2 Mafumu 22 BL92

Yosiya wabwino akonzanso kacisi

1 Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu cimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndi Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati.

2 Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m'njira yonse ya Davide kholo lace, osapambukira ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.

3 Ndipo kunali caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca Yosiya, mfumuyi inatuma Safani mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu, mlembi, ku nyumba ya Yehova, ndi kuti,

4 Kwera kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, awerenge ndalama zimene anthu anabwera nazo ku nyumba ya Yehova, ndizo zimene olindira pakhomo anasonkhetsa anthu; azipereke m'dzanja anchito akuyang'anira nyumba ya Yehova;

5 iwo azipereke kwa ogwira nchito ya m'nyumba ya Yehova, akonze mogamuka nyumbayi,

6 kwa amisiri a mitengo, ndi omanga nyumba, ndi omanga linga; ndi kuti agule mitengo ndi miyala yosema kukonza nazo nyumbayi.

7 Koma sanawawerengera ndalamazo zoperekedwa m'dzanja lao, pakuti anacita mokhulupirika.

Hilikiya apeza buku la cilamulo

8 Ndipo Hilikiya mkulu wa ansembe anati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la cilamulo m'nyumba ya Yehova. Napereka Hilikiya bukulo kwa Safani, iye naliwerenga.

9 Ndipo Safani mlembiyo anadza kwa mfumu, nambwezera mfumu mau, nati, Anyamata anu anakhuthula ndalama zopereka m'nyumba, nazipereka m'dzanja la anchito akuyang'anira nyumba ya Yehova.

10 Ndipo Safani mlembiyo anafotokozera mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe wandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu.

11 Ndipo kunali, atamva mfumu mau a m'buku la cilamulo, inang'amba zobvala zace.

12 Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Alabori mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti,

13 Mukani, funsirani ine, ndi anthu, ndi Yuda yense, kwa Yehova za mau a buku ili adalipeza; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukuru; popeza atate athu sanamvera mau a buku ili, kucita monga mwa zonse zotilemberamo.

Hulida mneneri wamkazi

14 Namuka Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu, ndi Akibori, ndi Safani, ndi Asaya, kwa Hulida mneneri wamkazi, ndiye mkazi wa Salumu mwana wa Tlkiva, mwana wa Harasi, wosunga zobvala za mfumu; analikukhala iye m'Yerusalemu m'dera laciwiri, nalankhula naye.

15 Ndipo Hulida ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Muuze munthuyo anakutumizani kwa ine,

16 Atero Yehova, Ta, onani, nditengera maloano coipa, ndi iwo okhalamo, cokwaniritsa mau onse a m'buku adaliwerenga mfumu ya Yuda;

17 popeza anandisiya Ine, nafukizira zonunkhira milungu yina, kuti autse mkwiyo wanga ndi nchito zonse za manja ao; cifukwa cace mkwiyo wanga udzayakira malo ana wosazimikanso.

18 Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero naye, Atero Yehova Mulungu wa Israyeli, Kunena za mau udawamva,

19 popeza mtima wako ngoolowa, ndipo unadzicepetsa pamaso pa Yehova muja udamva zonenera Ine malo ana ndi anthu okhalamo, kuti adzakhala abwinja, ndi temberero; ndipo unang'amba zobvala zako ndi kulira misozi pamaso panga, Inenso ndakumvera, ati Yehova.

20 Cifukwa cace, taona, ndidzakusonkhanitsa ukhale ndi makolo ako, nudzatengedwa ulowe m'manda mwako mumtendere; ndipo sudzaona m'maso mwako coipa conse ndidzacifikitsira malo ano. Ndipo anambwezera mfumu mau.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25