1 Ndipo ana a aneneri anati kwa Elisa, Taonani tsono, pamalo tikhalapo ife pamaso panu paticepera
2 Mutilole tipite ku Yordano, tikatengeko, ali yense mtengo, tidzimangire malo komweko, tikhalepo, Nati, Mukani.
3 Ndipo wina anati, Mulole mupite nafe anyamata anu. Nati, Ndidzamuka.
4 Namuka nao, nafika ku Yordano, iwo natema mitengo.
5 Ndipo wina analinkudula mtengo nkhwangwa inagwa m'madzi; ndipo anapfuula, nati, Kalanga ine mbuyanga! popeza ojobwereka.
6 Nati munthu wa Mulungu, Yagwera pati? Namuonetsapo yagwera. Pamenepo anadula kamtengo, nakaponya pomwepo, nayandamitsa nkhwangwayo.
7 Nati, Katole. Natambasula dzanja lace, naitenga.
8 Ndipo mfumu ya Aramu inalinkucita nkhondo ndi Israyeli, nipangana ndi anyamata ace, kuti, Misasa yanga idzakhala pakuti pakuti.
9 Ndipo munthu wa Mulunguyo anatuma mau kwa mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Mucenjere musapite pakuti, popeza Aaramu alikutsikira uko.
10 Pamenepo mfumu ya Israyeli inatumiza kumene munthu wa Mulungu anamuuzako ndi kumcenjeza; nadzisunga osapitako, kawiri kawiri.
11 Koma mtima wa mfumu ya Aramu unabvutika kwambiri pa icico, naitana anyamata ace, nanena nao, Kodi simudzandiuza wina wa ife wobvomerezana ndi mfumu ya Israyeli ndani?
12 Nati mmodzi wa anyamata ace, lai, mbuye wanga mfumu; koma Elisa, mneneriyo ali ku Israyeli, ndiye amafotokozera mfumu ya Israyeli mau muwanena m'kati mwace mwa cipinda canu cogonamo.
13 Nati iye, Kamuoneni komwe ali; ndikatume munthu kumtenga. Ndipo anamuuza kuti, Ali ku Dotana.
14 Pamenepo anatumizako akavalo ndi magareta ndi khamu lalikuru, nafikako usiku, nauzinga mudziwo.
15 Ndipo atalawirira mamawa mnyamata wa munthu wa Mulungu, naturuka, taonani, khamu la nkhondo linazinga mudzi ndi akavalo ndi magareta. Ndi mnyamata wace ananena naye, Kalanga ine, mbuye wanga! ticitenji?
16 Nati iye, Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife acuruka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.
17 Ndipo Elisa anapemphera, nati, Yehova, mumtsegulire maso ace kuti aone. Pamenepo Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magareta amoto akumzinga Elisa.
18 Ndipo atatsikira pali iye, Elisa anapemphera kwa Yehova, nati, Mukanthe mtundu uwu ucite khungu. Ndipo iye anawakantha, nawacititsa khungu, monga mwa mau a Elisa.
19 Ndipo Elisa ananena nao, Ngati njira ndi iyi? ngati mudzi ndi uwu? munditsate ine, ndidzakufikitsani kwa munthu mumfunayo; nawatsogolera ku Samariya.
20 Ndipo kunali, pakufika ku Samariya, Elisa anati, Yehova, muwakanganulire awa maso kuti aone. Nawakanganulira Yehova maso ao, naona iwo, ndipo tapenyani, ali pakati pa Samariya.
21 Niti mfumu ya Israyeli kwa Elisa pakuwaona, Atate wanga ndiwakanthe kodi, ndiwakanthe?
22 Nati, Musawakanthe; kodi mumakantha omwe mwawagwira ndi lupanga ndi uta wanu? apatseni mkate ndi madzi adye namwe, namuke kwa mbuye wao.
23 Ndipo anwakonzera cakudya cambiri, nadya namwa iwo; nawauza amuke; namuka kwa mbuye wao. Ndipo magulu a Aramu sanadzanso ku dziko la Israyeli.
24 Ndipo zitatha izi, Benihadadi mfumu ya Aramu anamemeza khamu lace lonse, nakwera, namangira misasa Samariya.
25 Koma m'Samariya munali njala yaikuru; ndipo taonani, anaumangira misasa mpaka mutu wa buru unagulidwa ndalama zasiliva makumi asanu ndi atatu; ndi limodzi la magawo anai la muyeso wa zitosi za nkhunda linagulidwa ndi ndalama zasiliva zisanu.
26 Ndipo popita mfumu ya Israyeli alikuyenda palinga, mkazi anampfuulira, nati, Ndithandizeni, mbuye wanga mfumu.
27 Nati iye, Akapanda kukuthandiza Yehova, ndikaona kuti kokuthandiza ine? kudwale kodi, kapena popondera mphesa
28 Nanena naye mfumu, Ufunanji? Nati iye, Mnzanga uyu ananena ndi ine, Tenga mwana wako timudye lero, ndi mwana wanga timudye mawa.
29 Ndipo tinaphika mwana wanga ndi kumudya, ndi mawa wace ndinanena naye, Tenga mwana wako, timudye; koma wambisa mwana wace.
30 Ndipo pakumva mfumu mau a mkaziyo, anang'amba zobvala zace alinkupita nayenda palinga, anthu napenya; ndipo taonani, pali ciguduli m'kati pa thupi lace.
31 Nati iye, Andilange Mulungu naonjezeko, ngati mutu wa Elisa mwana wa Safati uti ukhale pa iye lero lino.
32 Koma Elisa anakhala pansi m'nyumba mwace, ndi akulu anakhala pansi pamodzi naye; ndipo mfumu inatuma munthu amtsogolere, koma asanafike kwa Elisa mthengayo, anati kwa akulu, Mwapenya kodi m'mene mwana uyu wambanda watumiza munthu kucotsa mutu wanga? taonani, pakufika mthengayo mutseke pakhomo, mumkankhe ndi citseko. Kodi mapazi a mbuye wace samveka dididi pambuyo pace?
33 Akali cilankhulire nao, tapenyani, wamtsikira mthengayo; ndi mfumu inati, Taonani, coipa ici cicokera kwa Yehova; ndilindiranjinso Yehova?