2 Mafumu 19 BL92

Nkhawa ya Hezekiya ndi pemphero lace

1 Ndipo kunali, atamva Hezekiya, anang'amba zobvala zace, napfundira ciguduli, nalowa m'nyumba ya Yehova.

2 Natuma Eliyakimu woyang'anira nyumbayo, ndi Sebina mlembi, ndi akuru a ansembe opfundira ciguduli, kwa Yesaya mneneri mwana wa Amozi.

3 Nati kwa iye, Atero Hezekiya, Lero line ndilo tsiku la cisautso, ndi la kudzudzula, ndi la kunyoza; pakuti ana anafikira kubadwa, koma palibe mphamvu yakubala.

4 Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asuri mbuye wace, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga cifukwa ca mau adawamva Yehova Mulungu wanu; cifukwa cace uwakwezere otsalawo pemphero.

5 Ndipo anyamata a mfumu Hezekiya anafika kwa Yesaya.

6 Nanena nao Yesaya, Muzitero kwa mbuye wanu, Atero Yehova, Musamaopa mau mudawamva, amene anyamata a mfumu ya Asuri anandicitira nao mwano.

7 Taonani, ndidzalonga mwa iye mzimu wakuti adzamva mbiri, nadzabwerera kumka ku dziko lace, ndipo ndidzamgwetsa ndi lupanga m'dziko lace.

8 Nabwerera kazembeyo, napeza mfumu ya Asuri alikuthira nkhondo pa Libina, popeza anamva kuti adacoka ku Lakisi.

9 Ndipo anamva za Tirihaka mfumu ya Kusi, akuti, Taonani, waturuka kuthirana nawe nkhondo. Pamenepo anatumizanso mithenga kwa Hezekiya, ndi kuti,

10 Muzitero naye Hezekiya mfumu ya Yuda, kuti, Asakunyenge Mulungu wako amene umkhulupirira, ndi kuti, Yerusalemu sudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya Asuri.

11 Taona, udamva ico mafumu a Asuri anacitira maiko onse, ndi kuwaononga konse; ndipo uti upulumuke ndiwe kodi?

12 Kodi milunguyaamitundu inawalanditsa amene makolo anga anawaononga, ndiwo Gozani, ndi Hara Rezefi, ndi ana a Edeni okhala m'Telasara?

13 Iri kuti mfumu ya Hamati, ndi mfumu ya Aripadi, ndi mfumu ya mudzi wa Sefaravaimu, wa Hena, ndi Iva?

14 Ndipo Hezekiya analandira kalatayo ku dzanja la mithenga, namwerenga, nakwera Hezekiya kumka ku nyumba ya Yehova, namfunyulula pamaso pa Yehova.

15 Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati, Yehova Mulungu wa Israyeli wakukhala pakati pa akerubi, Inu ndinu Mulungu mwini wace, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

16 Cherani khutu lanu, Yehova, nimumve; tsegulani maso anu, Yehova, nimupenye; ndipo imvani mau a Sanakeribu, amene anatumiza kutonza nao Mulungu wamoyo.

17 Zoona, Yehova, mafumu a Asuri anapasula amitundu ndi maiko ao,

18 naponya milungu yao kumoto; popeza sindiyo milungu koma yopanga anthu ndi manja ao, mtengo ndi mwala; cifukwa cace anaiononga.

19 Ndipo tsono, Yehova Mulungu wathu, mutipulumutse m'dzanja lace, kuti adziwe maufumu onse a dziko lapansi kuti Inu ndinu Yehova Mulungu, Inu nokha nokha.

Yesaya amtonthoza mtima Hezekiya

20 Pamenepo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza kwa Hezekiya, ndi, kuti, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Condipempha iwe pa Sanakeribu mfumu ya Asuri ndacimva.

21 Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi wa Ziyoni akunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako.

22 Ndiye yani wamtonza ndi kumcitira mwano? ndiye yani wamkwezera mau ndi kumgadamira maso ako m'mwamba? Ndiye Woyerayo wa Israyeli.

23 Watonza Yehova mwa mithenga yako, nuti, Ndi magareta anga aunyinji ndakwera pa misanje ya mapiri ku mbali zace za Lebano, ndipo ndidzagwetsa mikungudza yace yaitali, ndi mitengo yace yosankhika yar mlombwa, ndidzalowanso m'ngaka mwace mweni mweni, ku nkhalango zace za madimba.

24 Ndakapa, ndamwa madzi acilendo, ndi ku mapazi anga ndidzaphwetsa mitsinje yonse ya Aigupto,

25 Sunamva kodi kuti Ine ndinacicita kale lomwe, ndi kucipanga masiku akalekale? tsopano ndacifikitsa kuli iwe, uzikhala wakupasula imidzi yamalinga ikhale miunda ya mabwinja.

26 Cifukwa cace okhalamo ao anali ofok a manja, anaopsedwa, nacita manyazi, ananga udzu wa kuthengo, ndi msipu wauwisi, ndi udzu wa patsindwi, ndi tirigu wopserera asanakule.

27 Koma ndidziwa kukhala pansi kwako, ndi kuturuka kwako, ndi kulowa kwako, ndi kundizazira kwako.

28 Cifukwa ca kundizazira kwako, ndi popeza kudzikuza kwako kwandifikira m'makutu mwanga, ndidzakukowa ndi ngowe yanga m'mphuno mwako, ndi cam'kamwa canga m'milomo mwako; ndipo ndidzakubwezera pa njira unadzerayi.

29 Ndi ici ndi cizindikilo cako: caka cino mudzadya za mphulumukwa, ndi caka ca mawa za mankhokwe, ndi caka camkuca muzibzala ndi kukolola, muzioka minda yampesa ndi kudya zipatso zace.

30 Ndipo opulumuka a nyumba ya Yuda otsalawo adzaphukanso mizu, ndi kupatsa zipatso pamwamba.

31 Pakuti ku Yerusalemu kudzaturuka otsala, ndi akupulumukawo ku phiri la Ziyoni; cangu ca Yehova cidzacita ici.

32 Cifukwa cace atero Yehova za mfumu ya Asuri, iye sadzalowa m'mudzi muno, kapena kuponyamo mubvi, kapena kufikako ndi cikopa, kapena kuundira mtumbira.

33 Adzabwerera njira yomweyo anadzera, ndipo sadzalowa m'mudzi muno, ati Yehova.

34 Pakuti ndidzacinjiriza mudzi uno kuupulumutsa, cifukwa ca Ine mwini, ndi cifukwa ca Davide mtumiki wanga.

Mthenga wa Yehova awapha Aasurio

35 Ndipo kunali, usiku womwewo mthenga wa Yehova anaturuka, nakantha m'misasa ya Aasuri zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu, ndipo pouka anthu mamawa, taonani, onsewo ndi mitembo.

36 Nacoka Sanakeribu mfumu ya Asuri, namuka, nabwerera, nakhala ku Nineve.

37 Ndipokunali popembedza iye m'nyumba ya Nisiroki mulungu wace, Adrameleki ndi Sarezere anamkantha ndi lupanga; napulumukira ku dziko la Ararati. Ndipo Esarihadoni mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25