1 ADAMU, Seti, Enosi,
2 Kenani, Mahalaheli, Yaredi,
3 Enoki, Metusela, Lameki,
4 Nowa, Semu, Hamu, ndi Yafeti.
5 Ana a Yafeti: Gomeri, ndi Magogi, ndi Madai, ndi Yavani, ndi Tubala, ndi Meseki, ndi Tirasi.
6 Ndi ana a Gomeri: Asikenazi, Difati, ndi Togarima.
7 Ndi ana a Yavani: Elisa, ndi Tarisisa, Kitimu, ndi Rodanimu.
8 Ana a Hamu: Kusi, ndi Mizraimu, Puti, ndi Kanani.
9 Ndi ana a Kusi: Seba, ndi Havila, ndi Sabita, ndi Rama, ndi Sabteka. Ndi ana a Rama: Seba, ndi Dedani.
10 Ndi Kusi anabala Nimmdi; iye anayamba kukhala wamphamvu pa dziko.
11 Ndi Mizraimu anabala Aludi, ndi Aanami, ndi Alehabi, ndi Anaftuki,
12 ndi Apatrusi, ndi Akasluki, (kumene anafuma Afilisti), ndi Akafitori.
13 Ndi Kanani anabala Zidoni mwana wace woyamba, ndi Heti,
14 ndi Ayebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi,
15 ndi Ahivi, ndi Aariki, ndi Asini,
16 ndi Aarivadi, ndi Azemari, ndi Ahamati.
17 Ana a Semu: Elamu, ndi Asuri, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu, ndi Uzi, ndi Huli, ndi Geteri, ndi Meseki.
18 Ndi Aripakisadi anabala Sela; ndi Sela anabala Eberi.
19 Ndi Eberi anabala ana amuna awiri, dzina la winayo ndiye Pelegi, popeza masiku ace dziko linagawanika; ndi dzina la mbale wace ndiye Yokitani.
20 Ndipo Yokitani anabala Almodadi, ndi Selefi, ndi Hazaramaveti, ndi Yera;
21 ndi Hadoramu, ndi Uzali, ndi Dikila;
22 ndi Ebala, ndi Abimaele, ndi Seba,
23 ndi Ofiri, ndi Havila, ndi Yobabi. Awa onse ndiwo ana a Yokitani.
24 Semu, Aripakisadi, Sela;
25 Eberi, Pelegi, Reu,
26 Serugi, Nahori, Tera;
27 Abramu, (ndiye Abrahamu).
28 Ana a Abrahamu: Isake, ndi Ismayeli.
29 Mibadwo yao ndi awa; woyamba wa Ismayeli Nebayoti; ndi Kedara ndi Adibeli, ndi Mibisamu,
30 Misma, ndi Duma Masa,
31 Hadada, ndi Tema, Nafisi, ndi Kedema. Awa ndi ana a Ismayeli.
32 Ndi ana a Ketura mkazi wamng'ono wa Abrahamu anabala Zimiramu, ndi Yokisani, ndi Medani, ndi Midyani, ndi Isibaki, ndi Sua. Ndi ana a Yokisani: Seba, ndi Dedani.
33 Ndi ana a Midyani: Efa, ndi Eferi, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elidaa. Awa onse ndiwo ana a Ketura.
34 Ndipo Abrahamu anabala Isake. Ana a Isake: Esau, ndi Israyeli.
35 Ana a Esau: Elifazi, Reueli, ndi Yeuzi, ndi Yolamu, ndi Kora.
36 Ana a Elifazi: Teani, ndi Omara, Zefi, ndi Gatamu, Kenazi, ndi Timna, ndi Amaleki.
37 Ana a Reueli: Nahati, Zera, Sama, ndi Miza.
38 Ndi ana a Seiri: Lotani, ndi Sobala, ndi Zibeoni, ndi Ana, ndi Disoni, ndi Ezeri, ndi Disani.
39 Ndi ana a Lotani: Hori, ndi Homamu; ndipo Timna ndiye mlongo wace wa Lotani.
40 Ana a Sobala: Abiani, ndi Manahati, ndi Ebala, Sefi, ndi Oramu. Ndi ana a Zibeoni: Aiya ndi Ana.
41 Mwana wa Ana: Disoni. Ndi ana a Disoni: Hamirani, ndi Esibani, ndi Itrani, ndi Kerani.
42 Ana a Ezeri: Bilani, ndi Zavani, ndi Yakani. Ana a Disani: Uzi, ndi Arani.
43 Mafumu tsono akucita ufumu m'dziko la Edomu, pakalibe mfumu wakucita ufumu pa ana a Israyeli, ndiwo Bela mwana wa Beori; ndi dzina la mudzi wace ndilo Dinaba.
44 Ndipo anafa Bela; ndi Yobabi mwana wa Zera wa ku Bozra anakhala mfumu m'malo mwace.
45 Namwalira Yobabi; ndi Husamu wa ku dziko la Atemani anakhala mfumu m'malo mwace.
46 Namwalira Husamu; ndi Hadada mwana wa Bedadi, amene anakantha Midyani ku thengo la Moabu, anakhala mfumu m'malo mwace; ndi dzina la mudzi wace ndi Aviti.
47 Namwalira Hadada; ndi Samla wa ku Masereka anakhala mfumu m'malo mwace.
48 Namwalira Samla: ndi Sauli wa ku Rehoboti ku nyanja anakhala mfumu m'malo mwace.
49 Namwalira Sauli; ndi Baalahanani mwana wa Akiboro anakhala mfumu m'malo mwace.
50 Namwalira Baalahanani; ndi Hadada anakhala mfumu m'malo mwace; ndipo dzina la mudzi wace ndi Pai; ndi dzina la mkazi wace ndiye Mehetabele mwana wamkazi wa Matradi mwana wamkazi wa Mezahabu.
51 Namwalira Hadada. Ndipo mafumu a Edomu ndiwo mfumu Timna, mfumu Aliya, mfumu Yeteti;
52 mfumu Oholibama, mfumu Bla, mfumu Pimoni;
53 mfumu Kenazi, mfumu Temani, mfumu Mizibara;
54 mfumu Magadieli, mfumu Iramu. Awa ndi mafumu a Edomu.