2 Mafumu 14 BL92

Amaziyamfumu ya Yuda, Yoasi ndi Yerobiamu waciwiri mafumu a Israyeli

1 Caka caciwiri ca Yoasi mwana wa Yoahazi mfumu ya Israyeli, Amaziya mwana wa Yoasi mfumu ya Yuda analowa ufumu wace.

2 Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu; nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai m'Yerusalemu; dzina la mace ndiye Yoadana wa ku Yerusalemu.

3 Ndipo anacita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lace; nacita monga mwa zonse anazicita Yoasi atate wace.

4 Koma misanje sanaicotsa; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.

5 Ndipo kunali, utakhazikika ufumu m'dzanja lace, anakantha anyamata ace amene adakantha mfumu atate wace;

6 koma ana a ambandawo sanawapha, monga mwalembedwa m'buku la cilamulo ca Mose, m'mene adalamulira Yehova, ndi kuti, Atate asaphedwere ana, kapena ana kuphedwera atate; koma yense afere kulak wa kwa iye yekha.

7 Anapha Aedomu m'Cigwa ca Mcere zikwi khumi, nalanda Sela ndi nkhondo, naucha dzina lace Yokiteli mpaka lero lino.

8 Pamenepo Amaziya anatuma mithenga kwa Yoasi mwana wa Yoahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Idzani tionane maso.

9 Natumiza Yoasi mfumu ya Israyeli kwa Amaziya mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebano unatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebano, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wace; ndipo Inapitapo nyama ya kuthengo ya ku Lebano, nipondereza mtungwiwo.

10 Wakanthadi Aedomu, koma mtima wako wakukweza; ulemekezeke, nukhale kwanu; udziutsiranji tsoka, ungagwe iwe ndi Yuda pamodzi nawe;

11 Koma Amaziya sanamvera. Motero anakwera Yoasi mfumu ya Israyeli, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betisemesi, ndiwo wa Yuda.

12 Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israyeli, nathawira yense kuhema kwace.

13 Ndipo Yoasi mfumu ya Israyeli anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yoasi mwana wa Ahaziya, ku Betisemesi, nadza ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira cipata ca Efraimu kufikira cipata ca kungondya, mikono mazana anai.

14 Natenga golidi ndi siliva yense, ndi zotengera zonse anazipeza m'nyumba ya Yehova, ndi ku cuma ca m'nyumba ya mfumu, acikole omwe; nabwera kumka ku Samariya,

15 Macitidwe ena tsono a Yoasi adazicita, ndi mphamvu yace, ndi umo analimbana naye Amaziya mfumu ya Yuda, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

16 Nagona Yoasi ndi makolo ace, namuika m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israyeli; nakhala mfumu m'malo mwace Yerobiamu mwana wace.

17 Ndipo Amaziya mwana wa Yoasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yoasi mwana wa Yoahazi mfumu ya Israyeli, zaka khumi ndi zisanu.

18 Macitidwe ena tsono a Amaziya, kodi sizilembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Yuda?

19 Ndipo anamcitira ciwembu m'Yerusalemu, nathawira iye ku Lakisi; koma anatumiza akumtsata ku Lakisi, namupha komweko.

20 Nabwera naye pa akavalo, namuika ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ace m'mudzi wa Davide.

21 Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wace Amaziya,

22 Anamanga Elati, naubweza kwa Yuda, atagona ndi makolo ace mfumuyo.

23 Caka cakhumi ndi zisanu ca Amaziya mwana wa Yoasi mfumu ya Yuda, Yerobiamu mwana wa Yoasi mfumu ya Israyeli analowa ufumu wace m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi anai mphambu cimodzi.

24 Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, sanaleka zolakwa zonse za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.

25 Anabweza malire a Israyeli kuyambira polowera ku Hamati mpaka nyanja ya kucidikha, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israyeli, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wace Yona mwana wa Amitai mneneriyo, ndiye wa Gati-heferi,

26 Pakuti Yehova anapenya kuti kuzunzika kwao kwa Israyeli nkowawa ndithu; popeza panalibe womangika kapena womasuka, ndipo panalibe womthandiza Israyeli.

27 Ndipo Yehova sadanena kuti adzafafaniza dzina la Israyeli pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobiamu mwana wa Yoasi.

28 Macitidwe ena tsono a Yerobiamu, ndi zonse anazicita, ndi mphamvu yace, umo anacita nkhondo, nabweza kwa Israyeli Damasiko ndi Hamati amene anali a Yuda, sizilembedwa kodi m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli?

29 Ndipo Yerobiamu anagona ndi makolo ace, ndiwo mafumu a Israyeli; nakhala mfumu m'malo mwace Zekariya mwana wace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25