2 Mafumu 18 BL92

Hezekiya wabwino akhazikanso cipembedzo ca Yehova

1 Ndipo kunali caka cacitatu ca Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israyeli, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu waceo

2 Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Abi mwana wa Zekariya.

3 Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazicita Davide kholo lace.

4 Anacotsa misanje, naphwanya zoimiritsa, nalikha cifanizo, naphwanya njoka ija yamkuwa adaipanga Mose; pakuti kufikira masiku awa ana a Israyeli anaifukizira zonunkhira, naicha Cimkuwa.

5 Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israyeli; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye.

6 Pakuti anaumirira Yehova osapambuka pambuyo pace, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.

7 Ndipo Yehova anali naye, nacita iye mwanzeru kuli konse anamukako, napandukira mfumu ya Asuri osamtumikira.

8 Anakantha Afilisti mpaka Gaza ndi malire ace, kuyambira nsanja ya olonda mpaka mudzi walinga.

9 Ndipo kunali caka cacinai ca mfumu Hezekiya, ndico caka cacisanu ndi ciwiri ca Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israyeli Salimanezeri mfumu ya Asuri anakwerera Samariya, naumangira misasa.

10 Pakutha pace pa zaka zitatu anaulanda, ndico caka cacisanu ndi cimodzi ca Hezekiya, ndico caka cacisanu ndi cinai ca Hoseya mfumu ya Israyeli analanda Samariya.

11 Ndipo mfumu ya Asuri anacotsa Aisrayeli kumka nao ku Asuri, nawakhalitsa m'Hala, ndi m'Habori, ku mtsinje wa Gozani, ndi m'midzi ya Amedi;

12 cifukwa sanamvera mau a Yehova Mulungu wao, koma analakwira cipangano cace, ndico zonse anazilamulira Mose mtumiki wa Yehova; sanazimvera kapena kuzicita.

Sanakeribu amangira Yerusalemu misasa

13 Caka cakhumi ndi zinai ca Hezekiya Sanakeribu mfumu ya Asuri anakwerera midzi yonse ya malinga ya Yuda, nailanda.

14 Natumiza Hezekiya mfumu ya Yuda kwa mfumu ya Asuri ku Lakisi, ndi kuti, Ndalakwa; mundicokere; cimene mundisenzetse ndisenza. Pamenepo mfumu ya Asuri anaikira Hezekiya mfumu ya Yuda matalente mazana atatu a siliva ndi matalente makumi atatu a golidi.

15 Napereka Hezekiya siliva yense wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku cuma ca nyumba yamfumu.

16 Nthawi yomweyi Hezekiya anakanganula golidi wa pa zitseko za Kacisi wa Yehova, ndi pa zimphuthu adazikuta Hezekiya mfumu ya Yuda, nampereka kwa mfumu ya Asuri.

17 Ndipo mfumu ya Asuri anatuma nduna ndi ndoda ndi kazembe ocokera ku Lakisi ndi khamu lalikuru la nkhondo kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Nakwera iwo, nafika ku Yerusalemu. Ndipo atakwera, anafika, naima ku mcerenje wa thamanda la kumtunda, ndilo la ku mseu wa ku mwaniko wa otsuka nsaru.

18 Ndipo m'mene adaitana mfumu, anawaturukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yoa mwana wa Asafu wolemba mbiri.

19 Nanena nao kazembeyo, Muuzetu Hezekiya, Itero mfumu yaikuru, mfumu ya Asuri, Cikhulupiriro ici ncotani ucikhulupirira?

20 Ukuti koma ndiwo mau a pakamwa pokha, Pali uphungu ndi mphamvu ya kunkhondo. Tsono ukhulupirira yani, kuti undipandukira?

21 Taona tsono ukhulupirira ndodo ya bango ili lothyoka, ndilo Aigupto; ndilo munthu akatsamirapo lidzamlowa m'dzanja lace ndi kulibola; atero Farao mfumu ya Aigupto kwa onse omkhulupirira iye.

22 Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamcotsera misanje yace ndi maguwa a nsembe ace, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira pa guwa la nsembe pane m'Yerusalemu?

23 Mukokerane tsono ndi mbuye wanga mfumu ya Asuri, ndipo ndidzakupatsani akavalo zikwi ziwiri, mukakhoza inu kuonetsa apakavalo.

24 Posakhoza kutero, mudzabweza bwanji nkhope ya nduna imodzi ya anyamata ang'ono a mbuye wanga, ndi kukhulupirira Aigupto akupatse magareta ndi apakavalo?

25 Ngati ndakwerera malo ana wopanda Yehova, kuwaononga? Yehova anati kwa ine, Kwerera dziko ili ndi kuliononga.

26 Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yoa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu m'Ciaramu; popeza ticimva ici; musalankhule nafe m'Ciyuda, comveka ndi anthu okhala palinga.

27 Koma kazembeyo ananena nao, Ngati mbuyanga ananditumiza kwa mbuyako, ndi kwa iwe, kunena mau awa? si kwa anthu awa nanga okhala palinga, kuti akadye zonyansa zao, ndi kumwa mkodzo wao pamodzi ndi inu?

28 Naima kazembeyo, napfuula ndi mau akulu m'Ciyuda, nanena kuti, Tamverani mau a mfumu yaikuru mfumu ya Asuri.

29 Itero mfumu, Asakunyengeni Hezekiya; pakuti sadzakhoza kukulanditsani m'dzanja lace;

30 kapena Hezekiya asakukhulupiritseni pa Yehova, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa ndithu, ndi mudzi uwu sudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya Asuri.

31 Musamvere Hezekiya; pakuti Itero mfumu ya Asuri, Mupangane nane zamtendere, nimuturukire kwa ine, ndi kumadya yense ku mpesa wace, ndi yense ku mkuyu wace, ndi kumwa yense madzi a m'citsime cace;

32 mpaka ndifika ndi kumuka nanu ku dziko lakunga dziko lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la mkate ndi minda yampesa, dziko la azitona ndi la uci; kuti mukhale ndi moyo osafai; nimusamvere Hezekiya akakukopani, ndi kuti, Yehova adzatilanditsa.

33 Kodi mlungu uli wonse wa amitundu walanditsa dziko lace m'dzanja la mfumu ya Asuri ndi kale lonse?

34 Iri kuti milungu ya Hamati, ndi ya Aripadi? iri kuti milungu ya Sefaravaimu, kapena Hena, ndi Iva? Kodi yalanditsa Samariya m'dzanja langa?

35 Ndi yiti mwa milungu yonse ya maiko inalanditsa maiko ao m'dzanja langa, kuti Yehova adzalanditsa Yerusalemu m'dzanja langa?

36 Koma anthuwo anakhala cete osamyankha mau; pakuti lamulo la mfumu ndilo kuti, Musamuyankha.

37 Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yoa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zobvala zao zong'ambika, namuuza mau a kazembeyo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25