1 Mbiri 29 BL92

Zopereka zaufulu zomangira Kacisi

1 Mfumu Davide ananenanso kwa khamu lonse, Mulungu wasankha mwana wanga Solomo yekha, ndiye mnyamata ndi wosakhwima; ndipo nchitoyi ndi yaikuru, pakuti cinyumbaci siciri ca munthu, koma ca Yehova Mulungu.

2 Ndi mphamvu yanga yonse tsono ndakonzeratu nyumba ya Mulungu wanga, golidi wa zija zagolidi ndi siliva wa zija zasiliva, ndi mkuwa wa zija zamkuwa, citsulo ca zija zacitsulo, ndi mtengo wa zija zamtengo, miyala yaberulo, ndi miyala yoikika, miyala yokometsera, ndi ya mawanga mawanga, ndi miyala ya mtengo wace ya mitundu mitundu ndi miyala yansangalabwe yocuruka.

3 Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, cuma cangacanga ca golidi ndi siliva ndiri naco ndicipereka ku nyumba ya Mulungu wanga, moenjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo;

4 ndico matalente zikwi zitatu za golidi, golidi wa Ofiri; ndi matalente zikwi zisanu ndi ziwiri a siliva woyengetsa, kumamatiza nazo makoma a nyumbazi;

5 golidi wa zija zagolidi, ndi siliva wa zija zasiliva, ndi za nchito ziri zonse akuzipanga manja a amisiri. Ndani uyo afuna mwini kudzipatulira kwa Yehova lero line?

6 Pamenepo akuru a nyumba za makolo, ndi akuru a mafuko a Israyeli, ndi akuru a zikwi ndi a mazana pamodzi ndi iwo oyang'anira nchito ya mfumu, anapereka mwaufulu,

7 napereka ku utumiki wa nyumba ya Mulungu golidi matalente zikwi zisanu, ndi madariki zikwi khumi; ndi siliva matalente zikwi khumi, ndi mkuwa matalente zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi citsulo matalente zikwi zana limodzi.

8 Ndipo amene anali nayo miyala ya mtengo wace anaipereka ku cuma ca nyumba ya Yehova, mwa dzanja la Yehieli Mgerisoni.

9 Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi cimwemwe cacikuru.

Pemphero la Davide, ndi kumwalira kwace

10 Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israyeli, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.

11 Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi cifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi pa dziko lap ansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.

12 Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo mucita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikuru; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.

13 Motero tsono, Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma.

14 Kama ndine yani, ndi anthu anga ndiwo ayani, kuti tidzakhoza kupereka mwaufulu motere? popeza zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu.

15 Pakuti ife ndife alendo pamaso panu, ndi ogonera, monga makolo athu onse; masiku athu a padziko akunga mthunzi, ndipo palibe kukhalitsa.

16 Yehova Mulungu wathu, zounjikika izi zonse tazikonzeratu kukumangirani Inu nyumba ya dzina lanu loyera zifuma ku dzanja lanu, zonsezi ndi zanu.

17 Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Kama ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu.

18 Yehova Mulungu wa Abrahamu, wa Isake, ndi wa Israyeli makolo athu, musungitse ici kosatha m'cilingaliro ca maganizo a mtima wa anthu anu, nimulunjikitse mitima yao kwanu,

19 nimupatse Solomo mwana wanga mtima wangwiro kusunga malamulo anu, mboni zanu, ndi malemba anu, ndi kucita izi zonse, ndi kumanga cinyumbaci cimene ndakonzeratu mirimo yace,

20 Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.

21 Ndipo anamphera Yehova nsembe, napereka nsembe zopsereza kwa Yehova m'mawa mwace mwa tsiku lija, ndizo ng'ombe cikwi cimodzi, nkhosa zamphongo cikwi cimodzi, ndi ana a nkhosa cikwi cimodzi, pamodzi ndi nsembe zao zothira, ndi nsembe zocuruka za Aisrayeli onse:

22 nadya namwa pamaso pa Mulungu tsiku lomwelo ndi cimwemwe cacikuru. Ndipo analonga ufumu Solomo mwana wa Davide kaciwiri, namdzozera Yehova akhale kalonga, ndi Zadoki akhale wansembe.

23 Momwemo Solomo anakhala pa mpando wacifumu wa Yehova, ndiye mfumu m'malo mwa Davide atate wace, nalemerera, nammvera iye Aisrayeli onse.

24 Ndi akuru onse, ndi amuna amphamvu onse, ndi ana amuna onse omwe a mfumu Davide, anagonjeratu kwa Solomo mfumu.

25 Ndipo Yehova anakuza Solomo kwakukuru pamaso pa Aisrayeli onse, nampatsa ulemerero wacifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Israyeli inali nao wotero.

26 Momwemo Davide mwana wa Jese adakhala mfumu ya Aisrayeli onse.

27 Ndipo nthawi yoti anakhala mfumu ya Israyeli ndiyo zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu m'Hebroni, ndi zaka makumi atatu anakhala mfumu m'Yerusalemu.

28 Nafa atakalamba bwino, wocuruka masiku, zolemera, ndi ulemerero; ndi Solomo mwana wace anakhala mfumu m'malo mwaceo

29 Zocita mfumu Davide tsono, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Samueli mlauli, ndi m'buku la mau a Natani mneneri, ndi m'buku la mau a Gadi mlauli;

30 pamodzi ndi za ufumu wace wonse, ndi mphamvu yace, ndi za nthawizo zidampitira iye, ndi Israyeli, ndimaufumu onse a maiko.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29