1 Ndipo Aaramu ndi Aisrayeli anakhala cete zaka zitatu, osathirana nkhondo.
2 Koma kunacitika caka cacitatu, kuti Yehosafati mfumu ya Yuda anatsikira kwa mfumu ya Israyeli.
3 Ndipo mfumu ya Israyeli ananena ndi anyamata ace, nati, Kodi simudziwa kuti Ramoti Gileadi ngwathu, ndipo tangokhala cete, osaulanditsa m'dzanja la mfumu ya Aramu.
4 Tsono anati kwa Yehosafati, Kodi udzapita nane kunkhondo ku Ramoti Gileadi? Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israyeli, M'mene ukhalira iwe ndi momwe ndikhalira ndine; anthu anga monga anthu ako, akavalo anga monga akavale ako.
5 Ndipo Yehosafati ananena ndi mfumu ya Israyeli, Fuusira ku mau a Yehova lero.
6 Pamenepo mfumu ya Israyeli inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Gileadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m'dzanja la mfumu.
7 Koma Yehosafati anati, Kodi pano palibe mneneri wina wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye?
8 Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wace wa Yimla. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.
9 Tsono mfumu ya Israyeli anaitana mdindo, nati, Kamtenge msanga Mikaya mwana wa Yimla.
10 Ndipo mfumu ya Israyeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala onse awiri, yense pa mpando wacifumu wace, obvala zobvala zao zacifumu pabwalo pa khomo la cipata ca Samaria; ndipo aneneri onse ananenera pamaso pao.
11 Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zacitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi mudzagunda nazo Aaramu mpaka atatha psiti,
12 Ndipo aneneri onse ananena momwemo, nati, Kwerani ku Ramoti Gileadi, ndipo mudzacita mwai; popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.
13 Tsono mthenga uja udakaitana Mikaya unanena naye, nati, Taona, mau a aneneri abvomerezana zokoma kwa mfumu ndi m'kamwa m'modzi; mau ako tsono afanane ndi mau a wina wa iwowo, nunene zabwino.
14 Koma Mikaya anati, Pali Yehova, zimene Yehova adzanena nane ndidzanena ine.
15 Ndipo atafika kwa mfumu, mfumu inati kwa iye, Mikaya, kodi tizimuka ku Ramoti Gileadi kukathira nkhondo, kapena tileke? Nati iye, Kwerani, ndipo mudzacita mwai, popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.
16 Ndipo mfumu inati, Ndikulumbiritse kangati kuti undiuze zoona zokha zokha m'dzina la Yehova?
17 Nati iye, Ndinaona Aisrayeli onse obalalika pamapiri ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo Yehova anati, Izi ziribe mwini, yense abwerere ndi mtendere ku nyumba yace.
18 Pamenepo mfumu ya Israyeli inanena ndi Yehosafati, Kodi sindinakuuza kuti uyu sadzanenera za ine zabwino, koma zoipa?
19 Ndipo anati, Cifukwa cace tamverani mau a Yehova, Ndinaona Yehova alikukhala pa mpando wace wacifumu, ndi khamu lonse la Kumwamba liri ciriri m'mbali mwace, ku dzanja lamanja ndi lamanzere,
20 Nati Yehova, Adzanyenga Ahabu ndani, kuti akwere nagwe ku Ramoti Gileadi? Ndipo anati wina mwakuti, wina mwakuti.
21 Pamenepo mzimu wina unaturuka, nuima pamaso pa Yehova, nuti, Ndidzamnyenga ndine. Nati Yehova kwa iye, Motani?
22 Nati, Ndidzaturuka, ndidzakhala mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri ace onse. Nati, Udzamnyengadi, nudzakhozanso; turuka, ukatero kumene.
23 Ndipo tsopano taonani, Yehova waika mzimu wonama m'kamwa mwa aneneri anu onse awa, ndipo Yehova ananena coipa ca inu.
24 Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenana anasendera, napanda Mikaya patsaya, nati, Mzimu wa Yehova wandicokera bwanji, kulankhula ndi iwe?
25 Mikaya nati, Taona, udzapenya tsiku lolowa iwe m'cipinda ca pakati kubisala.
26 Pamenepo inati mfumu ya Israyeli, Tengani Mikaya, mumbweze kwa Amoni kalonga wa mudzi, ndi kwa Yoasi mwana wa mfumu;
27 ndipo muziti, Itero mfumu, Khazikani uyu m'kaidi, mumdyetse cakudya ca nsautso, ndi madzi a nsautso, mpaka ndikabwera ndi mtendere.
28 Ndipo Mikaya anati, Mukabwera ndithu ndi mtendere Yehova sanalankhula mwa ine. Nati, Mvetsani, anthu inu nonse.
29 Tsono mfumu ya Israyeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakwera ku Ramoti Gileadi.
30 Ndipo mfumu ya Israyeli inanena ndi Yehosafati, Ine ndidzadzizimbaitsa, ndi kulawa kunkhondo, koma bvala iwe zobvala zako zacifumu. Ndipo mfumu ya Israyeli inadzizimbaitsa, nilowa kunkhondo.
31 Tsono mfumu ya Aramu idalamulira akapitao makumi atatu mphambu ziwiri za magareta ace, niti, Musaponyana ndi anthu ang'ono kapena akuru, koma ndi mfumu ya Israyeli yokha.
32 Ndipo kunali, akapitao a magareta ataona Yehosafati, anati, Zedi uyu ndiye mfumu ya Israyeli imene, napotolokera kukaponyana naye; koma Yehosafati anapfuula.
33 Ndipo pamene akapitao a magareta anaona kuti sindiye mfumu ya Israyeli, anabwerera osampitikitsa.
34 Ndipo munthu anakoka uta wace ciponyeponye, nalasa mfumu ya Israyeli pakati pa maluma a maraya acitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa gareta wace, Tembenuza dzanja lako, nundicotse kunkhondo, popeza ndalasidwa.
35 Ndipo nkhondo inakula tsiku lomwelo, ndipo mfumu inagwirizidwa m'gareta mwace kupenyana ndi Aaramu, natsirizika madzulo; ndipo mwazi unaturuka m'bala pa phaka la gareta.
36 Ndipo mfuu unafikira khamu lonse la nkhondo polowa dzuwa, ndi kuti, Yense kumudzi kwao, ndi yense ku dziko la kwao.
37 Ndipo inafa mfumu, naifikitsa ku Samaria, naika mfumu m'Samaria.
38 Ndipo potsuka garetayo pa thawale la ku Samaria agaru ananyambita mwazi wace, pala pamasamba akazi adama, monga mwa mau a Yehova amene ananenawo.
39 Tsono macitidwe ena a Ahabu, ndi zonse adazicita, ndi nyumba ya minyanga adaimanga, ndi midzi yonse adaimanga, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?
40 Ndipo Ahabu anagona ndi makolo ace; ndi Ahaziya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.
41 Koma Yehosafati mwana wa Asa anayamba kukhala mfumu ya Yuda caka cacinai ca Ahabu mfumu ya Israyeli.
42 Yehosafati anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu, pamene analowa ufumu, nakhala nifumu zaka makumi awiri mphambu zisanu m'Yerusalemu. Ndi dzina la amace linali Azuba mwana wa Sili.
43 Ndipo anayenda m'njira yonse ya atate wace Asa, osapambukamo; nacita coyenera pamaso pa Yehova, koma misanje sanaicotsa; anthu anapherabe nsembe, nafukiza zonunkhira pamsanje.
44 Ndipo Yehosafati anacitana mtendere ndi mfumu ya Israyeli.
45 Tsono maciddwe ena a Yehosafati, ndi mphamvu anaionetsayo, ndi umo anathira nkhondo, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
46 Ndipo anacotsa m'dziko anyamata onyansa aja adatsalira masiku a atate wace Asa.
47 Ndipo m'Edomu munalibe mfumu, koma kazembe wa mfumu.
48 Yehosafati anamanga zombo za ku Tarsisi kukatenga golidi ku Ofiri; koma sizinamuka, popeza zinaphwanyika pa Ezioni Geberi.
49 Pamenepo Ahaziyamwana wa Ahabu ananena ndi Yehosafati, Anyamata anga amuke pamodzi ndi anyamata anu m'zombo. Koma Yehosafati anakana.
50 Ndipo Yehosafati anagona ndi makolo ace, naikidwa ndi makolo ace m'mudzi wa Davide kholo lace; ndipo Yoramu mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.
51 Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israyeli pa Samaria m'caka cakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri ca Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israyeli zaka ziwiri.
52 Nacita coipa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya atate wace, ndi ya amace, ndi ya Yerobiamu mwana wa Nebati, amene adacimwitsa Israyeli.
53 Natumikira Baala, namweramira, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli, monga umo anacitira atate wace.