2 Mafumu 25 BL92

Yerusalemu apasulidwa, anthu natengedwa kunka ku Babulo

1 Ndipo kunali caka cacisanu ndi cinai ca ufumu wace, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babulo, iye ndi khamu lace lonse anadzera Yerusalemu, naumangira misasa, naumangira timalinga mouzinga.

2 Ndipo mudziwo unazingidwa ndi timalinga mpaka caka cakhumi ndi cimodzi ca mfumu Zedekiya.

3 Tsiku lacisanu ndi cinai la mwezi wacinai njala idakula m'mudzimo, panalibe cakudya kwa anthu a m'dzikomo.

4 Pamenepo linga la mudziwo linagamulidwa, nathawira ankhondo onse usiku, njira ya ku cipata ca pakati pa makoma awiri, iri ku munda wa mfumu; Akasidi tsono anali pamudzi pouzinga; nimuka mfumu pa njira ya kucidikha.

5 Koma nkhondo ya Akastdi inalondola mfumu, niipeza m'zidikha za Yeriko; koma nkhondo yace yonse inambalalikira.

6 Ndipo anaigwira mfumu, nakwera nayo kwa mfumu ya Babulo ku Ribila, naweruza mlandu wace.

7 Napha ana a Zedekiya pamaso pace, namkolowola Zedekiya maso ace, nammanga ndi maunyolo amkuwa, namuka nave ku Babulo.

8 Ndipo mwezi wacisanu, tsiku lacisanu ndi ciwiri la mweziwo, ndico caka cakhumi mphambu cisanu ndi cinai ca mfumu Nebukadinezara mfumu ya Babulo, Nebuzaradani mkuru wa olindirira, ndiye mnyamata wa mfumu ya Babulo, anadza ku Yerusalemu,

9 natentha nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za m'Yerusalemu; ndi nyumba zonse zazikuru anazitentha ndi moto.

10 Ndi khamu lonse la Akasidi linali ndi mkuru wa olindirira linagumula linga la Yerusalemu louzinga.

11 Ndi anthu otsalira m'mudzi, ndi opanduka akuthawira kwa mfumu ya Babulo, ndi aunyinji otsalira, Nebuzaradani mkuru wa olindirira anamuka nao andende.

12 Koma mkuru wa olindirira anasiya osaukadi a m'dziko akhale osunga minda yampesa, ndi alimi,

13 Ndipo zoimiritsa zamkuwa zinali m'nyumba ya Yehova, ndi maphaka ace, ndi thawale lamkuwa, zinali m'nyumba ya Yehova, Akasidi anazithyolathyola, natenga mkuwa wace kumka nao ku Babulo.

14 Nacotsanso miphika, ndi zoolera, ndi zozimira nyali, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo.

15 Ndi zoparira moto, ndi mbale zowazira za golidi yekha yekha, ndi zasiliva yekha yekha, mkuru wa asilikari anazicotsa.

16 Nsanamira ziwiri, thawale limodzi, ndi maphakawo adazipangira nyumba ya Yehova Solomo, mkuwa wa zipangizo izi zonse sanakhoza kuyesa kulemera kwace.

17 Msinkhu wace wa nsanamira imodzi ndiwo mikono khumi mphambu isanu ndi itatu, ndi pamwamba pace mutu wamkuwa; ndi msinkhu wace wa mutuwo ndiwo mikono itatu, ndi ukonde, ndi makangaza pamutu pouzinga, zonse zamkuwa; ndi nsanamira inzace inali nazo zomwezo pamodzi ndi ukonde.

18 Ndipo mkuru wa olindirira anatenga Seraya wansembe wamkulu, ndi Zefaniya wansembe waciwiri, ndi olindira pakhomo atatu;

19 natenga m'mudzimo mdindo woikidwa woyang'anira ankhondo; ndi anthu asanu a iwo openya nkhope ya mfumu opezeka m'mudzimo; ndi mlembi, kazembe wa nkhondo wolembera anthu a m'dziko; ndi anthu a m'dziko makumi asanu ndi limodzi opezeka m'mudzimo.

20 Ndipo Nebuzaradani mkuru wa olindirira anawatenga, napita nao kwa mfumu ya Babulo ku Ribila.

21 Niwakantha mfumu ya Babulo, niwaphera ku Ribila m'dziko la Hamati. Motero anamuka nao Ayuda andende kuwacotsa m'dziko lao.

Gedaliya wolamulira m'Yerusalemu aphedwa ndi Ismayeli

22 Koma kunena za anthu otsalira m'dziko la Yuda, amene adawasiya Nebukadinezara mfumu ya Babulo, iyeyu anamuika Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani akhale wowalamulira.

23 Ndipo pamene anamva akazembe onse a makamu, iwo ndi anthu ao, kuti mfumu ya Babulo adaika Gedaliya wowalamulira, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, ndiwo Ismayeli mwana wa Netaniya, ndi Yohanana mwana wa Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti wa ku Netofa, ndi Yazaniya mwana wa Mmakati, iwo ndi anthu ao omwe.

24 Nawalumbirira Gedaliya iwo ndi anthu ao, nanena nao, Musamaopa anyamata a Akasidi; khalani m'dziko; tumikirani mfumu ya Babulo, ndipo kudzakukomerani.

25 Koma kunali mwezi wacisanu ndi ciwiri anadza Ismayeli mwana wa Netaniya mwana wa Elisama, wa mbumba yacifumu, ndi anthu khumi pamodzi naye, nakantha Gedaliya; nafa iye, ndi Ayuda, ndi Akasidi okhala naye ku Mizipa.

26 Pamenepo ananyamuka anthu onse ang'ono ndi akuru, ndi akazembe a makamu, nadza ku Aigupto; pakuti anaopa Akasidi.

27 Ndipo kunali caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri ca kumtenga ndende Yoyakini mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi ziwiri, tsiku la makumi awiri mphambu asanu ndi awiri la mwezi, Evili Merodaki mfumu ya Babulo anamuweramutsa mutu wace wa Yoyakini mfumu ya Yuda aturuke m'kaidi, caka colowa iye ufumu wace;

28 nakamba naye zokoma, namkweza mpando wace waulemu upose mipando ya mafumu anali pamodzi naye m'Babulo.

29 Nasintha zobvala zace za m'kaidi, namadya iye mkate pamaso pace masiku onse a moyo wace.

30 Ndi kunena za cakudya cace, panali cakudya cosalekeza copatsidwa kwa iye ndi mfumu, tsiku Uri lonse gawo lace, masiku onse a moyo wace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25