2 Mafumu 17 BL92

Hoseyamfumu yotsiriza ya Israyeli, Salimanezeri mfumu ya Asuri apasula Samariya, Aisrayeli natengedwa ukapolo

1 Caka cakhumi ndi ziwiri ca Ahazi mfumu ya Yuda Hoseya mwana wa Ela analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka zisanu ndi zinai.

2 Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, koma osati monga mafumu a Israyeli asanakhale iye.

3 Anamkwerera Salimanezere mfumu ya Asuri kumthira nkhondo; ndipo Hoseya anamgonjera, namsonkhera mitulo.

4 Koma mfumu ya Asuri anampeza Hoseya alikucita ciwembu; popeza anatuma mithenga kwa So mfumu ya ku Aigupto, osaperekanso mtulo kwa mfumu ya Asuri, monga akacita caka ndi caka; cifukwa cace mfumu ya Asuri anamtsekera, nammanga m'kaidi.

5 Pamenepo mfumu ya Asuri anakwera m'dziko monse, nakwera ku Samariya, naumangira misasa zaka zitatu.

6 Caka cacisanu ndi cinai ca Hoseya mfumu ya Asuri analanda Samariya, natenga Aisrayeli andende, kumka nao ku Asuri; nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi.

7 Kudatero, popeza ana a Israyeli adacimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwaturutsa m'dziko la Aigupto pansi pa dzanja la Farao mfumu ya Aigupto, ndipo anaopa milungu yina,

8 nayenda m'miyambo ya amitundu amene Yehova adawaingitsa pamaso pa ana a Israyeli, ndi m'miyambo ya mafumu a Israyeli imene iwo anawalangiza.

9 Ndipo ana a Israyeli anacita m'tseri zinthu zosayenera pa Yehova Mulungu wao, nadzimangira misanje m'midzi mwao monse ku nsanja ya olonda ndi ku mudzi walinga komwe.

10 Nadziimikira zoimiritsa ndi zifanizo pa citunda ciri conse cacitali, ndi patsinde pa mtengo uli wonse wogudira;

11 nafukizapo zonunkhira pa misanje youse, monga umo amacitira amitundu amene Yehova adawacotsa pamaso pao, nacita zoipa kuutsa mkwiyo wa Yehova;

12 natumikira mafano amene Yehova anawanena nao, Musacita ici.

13 Ndipo Yehova anacitira umboni Israyeli ndi Yuda mwa dzanja la mneneri ali yense, ndi mlauli ali yense, ndi kuti, Bwererani kuleka nchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa cilamulo conse ndinacilamulira makolo anu, ndi kucitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.

14 Koma sanamvera, naumitsa khosi lao, monga khosi la makolo ao amene sanakhulupirira Yehova Mulungu wao.

15 Ndipo anakaniza malemba ace, ndi cipangano anacicita ndi makolo ao, ndi mboni zace anawacitira umboni nazo, natsata zopanda pace, nasanduka opanda pace, natsata amitundu owazinga, amene Yehova adawalamulira nao, kuti asacite monga iwowa.

16 Ndipo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wao, nadzipangira mafano oyenga, ana a ng'ombe awiri, napanga cifanizo, nagwadira khamu lonse la kuthambo, natumikira Baala.

17 Napititsa ana ao amuna ndi akazi kumoto, naombeza ula, nacita zanyanga, nadzigulitsa kucita coipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wace.

18 Cifukwa cace Yehova anakwiya naye Israyeli kwakukuru, nawacotsa pamaso pace osatsala mmodzi, koma pfuko la Yudalokha.

19 Yudansosanasunga malamulo a Yehova Mulungu wao, koma anayenda m'malemba a Israyeli amene adawaika.

20 Ndipo Yehova anakaniza mbumba yonse ya Israyeli, nawazunza, nawapereka m'dzanja la ofunkha, mpaka anawataya pamaso pace.

21 Pakuti anang'amba Israyeli, kumcotsa ku nyumba ya Davide; ndipo anamlonga mfumu Yerobiamu mwana wa Nebati; Yerobiamu naingitsa Israyeli asatsate Yehova, nawalakwitsa kulakwa kwakukuru.

22 Nayenda ana a Israyeli m'zolakwa zonse za Yerobiamu, zimene anazicita osazileka;

23 mpaka Yehova adacotsa Israyeli pamaso pace, monga adanena mwa dzanja la atumiki ace onse aneneriwo. Momwemo Israyeli anacotsedwa m'dziko lao kumka nao ku Asuri mpaka lero lino.

Mfumu ya Asuri amangitsa alendo m'midzi ya Samariya

24 Ndipo mfumu ya Asuri anabwera nao anthu ocokera ku Babulo, ndi ku Kuta, ndi ku Ava, ndi ku Hamati, ndi ku Safaravaimu, nawakhalitsa m'midzi ya Samariya, m'malo mwa ana a Israyeli; nakhala iwo eni ace a Samariya, nakhala m'midzi mwace.

25 Ndipo kunali, poyamba iwo kukhala komweko, sanaopa Yehova; ndipo Yehova anawatumizira mikango, niwapha ena a iwowa.

26 Motero ananena ndi mfumu ya Asuri, kuti, Amitundu aja mudawacotsa kwao, ndi kuwakhalitsa m'midzi ya Samariya, sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli; cifukwa cace anawatumizira mikango pakati pao, ndipo taonani, irikuwapha; popeza sadziwa makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.

27 Pamenepo mfumu ya Asuri analamulira, kuti, Mukani naye komweko wina wa ansembe munawacotsako, nakakhale komweko, akawalangize makhalidwe a Mulungu wa dzikoli.

28 Nadza wina wa ansembewo adawacotsa ku Samariya, nakhala ku Beteli, nawalangiza m'mene azimuopera Yehova.

29 Koma a mtundu uli wonse anapanga milungu yao yao, naiika m'nyumba za misanje adazimanga Asamariya, a mtundu uli wonse m'midzi mwao mokhala iwo.

30 Ndipo anthu a Babulo anapanga Sukoti Bemoti, ndi anthu a Kuta anapanga Nerigali, ndi anthu a Hamati anapanga Asima,

31 ndi Aava anapanga Nibazi ndi Tarataka; ndi a Sefaravaimu anawatentha ana ao m'moto kwa Adrameleki, ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu.

32 Popeza anaopanso Yehova, anadziikira mwa iwo okha ansembe a misanje, ndiwo anaperekera nsembe m'nyumba za misanje.

33 Amaopa Yehova, namatumikiranso milungu yao, monga mwa miyambo ya amitundu anawacotsako.

34 Mpaka lero lino acita monga mwa miyambo yoyambayi; saopa Yehova, sacita monga mwa malemba ao, kapena maweruzo ao, kapena cilamulo, kapena coikika adacilamulira Yehova ana a Yakobo, amene anamucha Israyeli,

35 ndiwo amene Yehova adapangana nao, nawalamulira, ndi kuti, Musamaopa milungu yina, kapena kuigwadira, kapena kuitumikira, kapena kuiphera nsembe;

36 koma Yehova amene anakukwezani kukuturutsani m'dziko la Aigupto ndi mphamvu yaikuru, ndi dzanja lotambasuka, Iyeyu muzimuopa, ndi Iyeyu muzimgwadira, ndi Iyeyu muzimphera nsembe;

37 ndi malemba, ndimaweruzo, ndi cilamulo, ndi coikika anakulemberani muzisamalira kuzicita masiku onse, nimusamaopa milungu: yina;

38 ndi cipangano ndinacicita nanu musamaciiwala, kapena kuopa milungu yina iai;

39 koma Yehova Mulungu wanu muzimuopa, nadzakulanditsani Iyeyu m'dzanja la adani anu onse.

40 Koma sanamvera, nacita monga mwa mwambo wao woyamba.

41 Ndipo amitundu awa anaopa Yehova, natumikira mafano ao osema; ana ao omwe, ndi zidzukulu zao zomwe, monga anacita makolo ao, momwemo iwo omwe mpaka lero lino.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25