2 Mafumu 5 BL92

Namani wakhateyo aciritsidwa

1 Ndipo Namani kazembe wa khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu anali munthu womveka pamaso pa mbuyace, ndi waulemu; popeza mwa iye Yehova adapulumutsa Aaramu; ndiyenso ngwazi, koma wakhate.

2 Ndipo Aaramu adaturuka magulu magulu, nabwera nalo m'ndende buthu locokera ku dziko la Israyeli, natumikira mkazi wa Namani iyeyu,

3 Nati uyu kwa mbuyace wamkazi, Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali m'Samariya, akadamciritsa khate lace.

4 Ndipo analowa wina, nauza mbuye wace, kuti, Buthulo lofuma ku dziko la Israyeli lanena zakuti zakuti.

5 Pamenepo mfumu ya Aramu inati, Tiye, muka, ndidzatumiza kalata kwa mfumu ya Israyeli. Pamenepo anacoka, atatenga siliva: matalente khumi, ndi golidi masekeli zikwi zisanu ndi cimodzi, ndi zobvala zakusintha khumi.

6 Ndipo anafika kwa mfumu ya Israyeli ndi kalata, wakuti, Pakulandira kalata uyu, taonani, ndatumiza Namani mnyamata wanga kwa inu, kuti mumciritse khate lace.

7 Ndipo kunali atawerenga kalatayu mfumu ya Israyeli, anang'amba zobvala zace, nati, Ngati ndine Mulungu, kupha ndi kubwezera moyo, kuti ameneyo atumiza kwa ine kumciritsa munthu khate lace? pakuti dziwani, nimupenye, kuti alikufuna cifukwa pa ine.

8 Koma kunali, pamene Elisa munthu wa Mulungu anamva kuti mfumu ya Israyeli adang'amba zobvala zace, anatumiza mau kwa mfumu, ndi kuti, Mwang'amba zobvala zanu cifukwa ninji? Adzetu kwa ine, ndipo adzadziwa kuti muli mneneri m'Israyeli.

9 M'mwemo: Namani anadza ndi akavalo ace ndi magareta ace, naima pakhomo pa nyumba ya Elisa.

10 Ndipo Elisa anamtumira mthenga, ndi kuti, Kasambe m'Yordano kasanu ndi kawiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka.

11 Koma Namani adapsa mtima, nacoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kuturuka adzanditurukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wace, ndi kuweyula dzanja lace pamalopo, ndi kuciritsa wakhateyo.

12 Nanga Abana ndi Faripara, mitsinje ya Damasiko, siiposa kodi madzi onse a m'Israyeli? ndilekerenji kukasamba m'mwemo, ndi kukonzeka? Natembenuka, nacoka morunda.

13 Pamenepo anyamata ace anasendera, nanena naye, nati, Atate wanga, mneneri akadakuuzani cinthu cacikuru, simukadacicita kodi? koposa kotani nanga ponena iye, Samba, nukonzeke?

14 Potero anatsika, namira m'Yordano kasanu ndi kawiri, monga adanena munthu wa Mulunguyo; ndi mnofu wace unabwera monga mnofu wa mwana wamng'ono, nakonzeka.

15 Pamer nepo anabwerera kwa munthu wa Mulungu iye ndi gulu lace lonse, nadzaima pamaso pace, nati, Taonani, tsopano ndidziwa kuti palibe Mulungu pa dziko lonse lapansi, koma kwa Israyeli ndiko; ndipo tsopano, mulandire cakukuyamikani naco kwa mnyamata wanu.

16 Koma anati, Pali Yehova, amene ndiima pamaso pace, sindidzalandira kanthu. Ndipo anamkangamiza acilandire, koma anakana.

17 Ndipo Namani anati, Mukakana, andipatse akatundu a dothi osenza nyuru ziwiri; pakuti mnyamata wanu sadzaperekanso nsembe yopsereza kapena yophera kwa milungu yina, koma kwa Yehova.

18 Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ici; akalowa mbuye wanga m'nyumba ya Rimoni kulambiramo, nakatsamira pa dzanja langa, nanenso ndikagwadira m'nyumba ya Rimoni, pakugwadira ine m'nyumba ya Rimoni, Yehova akhululukire mnyamata wanu mwa ici.

19 Ndipo ananena naye, Pita mumtendere. Ndipo anacoka, nayenda kanthawi.

Gehazi alangidwa ndi khate

20 Koma Gehazi, mnyamata wa Elisa, munthu wa Mulungu, anati, Taona, mbuye wanga analekera Namani uyu wa ku Aramu osalandira m'manja ace cimene anabwera naco; pali Yehova, ndidzathamangira ndi kulandira kanthu kwa iye.

21 Motero Gehazi anatsata Namani. Ndipo pamene Namani anaona wina alikumthamangira, anatsika pagareta kukomana naye, nati, Nkwabwino kodi?

22 Nati, Kuli bwino. Mbuye wanga wandituma, ndi kuti, Taonani, andifikira tsopano apa anyamata awiri a ana a aneneri, ocokera ku mapiri a Efraimu; muwapatse talente wa siliva, ndi zobvala zosintha ziwiri.

23 Nati Namani, Viole ulandire matalente awiri. Namkangamiza namanga matalente awiri a siliva m'matumba awiri, ndi zobvala zosintha ziwiri, nasenzetsa anyamata ace awiri; iwo anatsogola atazisenza.

24 Ndipo pamene anafika kumsanje anazilandira m'manjamwao, naziika m'nyumba; nauza anthuwo amuke, iwo nacoka.

25 Pamenepo analowa, na, ima kwa mbuye wace. Ndipo Elisa ananena naye, Ufuma kuti Gehazi? Nati, Ngati mnyamata wanu wayenda konse?

26 Ndipo anati kwa iye, Mtima wanga sunakuperekeza kodi, umo munthuyo anatembenuka pa gareta wace kukomana ndi iwe? Kodi nyengo yino ndiyo yakulandira siliva, ndi kulandira zobvala, ndi minda yaazitona, ndi yampesa, ndi nkhosa, ndi ng'ombe, ndi akapolo; ndi adzakazi?

27 Cifukwa cace khate la Namani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako cikhalire. Ndipo anaturuka pamaso pace wakhate wa mbu ngati cipale cofewa.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25