1 Pamenepo mfumu inatumiza anthu, namsonkhanitsira akulu onse a Yuda ndi a m'Yerusalemu.
2 Nikwera mfumu kumka ku nyumba ya Yehova, ndi amuna onse a Yuda, ndi onse okhala m'Yerusalemu pamodzi nave, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi anthu onse ang'ono ndi akulu; nawerenga iye m'makutu mwao mau onse a m'buku la cipangano adalipeza m'nyumba ya Yehova.
3 Niima mfumu paciunda, nicita pangano pamaso pa Yehova, kutsata Yehova, ndi kusunga malamulo ace, ndi mboni zace, ndi malemba ace, ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukhazikitsa mau a cipangano colembedwa m'buku ili; ndipo anthu onse anaimiririra panganoli.
4 Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo laciwiri, ndi olindira pakhomo, aturutse m'Kacisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi cifanizo cija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lace kumka nalo ku Beteli.
5 Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m'midzi ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; wo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.
6 Naturutsa cifanizoco m'nyumba ya Yehova kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni; nacitenthera ku mtsinje wa Kidroni, nacipera cikhale pfumbi, naliwaza pfumbi lace pa manda a ana a anthu.
7 Nagamula nyumba za anyamata adama okhala ku nyumba ya Yehova, kumene akazi anaomba nsaru zolenjeka za cifanizoco.
8 Naturutsa ansembe onse m'midzi ya Yuda, nawaipitsira misanje, imene ansembe adafukizapo zonunkhira, kuyambira Geba kufikira Beereseba; napasula misanje ya kuzipata, yokhala polowera pa cipata ca Yoswa kazembe wa mudzi, yokhala ku dzanja lako lamanzere kwa cipata ca mudzi.
9 Koma ansembe a misanje sanakwera kudza ku guwa la nsembe la Yehova ku Yerusalemu; koma anadya mkate wopanda cotupitsa pakati pa abale ao.
10 Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'cigwa ca ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wace wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki.
11 Nacotsanso akavalo amene mafumu a Yuda adapereka kwa dzuwa, polowera nyumba ya Yehova, ku cipinda ca Natani Meleki mdindoyo, cokhala kukhonde; natentha magareta a dzuwa ndi moto.
12 Ndi maguwa a nsembe anali patsindwi pa cipinda cosanja ca Ahazi adawapanga mafumu a Yuda, ndi maguwa a nsembe adawapanga Manase m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova, mfumu inawagumula, niwacotsa komweko, nitaya pfumbi lao ku mtsinje wa Kidroni.
13 Ndipo mfumu inawaipitsira misanje yokhala kum'mawa kwa Yerusalemu, ndiyo ya ku dzanja lamanja la phiri la cionongeko, imene Solomo mfumu ya Israyeli adaimangira Asitoreti conyansa ca Asidoni, ndi Kemosi conyansa ca Moabu, ndi Milikomu conyansa ca ana a Amoni.
14 Nathyolathyola zoimiritsa, nalikha zifanizo, nadzaza pamalo pao ndi mafupa a anthu.
15 Anagumulanso guwa la nsembe linali ku Beteli, ndi msanje adaumanga Yerobiamu mwana wa Nebati wolakwitsa Israyeli uja; guwa la nsembelo, ndi msanje womwe anagumula; natentha msanje, naupondereza ukhale pfumbi, natentha cifanizoco.
16 Ndipo potembenuka Yosiya anaona manda okhalako kuphiri, natumiza anthu naturutsa mafupa kumanda, nawatentha pa guwa la nsembe, kuliipitsa, monga mwa mau a Yehova anawalalikira munthu wa Mulungu wolalikira izi.
17 Anatinso, Cizindikilo ici ndiciona nciani? Namuuza anthu a m'mudziwo, Ndico manda a munthu wa Mulungu anafuma ku Yuda, nalalikira izi mwazicitira guwa la nsembe la ku Beteli.
18 Nati iye, Mlekeni, munthu asakhudze mafupa ace. Naleka iwo mafupa ace akhale pamodzi ndi mafupa a mneneri uja anaturuka m'Samariya.
19 Ndi nyumba zonse zoo mwe za ku misanje yokhala m'midzi ya Samariya, adazimanga mafumu a Israyeli kuutsa nazo mkwiyo wa Yehova, Yosiya anazicotsa, nazicitira monga mwa nchito zonse adazicita ku Beteli.
20 Ndipo anapha ansembe onse a misanje okhalako pa maguwa a nsembe, natentha-mafupa a anthu pamenepo, nabwerera kumka ku Yerusalemu.
21 Ndipo mfumu inalamulira anthu onse, kuti, Mcitireni Yehova Mulungu wanu Paskha, monga mulembedwa m'buku ili la cipangano,
22 Zedi silinacitika Paskha lotere ciyambire masiku a oweruza anaweruza Israyeli, ngakhale m'masiku a mafumu a Israyeli, kapena mafumu a Yuda;
23 koma Paskha ili analicitira Yehova m'Yerusalemu, Yosiya atakhala mfumu zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu.
24 Ndiponso obwebweta, ndi openda, ndi aterafi, ndi mafano, ndi zonyansa zonse zidaoneka m'dziko la Yuda ndi m'Yerusalemu, Yosiya anazicotsa; kuti alimbitse mau a cilamulo olembedwa m'buku adalipeza Hilikiya wansembe m'nyumba ya Yehova.
25 Ndipo asanabadwe iye panalibe mfumu wolingana naye, imene inatembenukira kwa Yehova ndi mtima wace wonse, ndi moyo wace wonse, ndi mphamvu yace yonse, monga mwa cilamulo conse ca Mose; atafa iyeyu sanaukanso wina wolingana naye.
26 Koma Yehova sanakululuka mkwiyo wace waukuru waukali umene adapsa mtima nao pa Yuda, cifukwa ca zoputa zonse Manase adaputa nazo mkwiyo wace.
27 Nati Yehova, Ndidzacotsa Yudanso pamaso panga, monga umo ndinacotsera Israyeli; ndipo ndidzataya mudzi uwu ndidausankha, ndiwo Yerusalemu, ndi nyumba ndidainena, Dzina langa lidzakhala komweko.
28 Macitidwe ena tsono a Yosiya, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
29 Masiku ace Farao-Neko mfumu ya Aigupto anakwerera mfumu ya Asuri ku mtsinje wa Firate; Ddipo mfumu Yosiya anaturuka kuponyana naye, koma anapha Yosiya ku Megido, atamuona.
30 Ndipo anyamata ace anamtengera wakufa m'gareta, nabwera naye ku Yerusalemu kucokera ku Megido, namuika m'manda ace ace. Ndipo anthu a m'dziko anatenga Yoahazi mwana wa Yosiya, namdzoza, namlonga ufumu m'malo mwa atate wace.Yoahazi, Yoyakimu ndi Yoyakini mafumu oipa a Yuda.
31 Yoahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu miyezi itatu m'Yerusalemu ndi dzina la mace ndiye Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
32 Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga umo monse adacita makolo ace.
33 Ndipo Faraoneko anammanga m'Ribila, m'dziko la Hamati; kuti asacite ufumu m'Yerusalemu; nasonkhetsa dzikoli msonkho wa matalente zana limodzi la siliva, ndi talente limodzi la golidi.
34 Ndipo Farao-Neko analonga ufumu Eliyakimu mwana wa Yosiya, m'malo mwa Yosiya atate wace, nasanduliza dzina lace likhale Yoyakimu; koma anapita naye Yoahazi, nafika iye m'Aigupto, nafa komweko.
35 Ndipo Yoyakimu anapereka siliva ndi golidi kwa Farao, koma anasonkhetsa dzikoli lipereke ndalamazi; monga mwa lamulo la Farao anasonkhetsa anthu a m'dziko siliva ndi golidi, yense monga mwa kuyesedwa kwace, kuzipereka kwa Farao-Neko.
36 Yoyakimu anali wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi ndi cimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Zebida mwana wa Pedaya wa Ruma.
37 Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazicita makolo ace.