1 Caka ca makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri ca Yerobiamu mfumu ya Israyeli, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wace.
2 Anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka makumi asanu mphambu ziwiri m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.
3 Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazicita atate wace Amaziya.
4 Komatu sanaicotsa misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.
5 Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yace, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko.
6 Macitidwe ena tsono a Azariya, ndi zonse anazicita, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
7 Nagona Azariya ndi makolo ace, namuika ndi makolo ace m'mudzi wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwace Yotamu mwana wace.
8 Caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu ca Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobiamu anakhala mfumu ya Israyeli m'Samariya miyezi isanu ndi umodzi.
9 Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga adacita makolo ace; sanaleka zolakwa zace za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.
10 Ndipo Salumu mwana wa Yabesi anamcitira ciwembu, namkantha pamaso pa anthu, namupha; nakhala mfumu m'malo mwace.
11 Macitidwe ena tsono a Zekariya, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.
12 Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wacinai adzakhala pa mpando wacifumu wa Israyeli. Ndipo kunatero momwemo.
13 Salumu mwana wa Yabesi analowa ufumu wace caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai ca Uziya mfumu ya Yuda, nakhala mfumu mwezi umodzi m'Samariya.
14 Koma anakwera Menahemu mwana wa Gadi kucokera ku Tiriza, nafika ku Samariya, nakantha Salumu mwana wa Yabesi m'Samariya, namupha; nakhala mfumu m'malo mwace.
15 Macitidwe ena tsono a Salumu ndi ciwembu cace anacicita, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.
16 Pamenepo Menahemu anakantha Tifisa, ndi onse anali m'mwemo, ndi malire ace kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulira pacipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m'mwemo.
17 Caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai ca Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi analowa ufumu wace wa Israyeti, nakhala mfumu zaka khumi m'Samariya.
18 Nacita coipa pamaso pa Yehova masiku ace onse, osaleka zolakwa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.
19 Pamenepo Puli mfumu ya Asuri anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Puli matalente a siliva cikwi cimodzi; kuti dzanja lace likhale naye kukhazikitsa ufumu m'dzanja lace.
20 Ndipo Menahemu anasonkhetsa Israyeli ndaramazi, nasonkhetsa acuma, yense masekeli makumi asanu a siliva: kuti azipereke kwa mfumu ya Asuri. Nabwerera mfumu ya Asuri osakhala m'dzikomo.
21 Macitidwe ena tsono a Menahemu, ndi zonse anazicita, sizinalembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?
22 Nagona Menahemu ndi makolo ace; nakhala mfumu m'malo mwace Pekahiya mwana wace.
23 Caka ca makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri.
24 Nacita coipa pamaso pa Yehova, sanaleka zolakwa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.
25 Ndipo Peka mwana wa Remaliya, kazembe wace, anamcitira ciwembu, nawakantha limodzi mfumu ndi Arigobo ndi Ariye m'Samariya, m'nsanja ya ku nyumba ya mfumu; pamodzi ndi iye panali amuna makumi asanu a Gileadi; ndipo anamupha, nakhala mfumu m'malo mwace.
26 Macitidwe ena tsono a Pekahiya ndi zonse anazicita, taonani zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.
27 Caka ca makumi asanu mphambu ziwiri ca Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya analowa ufumu wace wa Israyeli m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi awiri.
28 Nacita coipa pamaso pa Yehova: osaleka zolakwa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli,
29 Masiku a Peka mfumu ya Israyeli anadza Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, nalanda Ijoni, ndi Abeli-BeteMaaka, ndi Yanoa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Gileadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafitali; nawatenga andende kumka nao ku Asuri.
30 Ndipo Hoseya mwana wa Ela anamcitira ciwembu Peka mwana wa Remaliya, namkantha, namupha, nakhala mfumu m'malo mwace caka ca makumi awiri ca Yotamu mwana wa Uziya.
31 Macitidwe ena tsono a Peka, ndi zonse anazicita, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.
32 Caka caciwiri ca Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israyeli, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wace.
33 Ndiye wa zaka makumi awiri mphambu: zisanu polowa ufumu wace, nakhalamfumu zaka khumi ndi zisanu ndi cimodzi m'Yerusalemu; ndipo dzina la mace ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.
34 Nacita iye zoongoka pamaso pa Yehova; anacita monga mwa zonse anazicita atate; wace Uziya.
35 Komatu sanaicotsa misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. Iye anamanga cipata ca kumtunda ca nyumba ya Yehova.
36 Macitidwe ena tsono a Yotamu, ndi zonse anazicita, sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?
37 Masiku awa Yehova anayamba kutumizira Yuda Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya, amenyane naye.
38 Ndipo anagona Yotamu ndi makolo ace, namuika pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide kholo lace; nakhala mfumu m'malo mwace Ahazi mwana wace.