2 Mafumu 11 BL92

A taliya aononga mbumba yacifumu ya Yuda; apulumuka Yoasi, aphedwa Ataliya

1 Pamene Ataliya mace wa Ahaziya anaona kuti mwana wace wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yacifumu.

2 Koma Yoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wace wa Ahaziya, anatenga Yoasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'cipinda cogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwa.

3 Nakhala naye wobisika m'nyumba ya Yehova zaka zisanu ndi cimodzi; ndipo Ataliya anakhala mfumu ya dziko.

4 Koma caka cacisanu ndi ciwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye ku nyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m'nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu.

5 Nawalamulira, kuti, Cocita inu ndi ici: limodzi la magawo atatu la inu olowa pa Sabata lizilindira nyumba ya mfumu,

6 ndi lina lizikhala ku cipata ca Suri, ndi lina ku cipata kumbuyo kwa otumikira; momwemo muzisunga nyumba, ndi kuicinjiriza.

7 Ndipo magawo awiri ainu, ndiwo onse oturukira pa Sabata, azilindira nyumba ya Yehova kuzinga mfumu.

8 Ndipo muzizinga mfumu, yense zida zace m'manja mwace, ndi iye wakulowa poima inupo aphedwe; ndipo muzikhala inu ndi mfumu poturuka ndi polowa iye.

9 Ndipo atsogoleri a mazana anacita monga mwa zonse anawalamulira Yehoyada wansembe, natenga yense anthu ace olowera pa Sabata, ndi oturukira pa Sabata, nafika kwa Yehoyada wansembeyo.

10 Ndipo wansembeyo anapereka kwa atsogoleri a mazana mikondo ndi zikopa, zinali za mfumu Davide, zosungika m'nyumba ya Yehova.

11 Ndipo otumikira anakhala ciriri yense ndi zida zace m'manja mwace, kuyambira mbali ya kulamanja kufikira mbali ya kulamanzere ya nyumbayo, ku guwa la nsembe, ndi kunyumba, kuzinga mfumu.

12 Atatero, anaturutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m'manja, nati, Mfomu ikhale ndi movo.

13 Pamene Ataliya anamva phokoso la otumikira ndi anthu, anadza kwa anthu m'nyumba ya Yehova;

14 napenya, ndipo taonani, mfumu iri ciriri paciundo, monga adafocita, ndi atsogoleri ndi amalipenga pali mfomu; nakondwerera anthu onse a m'dziko, naomba malipenga. Pamenepo Ataliya anang'amba zobvala zace, napfuula, Ciwembu, Ciwembu.

15 Koma Yehoyada wansembe analamulira atsogoleri a mazana oyang'anira khamu, nanena nao, Mumturutse mkaziyo pabwalo pakati pa mipambo; womtsata iye mumuphe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Asaphedwe m'nyumba ya Yehova.

16 Ndipo anamgwira, napita naye njira yolowera akavalo ku nyumba ya mfumu, namupha pomwepo.

17 Ndipo Yehoyada anacita cipangano pakati pa Yehova ndi mfomu ndi anthu, akhale anthu a Yehova; pakati pa mfumunso ndi anthu.

18 Namuka anthu onse a m'dzikomo ku nyumba ya Baala, naigumula; maguwa ace a nsembe ndi mafano ace anawaswaiswa, napha Matana wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe. Ndipo wansembeyo anaika oyang'anira nyumba ya Yehova.

19 Napita nao atsogoleri a mazana, ndi opha anthu, ndi otumikira, ndi anthu onse a m'dziko; ndipo iwo anatsika nayo mfumu ku nyumba ya Yehova, nadzera njira ya cipata ca otumikira, kumka ku nyumba ya mfomu. Nakhala Iye pa cimpando ca mafumu.

20 Nakondwerera anthu onse a m'dziko, ndi m'mudzi munali phe; ndipo adapha Ataliya ndi lupanga ku nyumba ya mfumu.

21 Yoasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri polowa iye ufumu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25