1 Mbiri 19 BL92

Davide abwezera cilango kwa Aamoni pa cipongwe cao

1 Ndipo zitatha izi, Nahasi mfumu ya ana a Amoni anamwalira, ndi mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

2 Ndipo Davide anati, Ndidzamcitira zokoma mtima Hanuni mwana wa Nahasi, popeza atate wace anandicitira ine zokoma mtima. Momwemo Davide anatuma mithenga imtonthoze mtima pa atate wace. Pofika anyamata ace a Davide ku dziko la ana a Amoni kwa Hanuni kumtonthoza mtima,

3 akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni, Davide ali kucitira atate wanu ulemu kodi, popeza anakutumizirani otonthoza? sakudzerani kodi anyamata ace kufunafuna, ndi kugubuduza, ndi kuzonda dziko?

4 Ndipo Hanuni anatenga anyamata a Davide, nawameta, nadula malaya ao pakati kufikira m'matako, nawaleka acoke.

5 Pamenepo anamuka ena, namuuza Davide za amunawa. Natumiza iye kukomana nao, pakuti amunawa anacita manyazi kwambiri. Ndipo mfumu inati, Balindani ku Yeriko mpaka zamera ndebvu zanu; zitamera mubwere.

6 Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, Hanuni ndi ana a Amoni anatumiza matalente cikwi cimodzi a siliva, kudzilembera magareta ndi apakavalo ku Mesopotamiya, ndi ku Aramu-maaka, ndi ku Zoba.

7 Momwemo anadzilembera magareta zikwi makumi atatu mphambu ziwiri, ndi mfumu ya Maaka ndi anthu ace; nadza iwo, namanga misasa cakuno ca Medeba. Ana a Amoni omwe anasonkhana m'midzi mwao, nadza kunkhondo.

8 Pamene Davide anamva ici anatuma Yoabu ndi gulu lonse la anthu amphamvu.

9 Ndipo ana a Amoni anaturuka, nandandalitsa nkhondo ku cipata ca mudzi, ndi mafumu adadzawo anali pa okha kuthengo.

10 Pakuona Yoabu tsono kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, anasankha amuna osankhika onse a Israyeli, nawanika ayambane ndi Aaramu.

11 Ndipo anthu otsala anawapereka m'dzanja la Abisai mbale wace; ndipo anadzinika avambane ndi ana a Amoni.

12 Ndipo anati, Akandilaka Aaramu, udzandilanditsa ndiwe; koma akakulaka ana a Amoni, ndidzakulanditsa ndine.

13 Limbika mtima, tilimbikire anthu athu, ndi midzi ya Mulungu wathu; ndipo Yehova acite comkomera.

14 Pamenepo Yoabu ndi anthu anali naye anayandikira pamaso pa Aaramu kulimbana nao, ndipo anawathawa.

15 Ndipo pakuona ana a Amoni kuti adathawa Aaramu, iwo omwe anathawa pamaso pa Abisai mbale wace, nalowa m'mudzi. Pamenepo Yoabu anadza ku Yerusalemu.

16 Ndipo pakuona Aaramu kuti Israyeli anawakantha, anatumiza mithenga, naturuka nao Aaramu akukhala tsidya lija la mtsinjewo; ndi Sofaki kazembe wa khamu la Hadarezeri anawatsogolera.

17 Ndipo anamuuza Davide; namemeza iye Aisrayeli onse, naoloka Yordano, nawadzera, nanika nkhondo ayambane nao. Atandandalitsa nkhondo Davide kuyambana ndi Aaramu, anaponyana naye.

18 Ndipo Aaramu anathawa pamaso pa Israyeli; ndipo Davide anapha Aaramu apamagareta zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi anai; napha Sofaki kazembe wa khamulo.

19 Ndipo pakuona anyamata a Hadarezeri kuti Israyeli anawakantha, anapangana mtendere ndi Davide, namtumikira; ndi Aaramu anakana kuthandizanso ana a Amoni.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29