2 Mafumu 1 BL92

Eliya ndi nthenda ya Ahaziya

1 NDIPO atamwalira Ahabu, Moabu anapandukana ndi Israyeli.

2 Ndipo Ahaziya anagwa kubzola ku made wa cipinda cace cosanja cinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni ngati ndidzacira nthenda iyi.

3 Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli, kuti mukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni?

4 Cifukwa cace atero Yehova, Sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Nacoka Eliya.

5 Ndipo mithenga inabwerera kwa iye, nanena nayo, Mwabwerera cifukwa ninji?

6 Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni? Cifukwa cace sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.

7 Ndipo iye ananena nayo, Nanga maonekedwe ace a munthu anakwerayo kukomana nanu, nanena nanu mau awa, ndi otani?

8 Ninena naye, Ndiye munthu wobvala zaubweya, namangira m'cuuno mwace ndi lamba lacikopa. Nati iye, Ndiye Eliya wa ku Tisibe.

9 Pamenepo mfumu inatuma kwa iye asilikari makumi asanu ndi mtsogoleri wao. Iye nakwera kumka kwa Eliya; ndipo taonani, analikukhala pamwamba pa phiri. Ndipo analankhula naye, Munthu wa Mulungu iwe, mfumu ikuti, Tsika.

10 Nayankha Eliya, nanena ndi mtsogoleriyo, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike mota wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo unatsika mota kumwamba, nunyeketsa iye ndi makumi asanu ace.

11 Ndipo anabwereza kutuma kwa iye mtsogoleri wina ndi makumi asanu ace. Ndipo iye anayankha nanena naye, Munthu wa Mulungu iwe, itero mfumu, Tsika msanga.

12 Nayankha Eliya, nanena nao, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike mota wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo mota wa Mulungu unatsika kumwamba nunyeketsa iye ndi makumi asanu ace.

13 Ndipo anabwerezaaso kutuma mtsogolen wacitatu ndi makumi asanu ace. Nakwera mtsogoleri wacitatuyo, nadzagwada ndi maondo ace pamaso pa Eliya, nampembedza, nanena naye, Munthu wa Mulungu inu, ndikupemphani, moyo wanga ndi moyo wa anyamata anu makumi asanu awa akhale a mtengo wace pamaso panu.

14 Taonani, watsika mota wakumwamba, nunyeketsa atsogoleri awiri oyamba aja pamodzi ndi makumi asanu ao; koma tsopano moyo wanga ukhale wa mtengo wace pamaso panu.

15 Pamenepo mthenga wa Yehova anati kwa Eliya, Tsika naye, usamuopa. Nanyamuka iye, natsikira naye kwa mfumu.

16 Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli kufunsira mau ace? Cifukwa cace sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.

17 Motero anafa monga mwa mau a Yehova adanena Eliyawo. Ndipo Yehoramu analowa ufumu m'malo mwace caka caciwiri ca Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, pakuti analibe mwana wamwamuna.

18 Macitidwe ace ena tsono adawacita Ahaziya, kodi salembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25