1 Caka cacisanu ndi ciwiri ca Yehu, Yoasi analowa ufumu wace; nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi anai; ndi dzina la mai wace ndiye Zibiya wa ku Beereseba.
2 Ndipo Yoasi anacita zoongoka pamaso pa Yehova masiku ace onse, m'mene anamlangizira wansembe Yehoyada.
3 Koma misanje sanaicotsa; anthu anapherabe nsembe, nafukiza komisanje.
4 Ndipo Yoasi anati kwa ansembe, Landirani ndarama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo ku nyumba ya Yehova, ndizo ndarama za otha msinkhu, ndarama za munthu ali yense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m'mtima mwace kuti abwere nazo ku nyumba ya Yehova.
5 Ansembe azilandire yense kwa iye amene adziwana naye, akonze nazo mogamuka nyumba, pali ponse akapeza pogamuka.
6 Koma kunali, caka ca makumi awiri mphambu zitatu ca Yoasi sanathe kukonza mogamuka nyumba.
7 Pamenepo mfumu Yoasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndarama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba.
8 Nabvomera ansembe kusalandiranso ndarama za anthu, kapena kukonza mogamuka nvumba.
9 Ndipo Yehoyada wansembe anatenga bokosi, naboola ciboo pa cibvundikilo cace, naliika pafupi pa guwa la nsembe, ku dzanja lamanja polowera nyumba ya Yehova; ndipo ansembe akusunga pakhomo anaikamo ndarama zonse anabwera nazo anthu ku nyumba ya Yehova,
10 Ndipo pakuona kuti ndarama zidacuruka m'bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkuru wansembe, nazimanga m'matumba, naziyesa ndalama zopereka m'nyumba ya Yehova.
11 Napereka ndarama zoyesedwa m'manja mwa iwo akucita nchitoyi, akuyang'anira nyumba ya Yehova; ndipo iwo analipira nazo amisiri a mitengo ndi omanga, akugwira nchito ya pa nyumba ya Yehova,
12 ndi omanga miyala ndi osema miyala, ndi kugula mitengo ndi miyala yosema kukakonza mogamuka nyumba ya Yehova, ndi zonse zoigulira nyumba zoikonzera.
13 Koma sanapangira nyumba ya Yehova mbale zasiliva, mbano, mbale zowazira, malipenga, zotengera ziri zonse zagolidi, kapena zotengera ziri zonse zasiliva, kuzipanga ndi ndarama adabwera nazo ku nyumba ya Yehova;
14 pakuti anazipereka kwa iwo akugwira nchitoyi, nakonza nazo nyumba ya Yehova.
15 Ndipo sanawerengera anthu, amene anapereka ndaramazi m'manja mwao kuti apatse ogwira nchito; popeza anacita mokhulupirika.
16 Ndarama za nsembe zoparamula ndi ndarama za nsembe yaucimo sanabwera nazo ku nyumba ya Yehova; nza ansembe izi.
17 Pamenepo Hazaeli mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yace kukwera ku Yerusalemu.
18 Koma Yoasi mfumu ya Yuda: anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yoramu, ndi Ahaziya, makolo ace, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zace zace, ndi golidi yense anampeza pa cuma ca nyumba ya Yehova, ndi ca nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaeli mfumu ya Aramu; motero anabwerera kucoka ku Yerusalemu.
19 Macitidwe ena tsono a Yoasi ndi zonse adazicita sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
20 Ndipo anyamata ace ananyamuka, napangana, nakantha Yoasi ku nyumba ya Milo potsikira ku Silo.
21 Pakuti Yozakara mwana wa Simeati, ndi Yosabadi mwana wa Someri, anyamata ace, anamkantha, nafa iye; ndipo anamuika kwa makolo ace m'mudzi wa Davide; ndi Amaziya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.