2 Mafumu 10 BL92

Yehu aononga mbumba ya Ahabu

1 Ndipo Ahabu anali nao ana amuna makumi asanu ndi awiri m'Samariya. Nalemba akalata Yehu, natumiza ku Samariya kwa akulu a Yezreeli, ndiwo akulu akulu, ndi iwo adalera ana a Ahabu, ndi kuti,

2 Tsono akakufikani inu kalata uyu, popeza muli nao ana a mbuye wanu; muli naonso magareta ndi akavalo, ndi mudzi walinga, ndi zida,

3 musankhe wokoma ndi woyenerayo wa ana a mbuye wanu, ndi kumuika pa mpando wacifumu wa atate wace; ndipo muiponyere nkhondo nyumba ya mbuye wanu.

4 Koma anaopa kwambiri, nati, Taonani, mafumu awiri sanaima pamaso pace, nanga ife tidzaima bwanji?

5 Ndipo iye wakuyang'anira nyumba, ndi iye wakuyang'anira mudzi, ndi akulu akulu, ndi iwo akulera anawo, anatumiza kwa Yehu, ndi kuti, Ife ndife akapolo anu ndi zonse mutiuza tidzacita; sitidzalonga munthu yense mfumu; cokomera pamaso panu citani.

6 Nawalembera kalata kaciwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu va amunawo ana a mbuyewanu, ndi kundidzera ku Yezreeli mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m'mudzi, amene anawalera.

7 Ndipo kunali, powafika kalatayo, anatenga ana a mfumu, nawapha amuna makumi asanu ndi awiri, naika mitu yao m'mitanga, naitumiza kwa iye ku Yezreeli.

8 Nudza mthenga, numfotokozera, kuti, Abwera nayo mitu va ana a mfumu. Nati iye, Mulunjike miulu iwiri polowera pa cipata kufikira m'mawa.

9 Ndipo kunali m'ma wa, iye anaturuka, naima, nati kwa anthu onse, Muli olungama inu, taonani, ndinapandukira mbuye wanga ndi kumupha; koma awa onse anawakantha ndani?

10 Dziwani tsono, kuti sikadzagwa pansi kanthu ka mau a Yehova, amene Yehova ananena za nyumba va Ahabu; pakuti Yehova wacita cimene adanena mwa mtumiki wace Eliya.

11 Nawakantha Yehu otsala onse a nyumba ya Ahabu m'Yezreeli, ndi omveka ace onse, ndi odziwana naye, ndi ansembe ace, mpaka sanatsala wa iye ndi mmodzi yense.

12 Pamenepo ananyamuka, nacoka, namuka ku Samariya, Ndipo pokhala ku nyumba yosengera ya abusa panjira,

13 Yehu anakomana nao abale a Ahaziya mfumu ya Yuda, nati, Ndinu ayani? Nati iwo, Ife ndife abale a Ahaziya, tirikutsika kulankhulira ana a mfumu, ndi ana a nyumba yaikuru.

14 Nati iye, Agwireni amoyo. Nawagwira amoyo, nawapha ku dzenje la nyumba yosengera, ndiwo amuna makumi anai mphambu awiri; sanasiya ndi mmodzi yense.

Aphedwa aneneri a Baala

15 Atacoka pamenepo, anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamcingamira; namlankhula, nanena naye, Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga ubvomerezana nao mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lace, namkweretsa pali iye pagareta.

16 Nati iye, Tiye nane, ukaone cangu canga ca kwa Yehova. M'mwemo anamuyendetsa m'gareta wace.

17 Ndipo anafika ku Samariya, nakantha onse otsala a Ahabu m'Samariya, mpaka adamuononga monga mwa mau a Yehova adanenawo kwa Elisa.

18 Ndipo Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi, nanena nao, Ahabu anatumikira Baala pang'ono, koma Yehu adzamtumikira kwambiri.

19 Mundiitanire tsono adze kwa ine aneneri onse a Baala, ompembedza onse, ndi ansembe ace onse, asasowe mmodzi; pakuti ndiri nayo nsembe yaikuru yocitira Baala; ali yense wosapenyekapo sadzakhala ndi moyo. Kama Yehu anacicita monyenga, kuti akaononge otumikira Baala.

20 Nati Yehu, Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala. Naulalikira.

21 Ndipo Yehu anatumiza kwa Aisrayeti onse, nadza otumikira Baala onse, wosatsala ndi mmodzi yense wosafika. Nalowa m'nyumba ya Baala; ndi nyumba ya Baala inadzala pha.

22 Nati kwa iye wosunga nyumba ya zobvala, Turutsira otumikira Baala onse zobvala. Nawaturutsira zobvala.

23 Nalowa Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu m'nyumba ya Baala, nati kwa otumikira Baala, Mufunefune, nimuone asakhale nanu muno otumikira Yehova, koma otumikira Baala okha.

24 Nalowa iwo kupereka nsembe zophera ndi nsembe zopsereza. Koma Yehu adadziikira kubwalo amuna makumi asanu ndi atatu, nati, Munthu akalola wina wa anthuwa ndirikuwaika m'manja mwanu apulumuke, moyo wace kulipa moyo wace.

25 Ndipo kunali, atatsiriza kupereka nsembe yopsereza, Yehu anati kwa otumikira ndi atsogoleri, Lowani, akantheni; asaturuke ndi mmodzi yense. Nawakantha ndi lupanga lakuthwa; ndi otumikira ndi atsogoleri anawataya kubwalo, namuka ku mudzi wa nyumba ya Baala.

26 Naturutsa zoimiritsa zija zinali m'nyumba ya Baala, nazitentha.

27 Nagamula fane la Baala, nagamula nyumba ya Baala, naiyesa dzala mpaka lero lino.

28 Momwemo Yehu anaononga Baala m'Israyeli.

Yehu apembedza mafano

29 Koma Yehu sanazileka zoipa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene adacimwitsa nazo Israyeli, ndizo ana a ng'ombe agolidi okhala m'Beteli ndi m'Dani.

30 Ndipo Yehova anati kwa Yehu, Popeza wacita bwino, pocita coongoka pamaso panga, ndi kucitira nyumba ya Ahabu monga mwa zonse zinali m'mtima mwanga, ana ako a ku mbadwo wacinai adzakhala pa mpando wacifumu wa Israyeli.

31 Koma Yehu sanasamalira kuyenda m'cilamulo ca Yehova Mulungu wa Israyeli ndi mtima wace wonse; sanaleka zoipa za Yerobiamu, zimene anacimwitsa nazo Israyeli.

32 Masiku ao Yehova anayamba kusadza Israyeli; ndipo Hazaeli anawakantha m'malire onse a Israyeli,

33 kuyambira ku Yordano kum'mawa, dziko lonse la Gileadi, la Agadi, ndi la Arubeni, ndi Amanase, kuyambira ku Aroeri, ndiwo kumtsinje Arinoni, ndilo Gileadi ndi Basana.

34 Ndipo macitidwe ena a Yehu, ndi zonse anazicita, ndi mphamvu yace yonse, sizinalembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafwnu a Israyeli

35 Nagona Yehu ndi makolo ace, namuika m'Samariya. Ndi Yehoahazi mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

36 Ndipo masiku ace akukhala Yehu mfumu ya Israyeli m'Samariya ndiwo zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25