2 Mafumu 4 BL92

Elisa afurukitsa mafuta a mkazi wamasiye

1 Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anapfuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ace.

2 Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikucitire ciani? undiuze m'nyumba mwako muli ciani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta.

3 Pamenepo anati, Kabwereke zotengera kwina kwa anansi ako onse, zotengera zopanda kanthu, zisakhale pang'ono.

4 Nulowe, uudzitsekere wekha ndi ana ako amuna ndi kutsanulira m'zotengera zonsezi, nuike padera zodzalazo.

5 Pamenepo anamcokera, nadzitsekera yekha ndi ana ace amuna; iwo namtengera zotengerazo, iye namatsanulira.

6 Ndipo kunali, zitadzala zotengera, anati kwa mwana wace, Nditengere cotengera cina, Nanena naye, Palibe cotengera cina. Ndipo mafuta analeka.

7 Pamenepo anadza, namfotokozera munthu wa Mulungu. Nati iye, Kagulitse mafuta, ukabwezere mangawa ako, ndi zotsalapo zikusunge iwe ndi ana ako.

Mkazi wa ku Sunemu ndi mwana wace

8 Ndipo linafika tsiku lakuti Elisa anapitirira kumka ku Sunemu, kumeneko kunali mkazi womveka; ameneyo anamuumiriza adye mkate. Potero pomapitirako iyeyu, adafowapa, mbukirako kukadya mkate.

9 Ndipo mkaziyo anati kwa mwamuna wace, Taona, tsopano ndidziwa kuti munthu uyu wakupitira pathu pano cipitire ndiye munthu woyera wa Mulungu.

10 Timmangire kacipinda kosanja, timuikirenso komweko kama, ndi gome, ndi mpando, ndi coikapo nyali; ndipo kudzatero kuti akatidzera alowe m'mwemo.

11 Ndipo linadza tsiku lakuti anafikako, nalowa m'cipinda cosanja, nagona komweko.

12 Nati kwa Gehazi mnyamata wace, Itana Msunemu uja. Namuitana, naima mkaziyo pamaso pace.

13 Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikucitire iwe ciani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga.

14 Pamenepo anati, Nanga timcitire iye ciani? Nati Gehazi, Zedi alibe mwana, ndi mwamuna wace wakalamba.

15 Nati, Kamuitane. Namuitana, naima pakhomo mkaziyo.

16 Ndipo anati, Nyengo yino caka cikudzaci udzafukata mwana wamwamuna. Koma anati, lai, mbuyanga, munthu wa Mulungu, musanamiza mdzakazi wanu.

17 Ndipo mkaziyo anaima, naona mwana wamwamuna nyengo yomweyo caka cimene cija Elisa adanena naye.

18 Ndipo atakula mwanayo, linadza tsiku lakuti anaturuka kumka kwa atate wace, ali kwa omweta tirigu.

19 Natikwa atate wace, Mutu wanga, mutu wanga! Pamenepo anati kwa mnyamata, Umnyamule umuke naye kwa amace.

20 Namnyamula, napita naye kwa amace. Ndipo anakhala pa maondo ace kufikira usana, namwalira.

21 Ndipo anakwera, namgoneka pa kama wa munthu wa Mulungu, naturuka, namtsekera.

22 Naitana mwamuna wace, nati, Nditumizire mmodzi wa anyamata ndi buru mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu uja wa Mulungu, ndi kubweranso.

23 Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero cifukwa ninji? ngati mwezi wakhala, kapena: mpa sabata? Koma anati, Kuli bwino.

24 Pamenepo anamangirira buru mbereko, nati kwa mnyamata wace, Kusa, tiye; usandilezetsa kuyendaku, ndikapanda kukuuza.

25 Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu ku phiri la Karimeli. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wace, Tapenya, suyo Msunemu uja;

26 uthamange tsopano kukomana naye, nunene naye, Muli bwino kodi? mwamuna wanu ali bwino? mwanayo ali bwino? Ndipo anati, Ali bwino.

27 Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wace ulikumwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ici.

28 Ndipo mkaziyo anati, Ngati ndinapempha mwana kwa mbuyanga? Kodi sindinati, Musandinyenga?

29 Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m'cuuno, nutenge ndodo yanga m'dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usamlankhule; akakulankhula wina usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.

30 Koma mace wa mwana anati, Pali Yehova, pali inunso, ngati nkukusiyani. Ndipo ananyamuka, namtsata.

31 Nawatsogolera Gehazi, naika ndodo pankhope pa mwanayo; koma mwanayo analibe mau, kapena kusamalira. Motero anabwerera kukomana naye, namuuza kuti, Sanauke mwanayo.

32 Ndipo pamene Elisa analowa m'nyumba, taonani, mwanayo ngwakufa, adamgoneka pakama pace.

33 Nalowa Elisa, nadzitsekera awiriwa, napemphera kwa Yehova.

34 Nakwera, nagona pa mwanayo ndi kulinganiza pakamwa pace ndi pakamwa pace, maso ace ndi maso ace, zikhato zace ndi zikhato zace, nadzitambasula pa iye, ndi mnofu wa mwana unafunda.

35 Pamenepo anabwera nayenda m'nyumba, cakuno kamodzi, cauko kamodzi; nakwera, nadzitambasuliranso pa iye; ndi mwana anayetsemula kasanu ndi kawiri, natsegula mwanayo maso ace.

36 Pamenepo anaitana Gehazi, nati, Kaitane Msunemu uja, Namuitana. Ndipo atalowa kuli iye, anati, Nyamula mwana wako.

37 Iye nalowa, nagwa pa mapazi ace, nadziweramitsa pansi; nanyamula mwana wace, naturuka.

Muli imfa m'nkhalimo

38 Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m'dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pace; ndipo anati kwa mnyamata wace, Ika nkhali yaikuruyo, uphikire ana a aneneri.

39 Naturuka wina kukachera ndiwo kuthengo, napeza conga ngati mpesa, nacherapo zipuzi kudzaza m'pfunga mwace, nadza, nazicekera-cekera m'nkhali ya cakudya, popeza sanazidziwa.

40 Pamenepo anagawira anthu kuti adye. Koma kunali; pakudya cakudyaco, anapfuula nati, Munthu wa Mulungu, muli imfa m'nkhalimo. Ndipo sanatha kudyako.

41 Pamenepo anati, Bwera naoni ufa. Nathira m'nkhalimo; nati, Gawirani anthu kuti adye. Ndipo m'nkhalimo munalibe cowawa.

Mikate makumi awiri ikwanira anthu ambiri

42 Ndipo anadza munthu kucokera ku Baala Salisa, nabwera nayo mikate ya zipatso zoyamba kwa munthu wa Mulungu, mikate ya barele makumi awiri, ndi ngala zaziwisi za tirigu zosaomba. Ndipo anati, Uwapatse anthu kuti adye.

43 Koma mnyamata wace anati, Ciani? ndigawire amuna zana ici kodi? Koma anati, Uwapatse anthu kuti adye; pakuti atero Yehova, Adzadya nadzasivako.

44 Potero anawagawira, nadya, nasiyapo, monga mwa mau a Yehova.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25