1 Ndipo kunali, pamene Yehova adati akweze Eliya kumwamba ndi kabvumvulu, Eliya anacokera ku Giligala pamodzi ndi Elisa.
2 Ndipo Eliya anati kwa Elisa, Ukhale pompano pakuti Yehova wandituma ndimke ku Beteli. Nati Elisa, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Motero anatsikira iwo ku Beteli.
3 Ndipo ana a aneneri okhala ku Beteli anaturukira Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akucotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati, lode ndidziwa, khalani muli cete.
4 Ndipo Eliya anati kwa iye, Elisa, ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yeriko. Nati iye, Pali Yehova, pali inu, sindikusiyani. Motero anadza ku Yeriko.
5 Pamenepo ana a aneneri okhala ku Yeriko anayandikira kwa Elisa, nanena naye, Kodi udziwa kuti Yehova akucotsera lero mbuye wako, mtsogoleri wako? Nati iye, Inde ndidziwa, khalani muli cete.
6 Ndipo Eliya ananena naye, Ukhale pompano, pakuti Yehova wandituma ku Yordano, Nati iye, Pali Mulungu, pali inu, sindikusiyani. Napitirira iwo awiri.
7 Ndipo anthu makumi asanu a ana a aneneri anapita, naima patali pandunji pao, iwo awiri naima ku Yordano.
8 Ndipo Eliya anagwira copfunda cace, nacipindapinda napanda madzi, nagawikana kwina ndi kwina; ndipo anaoloka iwo onse awiri pansi pouma.
9 Ndipo kunali ataoloka, Eliya anati kwa Elisa, Tapempha cimene ndikucitire ndisanacotsedwe kwa iwe. Ndipo Elisa anati, Mundipatse magawo awiri a mzimu wanu akhale pa ine.
10 Nati iye, Wapempha cinthu capatali, koma ukandipenya pamene ndicotsedwa kwa iwe, kudzatero nawe; koma ukapanda kundipenyapo, sikudzatero at.
11 Ndipo kunacidka, akali ciyendere ndi kukambirana, taonani, anaoneka gareta wamoto ndi akavalo amoto, nawalekanitsa awiriwa; Eliya nakwera kumwamba ndi kabvumvulu.
12 Ndipo Elisa anapenya, napfuula, Atate wanga, atate wanga, gareta wa Israyeli ndi apakavalo ace! Koma analibe kumpenyanso; nagwira zobvala zace zace, nazing'amba pakati.
13 Pamenepo anatola copfunda cace ca Eliya cidamtayikiraco, nabwerera, naima m'mphepete mwa Yordano.
14 Ndipo anatenga copfunda ca Eliya cidamtayikiraco, napanda madziwo, nati, Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya? Ndipo atapanda madziwo anagawikana kwina ndi kwina, naoloka Elisa.
15 Ndipo pamene anampenya ana a aneneri okhala ku Yeriko pandunji pace, anati, Mzimu wa Eliya watera pa Elisa. Ndipo anadza kukomana naye, nadziweramitsa pansi kumaso kwace.
16 Ndipo ananena naye, Taonani, tsono anyamata anufe tiri nao amuna makumi asanu amphamvu, amuke kukafuna mbuye wanu; kapena wamkweza mzimu wa Yehova ndi kumponya pa phiri lina, kapena m'cigwa dna. Koma anati, Musatumiza.
17 Koma anamuumiriza kufikira anacita manyazi; pamenepo anati, Tumizani. Motero anatumiza amuna makumi asanu, namfunafuna iwo masiku atatu, osampeza.
18 Nabwerera kwa iye ali cikhalire ku Yeriko, ndipo anati kwa iwo, Kodi sindinanena nanu, Musamuka?
19 Ndipo amuna a kumudzi anati kwa Elisa, Taonani, pamudzi pano mpabwino, monga umo aonera mbuye wanga; koma madzi ndi oipa, ndi nthaka siibalitsa.
20 Pamenepo anati, Nditengereni cotengera catsopano, muikemo mcere. Ndipo anabwera naco kwa iye.
21 Ndipo anaturuka kumka ku magwero a madzi, nathiramo mcere, nati, Atero Yehova, Ndaciritsa madzi awa, sikudzafumirakonso imfa, kapena kusabalitsa.
22 Cotero madzi anaciritsidwa mpaka lero lino, monga mwa mau a Elisa ananenawo.
23 Ndipo anacokako kukwera ku Beteli, ndipo iye ali cikwerere m'njiramo, munaturuka anyamata ang'ono m'mudzimo, namseka, nati kwa iye, Takwera wadazi, takwera wadazi!
24 Ndipo anaceuka, nawaona, nawatemberera m'dzina la Yehova. Ndipo kuthengo kunaturuka zimbalangondo ziwiri zazikazi, ndi kupwetedza mwa iwo ana makumi anai mphambu awiri.
25 Ndipo anacokako kumka ku phiri la Karimeh; nabwera kumeneko nafika ku Samariya.