2 Mafumu 9 BL92

Yehu adzozedwa mfumu ya Israyeli

1 Ndipo Elisa mneneriyo anaitana mmodzi wa ana a aneneri, nanena naye, Udzimangire m'cuuno, nutenge nsupa iyi ya mafuta m'dzanja mwako, numuke ku Ramoti Gileadi.

2 Ndipo ukafikako, ukaunguzeko Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimsi, nulowe numnyamukitse pakati pa abale ace, nupite naye ku cipinda cam'katimo.

3 Nutenge nsupa ya mafutayo, nuwatsanulire pamutu pace, nunene, Atero Yehova; Ndakudzoza iwe ukhale mfumu pa Israyeli. Utatero, tsegula pakhomo, nuthawe osacedwa,

4 Pamenepo mnyamatayo, ndiye mneneri, anamuka ku Ramoti Gileadi.

5 Nalowa, ndipo taonani, akazembe a khamu alikukhala pansi; nati iye, Ndiri ndi mau kwa inu, kazembe. Nati Yehu, Kwa yani wa ife tonse? Nati iye, Kwa Inu, kazembe.

6 Nanyamuka, nalowa m'nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pace, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisrayeli.

7 Nudzakantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere cilango ca mwazi wa: atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebeli.

8 Popeza nyumba yonse ya Ahabu idzaonongeka, ndipo ndidzalikhira Ahabu ana amuna onse womangika ndi womasuka m'Israyeli.

9 Ndipo ndidzalinganiza nyumba ya Ahabu ndi nyumba ya Yerobiamu mwana wa Nebati, ndi nyumba ya Basa mwana wa Ahiya.

10 Ndipo agaru adzamudya Yezebeli pa dera la Yezreeli, wopanda wina wakumuika. Pamenepo anatsegula pakhomo, nathawa.

11 Ndipo Yehu anaturukira kwa anyamata a mbuye wace, nanena naye wina, Mtendere kodi? anakudzera cifukwa ninji wamisala uyu? Nanena nao, Mumdziwa munthuyo ndi makambidwe ace.

12 Nati iwo, Kunama uku; utifotokozere tsono. Nati iye, Anati kwa ine cakuti cakuti; ndi kuti, Atero Yehova, Ndakudzoza mfumu pa Israyeli.

13 Nafulumira iwo, nagwira yense copfunda cace, naciyala pokhala iye paciunda, naomba lipenga, nati, Yehu ndiye mfumu.

Yehu awapha Yoramu ndi Ahaziya

14 Motero Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimsi anapandukira Yoramu. Tsono Yoramu atalindira ku Ramoti Gileadi, iye ndi Aisrayeli onse, cifukwa ca Hazaeli mfumu ya Aramu;

15 koma mfumu Yoramu adabwera ku Yezreeh ampoletse mabala ace anamkantha Aaramu, muja adalimbana naye Hazaeli mfumu ya Aramu. Nati Yehu, Ukatero mtima wanu, asapulumuke mmodzi yense kuturuka m'mudzi kukafotokozera m'Yezreeli.

16 Nayenda Yehu m'gareta, namuka ku Yezreeli, popeza Yoramu anagonako; ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anatsikira kukamuona Yoramu.

17 Ndipo mlonda ali ciriri pacilindiro m'Yezreeli, naona gulu la Yehu lirinkudza, nati, Ndiona gulu. Nati Yoramu, Tenga wapakavalo, numtumize akomane nao, nanene, Mtendere kodi?

18 Ndipo anamuka wapakavalo kukomana naye, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga. Ndi mlonda anawafotokozera kuti, Mthenga wawafika, koma wosabwera.

19 Pamenepo anatumiza wina wapakavalo, nawafika, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga.

20 Ndi mlonda anafotokozera, kuti, Wawafika, koma wosabwera; ndipo kuyendetsako kukunga kuyendetsa kwa Yehu mwana wa Nimsi, pakuti ayendetsa moyaruka.

21 Nati Yoramu, Manga. Namanga gareta wace, Ndipo Yoramu mfumu ya Israyeli ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anaturuka yense m'gareta wace, naturuka kukakomana ndi Yehu, nakomana naye pa munda wa Naboti m'Yezreeli.

22 Ndipo kunali, pamene Yoramu anaona Yehu, anari, Mtendere kodi, Yehu? Nati iye, Ngwanji mtendere pokhala cacuruka cigololo ndi nyanga zace za mai wako Yezebeli?

23 Natembenuza Yoramu manja ace, nathawa, nati kwa Ahaziya, Ciwembu, Ahaziya.

24 Nafa nao Yehu uta wace, nalasa Yoramu pacikota, nuturuka mubvi pa mtima wace, naonyezeka iye m'gareta wace.

25 Nati Yehu kwa Bidikara kazembe wace, Mnyamule, numponye m'munda wa Naboti wa ku Yezreeli; pakuti kumbukila m'mene ine ndi iwe tinali pa akavalo athu pamodzi kutsata Ahabu atate wace, Yehova anamsenzetsa katundu uyu.

26 Ndapenyadi dzulo mwazi wa Naboti ndi mwazi wa ana ace, ati Yehova; ndipo ndikubwezera pamunda pano, ati Yehova, Mtengeni tsono, mumponye pamundapo, monga mwa mau a Yehova.

27 Koma pociona ici Ahaziya mfumu ya Yuda anathawa njira ya ku khumbi la m'munda. Namtsata Yehu, nati, Mumkanthe uyonso pagareta; namkantha pa cikweza ca Guru ciri pafupi pa Yibleamu. Nathawira iye ku Megido, namwalira komweko.

28 Ndipo anyamata ace anamnyamulira pagareta kumka naye ku Yerusalemu, namuika ku manda ace pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide.

29 Ndipo pa caka cakhumi ndi cimodzi ca Yoramu mwana wa Ahabu, Ahaziya analowa ufumu pa Yuda.

Imfa ya Yezebeli

30 Ndipo pofika Yehu ku Yezreeli, Yezebeli anamva, nadzikometsera m'maso, naluka tsitsi lace, nasuzumira pazenera.

31 Ndipo polowa Yehu pacipata, mkaziyo anati, Mtendere kodi Zimri, iwe wakupha mbuyako?

32 Koma anakweza maso ace kuzenera, nati, Ali ndi ine ndani? Ndani? Nampenyererako adindo awiri kapena atatu.

33 Nati iye, Mgwetsereni pansi. Namgwetsera pansi, nuwazikako mwazi wace pakhoma ndi pa akavalo, nampondereza iye pansi.

34 Ndipo atalowa, anadya namwa, nati, Kampenyeni tsono mkazi wotembereredwa uyu, nimumuike; popeza ndiye mwana wa mfumu.

35 Namuka iwo kuti amuike; koma sanapezako kanthu kena koma bade, ndi mapazi, ndi zikhato za manja.

36 Nabwerera iwo, namfotokozera. Nati iye, Ndiwo mau a Yehova ananena wo mwa mtumiki wace Eliya wa ku Tisibe, ndi koti, Pa munda wa Yezreeli agaru adzadya mnofu wa Yezebeli;

37 ndi thupi la Yezebeli lidzakhala ngati ndowe pamunda m'dera la Yezreeli, kuti sadzati, Ndi Yezebeli uyu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25