2 Mafumu 8 BL92

Wa ku Sunemu abwera kwao itatha njalayo

1 Ndipo Elisa ananena ndi mkazi uja adamuukitsira mwana wace, kuti, Nyamuka, numuke iwe ndi banja lako, nugonere komwe ukaone malo; pakuti Yehova waitana njala, nidzagwera dziko zaka zisanu ndi ziwiri.

2 Nanyamuka mkaziyo, nacita monga mwa mau a munthu wa Mulunguyo, namuka ndi banja lace, nagonera m'dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.

3 Ndipo pakutha pace pa zaka zisanu ndi ziwirizo, mkaziyo anabwera kucoka m'dziko la Afilisti, naturuka kukanena za nyumba yace ndi munda wace kwa mfumu.

4 Koma mfumu inalikulankhula ndi Gehazi mnyamata wa munthu wa Mulungu, ndi kuti, Ndifotokozere zazikuru zonse Elisa wazicita.

5 Ndipo kunali, alimkufotokozera mfumu m'mene adamuukitsira wakufayo, taonani, mkaziyo adamuukitisira mwana wace ananena za nyumba yace ndi munda wace kwa mfumu. Nati Gehazi, Mbuye wanga mfumu, suyu mkaziyo, suyu mwana wace Elisa anamuukitsayo?

6 Ndipo pofunsa mfumu, mkaziyo anaisimbira. Pamenepo mfumu anamuikira mdindo, ndi kuti, Bwezetsa zace zonse ndi zipatso zonse za m'munda, cicokere iye m'dziko mpaka lero lino.

Hazaeli mfumu ya Aramu

7 Ndipo Elisa anafika ku Damasiko, podwala Benihadadi mfumu ya Aramu; ndipo anamuuza, kuti, Munthu wa Mulungu wadza kuno.

8 Niti mfumu kwa Hazaeli, Tenga caufulu m'dzanja lako, nukamkumike munthu wa Mulungu, nukafunsire Yehova mwa iye, ndi kuti, Ndidzacira kodi nthenda iyi?

9 Namuka Hazaeli kukakomana naye, napita naco caufulu, ndico ca zokoma zonse za m'Damasiko, zosenza ngamila makumi anai, nafika naima pamaso pace, nati, Mwana wanu Benihadadi mfumu ya Aramu, wandituma ine kwa inu, ndi kuti, Kodi ndidzacira nthenda iyi?

10 Nanena naye Elisa, Kamuuze, kuti, Sudzacira konse; popeza Yehova wandionetsa kuti adzafa ndithu.

11 Ndipo anamyang'ana cidwi, mpaka anacita manyazi, nalira misozi munthu wa Mulungu.

12 Nati Hazaeli, Muliriranji, mbuye wanga? Nayankha iye, Popeza ndidziwa coipa udzacitira ana a Israyeli; udzatentha malinga ao ndi moto, nudzapha anyamata ao ndi lupanga, nudzaphwanya makanda ao, nudzang'amba akazi ao okhala ndi pakati.

13 Nati Hazaeli, Koma nanga kapolo wanu ali ciani, ndiye garu, kuti akacite cinthu cacikuru ici? Nayankha Elisa, Yehova wandionetsa kuti udzakhala mfumu ya pa Aramu.

14 Ndipo anacoka kwa Elisa, nadza kwa mbuye wace; ameneyo ananena naye, Anakuuza ciani Elisa? Nati iye, Anandiuza kuti mudzacira ndithu.

15 Ndipo kunali m'mawa mwace, anatenga cimbwi, nacibviika m'madzi, naciphimba pankhope pa mfumu, nifa; ndipo Hazaeli analowa ufumu m'malo mwace.

Yehoramu mfumu ya Yuda

16 Ndipo caka cacisanu ca Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israyeli, pokhala Yehosafati mfumu ya Yuda, Yehoramu mwana wa Yehosafati analowa ufumu.

17 Ndiye wa zaka makumi atatu ndi ciwiri polowa ufumu wace, nacita ufumu zaka zisanu ndi zitatu ku Yerusalemu.

18 Nayenda m'njira ya mafumu a Israyeli, m'mene inacitira nyumba ya Ahabu; pakuti mkazi wace ndiye mwana wa Ahabu, nacita iye coipa pamaso pa Yehova.

19 Koma Yehova sanafuna kuononga Yuda, cifukwa ca Davide mtumiki wace monga adamuuza, kuti adzampatsa nyali ya kwa ana ace kosalekeza.

20 Masiku ace Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda, nadziikira mfumu okha.

21 Pamenepo Yoramu anaoloka kumka ku Zairi, ndi magareta ace onse pamodzi naye; nauka iye usiku, nakantha Aedomu akumzinga ndi nduna za magareta, nathawira anthu ku mahema ao.

22 Motero Aedomu anapanduka ku ulamuliro wa Yuda mpaka lero lino. Ndipo Alibina anapanduka nthawi yomweyi.

23 Ndi macitidwe ena a Yoramu, ndi zonse anazicita, sizinalembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda.

24 Nagona Yoramu ndi makolo ace, naikidwa pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide; ndipo Ahaziya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

Ahaziva mfumu ya Yuda

25 Caka cakhumi ndi ziwiri ca Yoramu mwana wa Ahabu mfumu Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda analowa ufumu wace.

26 Ahaziya ndiye, Wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu caka cimodzi. Ndi dzina la mace ndiye Ataliya mdzukulu wa Omri mfumu ya Israyeli.

27 Ndipo anayenda m'njira ya nyumba ya Ahabu, nacita coipa pamaso pa Yehova, m'mene inacitira nyumba ya Ahabu; pakuti ndiye wa cibale ca banja la Ahabu.

28 Ndipo anamuka Yoramu mwana wa Ahabu kukathira nkhondo pa Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Gileadi; ndi Aaramu analasa Yoramu.

29 Ndipo mfumu Yoramu anabwera kuti ampoletse m'Yezreeli mabalawo adamkantha Aaramu ku Rama, polimbana naye Hazaeli mfumu ya Aramu, Natsikirako Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda kukamuona Yoramu mwana wa Ahabu m'Yezreeli, pakuti anadwala.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25