1 Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israyeli m'Samariya m'caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.
2 Nacita coipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wace ndi amace; pakuti anacotsa coimiritsa ca Baala adacipanga atate wace.
3 Koma anakangamira zoipa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene anacimwitsa nazo Israyeli, osalekana nazo.
4 Ndipo Mesa mfumu ya Moabu anali mwini nkhosa, akapereka kwa mfumu ya Israyeli ubweya wa ana a nkhosa zikwi zana limodzi, ndi wa mphongo zikwi zana limodzi.
5 Kama kunacitika, atafa Ahabu mfumu ya Moabu anapandukana ndi mfumu ya Israyeli.
6 Ndipo mfumu Yehoramu anaturuka m'Samariya nthawi yomweyo, namemeza Aisrayeli onse.
7 Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Moabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Moabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako.
8 Ndipo anati, Tikwerere njira yiti? Nati iye, Njira ya ku cipululu ca Edomu.
9 Namuka mfu mu ya Israyeli, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata.
10 Ndipo mfumu ya Israyeli inati, Kalanga ife! pakuti Yehova waitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Moabu.
11 Koma Yehosafati anati, Palibe pano mneneri wa Yehova kodi, kuti tifunsire Yehova mwa iye? Ndipo wina wa anyamata a mfumu ya Israyeli anayankha, nati, Elisa mwana wa Safati ali pano, ndiye uja anathira madzi m'manja a Eliya.
12 Nati Yehosafati, Mau a Yehova ali ndi iyeyo, Pamenepo mfumu ya Israyeli, ndi Yehosafati, ndi mfumu ya Edomu, anatsikira kuli iye.
13 Ndipo Elisa anati kwamfumuya Israyeli, Ndiri ndi ciani ndi inu? mukani kwa aneneri a atate wanu, ndi kwa aneneri a amai wanu. Koma mfumu ya Israyeli inanena naye, Iai, pakuti Yehova anaitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Moabu.
14 Ndipo Elisa anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndiima pamaso pace, ndikadapanda kusamalira nkhope ya Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikadakuyang'anitsani, kapena kukuonani.
15 Koma tsopano, nditengereni wanthetemya. Ndipo kunali, waothetemyayo ali ciyimbire, dzanja la Yehova linamgwera.
16 Ndipo anati, Atero Yehova, Kumbani m'cigwa muno mukhale maenje okha okha.
17 Pakuti atero Yehova, Simudzaona mphepo, kapena kuona mvula, koma cigwaco cidzadzala ndi madzi; ndipo mudzamwa inu, ndi ng'ombe zanu, ndi zoweta zanu.
18 Ndipo ici cidzapepuka pamaso pa Yehova; adzaperekanso Amoabu m'dzanja lanu.
19 Ndipo mudzakantha midzi yonse ya matioga, ndi midzi yonse yosankhika, ndi kulikha mitengo yonse yabwino, ndi kufotsera zitsime zonse zamadzi, ndi kuipitsa pa nthaka ponse pabwino ndi miyala.
20 Ndipo kunacitika m'mawa, pomapereka nsembe yaufa, taonani, anafika madzi odzera ku Edomu; ndipo dziko linadzala ndi madzi.
21 Atamva tsono Amoabu onse kuti adakwera mafumu aja kuthirana nao nkhondo, anamemeza onse akumanga lamba m'cuuno ndi okulapo, naima iwo m'malire.
22 Ndipo pamene anauka mamawa dzuwa linawala pamadzipo, naona Amoabu madzi ali pandunji pao ali psyu ngati mwazi;
23 nati, Uja ndi mwazi, atha kuonongana mafumu aja, anakanthana wina ndi mnzace; ndipo tsopano, tiyeni Amoabu inu, tikafunkhe.
24 Ndipo pamene anafika ku misasa ya Israyeli, Aisrayeli ananyamuka, nakantha Amoabu, nathawa iwo pamaso pao; ndipo analowa m'dziko ndi kukantha Amoabu.
25 Napasula midzi, naponya yense mwala wace panthaka ponse pabwino, naidzaza, nafotsera zitsime zonse zamadzi, nagwetsa mitengo yonse yabwino, kufikira anasiya miyala yace m'Kirihasereti mokha; koma oponya miyala anauzinga, naukantha.
26 Ndipo ataona mfumu ya Moabu kuti nkhondo idamlaka, anapita nao anthu mazana asanu ndi awiri akusolola lupanga, kupyola kufikira kwa mfumu ya Edomu, koma sanakhoza.
27 Pamenepo anagwira mwana wace wamwamuna woyamba amene akadakhala mfumu m'malo mwace, nampereka nsembe yopsereza palinga. Ndipo anakwiyira Israyeli kwambiri; potero anamcokera, nabwerera ku dziko lao.