2 Mafumu 20 BL92

Hezekiya adwala nacira

1 Masiku ajawo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Namdzera Yesaya mneneri mwana wa Amozi, nanena naye, Atero Yehova, Siyira banja lako; pakuti udzafa, sudzakhala ndi moyo.

2 Pamenepo anatembenuzira nkhope yace kukhoma, napemphera kwa Yehova, ndi kuti,

3 Mukumbukile Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'coonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kucita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukuru.

4 Ndipo kunali, asanaturukire Yesaya m'kati mwa mudzi, anamdzera mau a Yehova, ndi kuti,

5 Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, nelidzakuciritsa, tsiku lacitatu udzakwera kumka ku nyumba ya Yehova.

6 Ndipo ndakuonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu; ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'dzanja la mfumu ya Asuri; ndidzacinjiriza mudzi uno, cifukwa ca Ine ndekha, ndi cifukwa ca Davide mtumiki wanga.

7 Nati Yesaya, Tenga ncinci yankhuyu. Naitenga, naiika papfundo, nacira iye.

8 Nati Hezekiya kwa Yesaya, Cizindikilo cace nciani kuti Yehova adzandiciza, ndi kuti ndidzakwera kumka ku nyumba ya Yehova tsiku lacitatu?

9 Nati Yesaya, Cizindikilo ndici akupatsa Yehova, kuti Yehova adzacicita conena iye; kodi mthunzi umuke m'tsogolo makwerero khumi, kapena ubwerere m'mbuyo makwerero khumi?

10 Nati Hezekiya, Kutsikira mthunzi makwerero khumi nkopepuka, kutero ai; koma mthunzi ubwerere makwerero khumi.

11 Napfuulirakwa Yehova Yesayamneneriyo, nabweza iye mthunzi m'mbuyo makwerero khumi, ndiwo amene udatsikira pa makwerero a Ahazi.

Hezekiya acimwa mwa kuonetsa cuma cace

12 Nthawi ija Berodaki Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Sabulo anatumiza akalata ndi mtulo kwa Hezekiya, popeza adamva kuti adadwala Hezekiya.

13 Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya cuma cace, siliva, ndi golidi, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zace, ndi zonse zopezeka pacuma pace; panalibe kanthu m'nyumba mwace, kapena m'ufumu wace wonse osawaonetsa Hezekiya.

14 Koma Yesaya mneneri anadza kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Anatani anthu awa? anadza kwa inu kufumira kuti? Nati Hezekiya, Afumira dziko la kutari ku Babulo.

15 Nati iye, Anaona ciani m'nyumba mwanu? Nati Hezekiya, Zonse za m'nyumba mwanga anaziona, palibe kanthu pacuma canga kosawaonetsa.

16 Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Tamverani mau a Yehova.

17 Taonani, akudza masiku kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zokundika makolo ako mpaka lero, zidzatengedwa kumka ku Babulo, kosasiyidwa kanthu konse, ati Yehova.

18 Nadzatenga ena a ana ako oturuka mwa iwe, amene udzawabala, nadzakhala iwo adindo m'cinyumba ca mfumu ya Babulo.

19 Pamenepo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova udawanena ndi abwino. Natinso, Si momwemo nanga, mtendere ndi coonaeli zikakhala masiku anga?

20 Macitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi mphamvu yace yonse, ndi umo anamangira dziwe ndi mcera, nautengera mudzi madzi, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

21 Nagona Hezekiya ndi makolo ace; nakhala mfumu m'malo mwace Manase mwana wace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25