2 Mafumu 13 BL92

Yoahazi mfumu ya Israyeli

1 Caka ca makumi awiri ndi zitatu ca Yoasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yoahazimwana wa Yehu analowa ufumu wace wa Israyeli ku Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri.

2 Nacita coipa pamaso pa Yehova, natsata zolakwa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli; sanazileka.

3 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayaka pa Israyeli, nawapereka m'dzanja la Hazaeli mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaeli, masiku onsewoo

4 Koma Yoahazi anapembedza Yehova, Yehova namvera; pakuti anapenya kupsinjika kwace kwa Israyeli m'mene mfumu ya Aramu inawapsinja.

5 Ndipo Yehova anapatsa Israyeli mpulumutsi, naturuka iwo pansi pa dzanja la Aaramu; nakhala ana a Israyeli m'mahema mwao monga kale.

6 Komatu sanalekana nazo zolakwa za nyumba ya Yerobiamu, zimene analakwitsa nazo Israyeli, nayenda m'mwemo; nicitsalanso cifanizo m'Samariya.

7 Koma mfumu ya Aramu sanasiyira Yoahazi anthu, koma apakavalo makumi asanu, ndi magareta khumi, ndi oyenda pansi zikwi khumi; popeza mfumu ya Aramu anawaononga, nawayesa ngati pfumbi lopondapo.

8 Macitidwe ena tsono a Yoahazi, ndi zonse anazicita, ndi mphamvu yace, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

9 Ndipo Yoahazi anagona ndi makolo ace, namuika m'Samariya; nakhala mfumu m'malo mwace Yoasi mwana wace.

Yoasi mfumu ya Israyeli

10 Caka ca makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri ca Yoasi mfumu ya Yuda, Yoasi mwana wa Yoahazi analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi cimodzi.

11 Nacita coipa pamaso pa Yehova, osazileka zolakwa zonse za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli, koma anayendamo.

12 Macitidwe ena tsono a Yoasi, ndi zonse anazicita, ndi mphamvu yace yocita nkhondo nayo pa Amaziya mfumu ya Yuda, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

13 Ndipo Yoasi anagona ndi makolo ace, ndi Yerobiamu anakhala pa mpando wacifumu wace; namuika Yoasi m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israyeli.

Kumwalira kwa Elisa

14 Ndipo Elisa anadwala nthenda ija adafa nayo, namtsikira Yoasi mfumu ya Israyeli, namlirira, nati, Atate wanga, atate wanga, gareta wa Israyeli ndi apakavalo ace!

15 Nanena naye Elisa, Tenga uta ndi mibvi; nadzitengera uta ndi mibvi.

16 Nati kwa mfumu ya Israyeli, Pingiridzani. Napingiridza. Ndipo Elisa anasanjika manja ace pa manja a mfumu.

17 Nati, Tsegulani zenera la kum'mawa. Nalitsegula. Nati Elisa, Ponyani. Naponya. Nati iye, Mubvi wa cipulumutso wa Yehova ndiwo mubvi wa kukupulumutsani kwa Aaramu; popeza mudzakantha Aaramu m'Afeki mpaka mudzawatha.

18 Nati iye, Tengani mibvi; naitenga, Nati kwa mfumu ya Israyeli, Kwapula pansi; nakwapula katatu, naleka.

19 Nakwiya naye munthu wa Mulungu, nati, Mukadakwapula kasanu, kapena kasanu ndi kamodzi; mukadatero, mukadadzakantha Aaramu mpaka kuwatha; koma tsopano mudzawakantha Aaramu katatu kokha.

20 Pamenepo Elisa anamwalira, ndipo anamuika. Ndipo magulu a Amoabu analowa m'dziko poyambira caka.

21 Ndipo anthu, pakuika maliro a munthu wina, anaona gulu la nkhondo, naponya mtembo m'manda mwa Elisa; koma pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, wakufayo anauka, naima ciriri.

22 Ndipo Hazaeli mfumu ya Aramu anapsinja Israyeli masiku onse a Yoahazi.

23 Koma Yehova analeza nao mtima, nawacitira cifundo, nawatembenukira; cifukwa ca cipangano cace ndi Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, wosafuna kuwaononga, kapena kuwatayiratu pankhope pace.

24 Nafa Hazaeli mfumu ya Aramu, nakhala mfumu m'malo mwace Benihadadi mwana wace.

25 Ndi Yoasi mwana wa Yoahazi analandanso m'dzanja la Benihadadi mwana wa Hazaeli midzi ija adailanda m'dzanja la Yoahazi atate wace ndi nkhondo. Yoasi anamkantha katatu, naibweza midzi ya Israyeli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25