1 Masiku ace Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anakwerako, Yoyakimu nagwira mwendo wace zaka zitatu; pamenepo anatembenuka nampandukira.
2 Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Akasidi, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amoabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova: adawanena ndi dzanja la atumiki ace aneneriwo.
3 Zedi ici cinadzera Yuda mwa lamulo la Yehova, kuwacotsa pamaso pace, cifukwa ca zolakwa za Manase, monga mwa zonse anazicita;
4 ndiponso cifukwa ca mwazi wosacimwa adaukhetsa; popeza anadzaza Yerusalemu ndi mwazi wosacimwa; ndipo Yehova sanafuna kukhululukira.
5 Macitidwe ena tsono a Yoyakimu, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
6 Nagona Yoyakimu ndi makolo ace, ndipo Yoyakini mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.
7 Koma mfumu ya Aigupto sinabwerezanso kuturuka m'dziko lace, pakuti mfumu ya Babulo idalanda kuyambira ku mtsinje wa Aigupto kufikira ku mtsinje Firate, ndilo lonse anali nalo mfumu ya Aigupto.
8 Yoyakini anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu polowa iye ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu; ndi dzina la mace ndiye Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.
9 Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga umo monse adacita atate wace.
10 Nthawi ija anyamata a Nebukadinezara mfumu ya Babulo anakwerera Yerusalemu, naumangira mudziwo misasa.
11 Nafika Nebukadinezara mfumu ya Babulo kumudzi, ataumangira misasa anyamata ace,
12 ndipo Yoyakini mfumu ya Yuda anaturukira kwa mfumu ya Babulo, iye ndi mace, ndi anyamata ace, ndi akalonga ace, ndi adindo ace; mfumu ya Babulo nimtenga caka cacisanu ndi citatu ca ufumu wace.
13 Naturutsa kucotsa komweko cuma conse ca nyumba ya Yehova, ndi cuma ca nyumba ya mfumu, naduladula zipangizo zonse zagolidi adazipanga Solomo mfumu ya Israyeli m'Kacisi wa Yehova, monga Yehova adanena.
14 Nacoka nao a m'Yerusalemu onse, ndi akalonga onse, ndi ngwazi zonse, ndiwo andende zikwi khumi, ndi amisiri onse, ndi osula onse; sanatsala ndi mmodzi yense, koma anthu osauka okha okha a m'dziko.
15 Nacoka naye Yoyakini kumka naye ku Babulo, ndi mace wa mfumu, ndi akazi a mfumu, ndi adindo ace, ndi omveka a m'dziko; anacoka nao andende ku Yerusalemu kumka nao ku Babulo.
16 Ndi anthu amphamvu onse, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi amisiri, ndi osula cikwi cimodzi, onsewo acamuna oyenera nkhondo, omwewo mfumu ya Babulo anadza nao andende ku Babulo.
17 Ndipo mfumu ya Babulo analonga Mataniya mbale wa atate wace akhale mfumu m'malo mwace, nasanduliza dzina lace likhale Zedekiya.
18 Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi ndi cimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
19 Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adacita Yoyakimu.
20 Pakuti mwa mkwiyo wa Yehova zonse zidacitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda, mpaka adawataya pamaso pace; ndipo Zedekiya anapandukira mfumu ya Babulo.