mkono umodzi ndi nusu; ndiponso pakamwa pace panali zolemba ndi matsekerezo ace anali amphwamphwa, si ozunguniza.
32 Ndipo njinga zinai zinali pansi pa matsekerezo, ndi mitanda ya njinga inali m'mphakamo, ndi msinkhu wa njinga imodzi unali mkono umodzi ndi nusu.
33 Ndipo mapangidwe a njinga analingana ndi mapangidwe a njinga za gareta, mitanda yace ndi mkombero wace ndi nthiti zace ndi mtima wace zonsezo zinayengedwa.
34 Ndipo panali ngati mapewa anai pansi pa ngondya zinai za phaka limodzi, mapewawo anali a phaka lomwelo.
35 Ndipo pamwamba pa phaka panali khoma lozunguniza, msinkhu wace nusu ya mkono; ndi pamwamba pa phaka panali mbano zace ndi matsekerezo a phaka lomwelo.
36 Ndipo m'mapanthi mwa mbano zace ndi pa matsekerezo ace analemba ngati akerubi ndi mikango ndi migwalangwa, monga mwa malo ace a zonsezo, ndi zoyangayanga zozungulira.
37 Motero anapanga maphaka khumiwo, anafanana mayengedwe ao muyeso wao ndi maonekedwe ao.
38 Ndipo anapanga mbiya zamphwamphwa khumi zamkuwa; m'mbiya imodziyo munalowamo madzi a mitsuko yaikuru makumi anai, ndipo mbiya iri yonse inali ya mikono inai: pa phaka liri lonse la maphaka aja khumi panakhala mbiya imodzi.
39 Ndipo anaika maphaka asanu ku dzanja lamanja la nyumba, ndi maphaka asanu ku dzanja lamanzere la nyumba; naika thawalelo ku dzanja lamanja la nyumba kum'mawa kupenya kumwera.
40 Ndipo Hiramu anayenga mbiyazo ndi zoolera ndi mbale zowazira. Motero Hiramu anatsiriza kupanga nchito yonse anaicitira mfumu Solomo ya m'nyumba ya Yehova.
41 Nsanamira ziwirizo, ndi mbale za mitu inali pamwamba pa nsanamira ziwirizo, ndi maukonde awiri ophimbira mbale ziwiri za mitu inali pamwamba pa nsanamirazo,
42 ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwo, mizere iwiri ya makangaza a ukonde umodzi kuphimbira mbale ziwiri za mitu inali pa nsanamirazo,
43 ndi maphaka khumiwo ndi mbiya khumi ziri pa maphakawo,
44 ndi thawale limodzilo, ndi ng'ombe khumi mphambu ziwirizo pansi pa thawale;
45 ndi miphikayo, ndi zoolerazo, ndi mbalezo; inde zotengera zonse zimene Hiramu anampangira mfumu Solomo za m'nyumba ya Yehova, zinali za mkuwa wonyezimira.
46 Mfumu inaziyenga pa cidikha ca ku Yordano, m'dothe ladongo, pauti pa Sukoti ndi Zaritani.
47 Ndipo Solomo anazileka zipangizo zonse osaziyesa, popeza zinacuruka ndithu; kulemera kwace kwa mkuwa wonsewo sikunayeseka.
48 Ndipo Solomo anapanga zipangizo zonse za m'nyumba ya Mulungu: guwa la nsembe lagolidi, ndi gome lagolidi loikapo mikate yoonekera;
49 ndi zoikapo nyali za golidi woyengetsa, zisanu ku dzanja lamanja, zisanu kulamanzere, cakuno ca monenera, ndi maluwa ndi nyali ndi mbano zagolidi;
50 ndi zikho, ndi zozimira nyali, ndi mbale, ndi zipande, ndi zopalira mota za golidi woyengetsa, ndi zomangira zitseko zagolidi, za zitseko za cipinda ca m'katimo, malo opatulikitsa, ndiponso za zitseko za nyumba ya Kacisi.
51 Motero nchito zonse zinatsirizika, zimene mfumu Solomo anacitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomo analonga zinthu adazipatula Davide atate wace, ndizo siliva ndi golidi ndi zipangizo zomwe naziika mosungira cuma ca nyumba ya Yehova.