1 Mbiri 11 BL92

Davide atalowa ufumu alanda Yerusalemu

1 Pamenepo Aisrayeli onse anasonkhana kwa Davide ku Hebroni, ndi kuti, Taonani, ife ndife pfupa lanu, ndi mnofu wanu.

2 Ngakhale kale lomwe, pokhala mfumu Sauliyo, woturuka ndi kulowa nao Aisrayeli ndinu; ndipo Yehova Mulungu wanu anati kwa inu, Uzidyetsa anthu anga Aisrayeli, nukhale mtsogoleri wa anthu anga Israyeli.

3 Akuru onse omwe a Israyeli anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide akhale mfumu ya Israyeli monga mwa mau a Yehova, ndi lizanja la Samueli.

4 Namuka Davide ndi Aisrayeli onse naye ku Yerusalemu, ndiwo Yebusi; ndipo Ayebusi nzika za m'dziko zinali komweko.

5 Ndipo nzika za m'Yebusi zinati kwa Davide, Sungalowe muno. Koma Davide analanda linga la Ziyoni, ndiwo mudzi wa Davide.

6 Nati Davide, Ali yense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yoabu mwana wa Zeruya, nakhala mkuru iyeyu.

7 Ndipo Davide anakhala m'lingamo; cifukwa cace analicha mudzi wa Davide.

8 Ndipo anamanga mudzi pozungulira pace, kuyambira ku Milo ndi pozungulira pace; ndi Yoabu anakonzanso potsala pa mudzi.

9 Ndipo Davide anakula-kulabe, pakuti Yehova wa makamu anali naye.

Amphamvu a Davide

10 Akuru a amphamvu aja Davide anali nao akulimbika pamodzi naye m'ufumu wace, pamodzi ndi Aisrayeli onse, kumlonga ufumu, monga mwa mau a Yehova akunena za Israyeli, ndi awa.

11 Kuwerenga kwa amphamvu aja Davide anali nao ndi uku: Yasobeamu mwana wa Mhakimoni, mkuru wa makumi atatu aja, anasamulira mazana atatu mkondo wace, nawapha nthawi imodzi.

12 Ndi pambuyo pace Eleazara mwana wa Dodo M-ahohi, ndiye mmodzi wa atatu aja amphamvu.

13 Anali pamodzi ndi Da vide ku Pasidamimu muja; Afilisti anasonkhanako kunkhondo kumene kunali munda wodzala ndi barele; ndipo anthu anathawa pamaso pa Afilisti.

14 Koma anadziimika pakati pa munda, naulanditsa, nakantha Afilisti; m'mwemo anawapulumutsa Yehova ndi cipulumutso cacikuru.

15 Ndipo atatu a akuru makumi atatu anatsikira kuthanthwe kwa Davide, ku phanga la Adulamu; ndi nkhondo ya Afilisti idamanga misasa m'cigwa ca Refaimu.

16 Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la askari linali ku Betelehemu.

17 Ndipo Davide analakalaka, nati, Ha! mwenzi wina atandimwetsa madzi a m'citsime ca ku Betelehemu ciri kucipata,

18 Napyola atatuwo misasa ya Afilish natunga madzi ku citsime ca ku Betelehemu ciri kucipata, nabwera nao kwa Davide; koma Davide anakana kumwako, koma anawathirira kwa Yehova;

19 nati, Pali Mulungu wanga, kukhale kutali kwa ine kucita ici. Ngati ndidzamwa mwazi wa anthu awa? Akadataya moyo wao, inde akadataya moyo wao, pakukatenga madziwa. M'mwemo sanafuna kuwamwa. Izi anazicita atatu amphamvuwa.

20 Ndipo Abisai mbale wa Yoabu, ndiye wamkuru wa atatuwa; pakuti anasamulira mazana atatu mkondo wace, nawapha, namveka dzina pakati pa atatuwa.

21 Mwa atatuwa iye anali waulemu woposa awiriwa, nasanduka mkuru wao; koma sanafikana nao atatu oyamba aja.

22 Benaya mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi ya ku Kabzeeli, wocita zazikuru, anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Moabu; anatsikanso, napha mkango m'kati mwa dzenje nyengo ya cipale cofewa.

23 Anaphanso M-aigupto munthu wamkuru, msinkhu wace mikono isanu, ndi m'dzanja la M-aigupto munali mkondo ngati mtanda woombera nsaru; ndipo anamtsikira ndi ndodo, nakwatula mkondo m'dzanja la M-aigupto, namupha ndi mkondo wace womwe.

24 Izi anazicita Benaya mwana wa Yehoyada, namveka dzina mwa atatu amphamvuwo.

25 Taonani, anali wa ulemu woposa makumi atatuwo, koma sanafikana atatu oyamba aja; ndipo Davide anamuika mkuru wa olindirira ace.

26 Ndipo amphamvuwo a magulu a nkhondo ndiwo Asaheli mbale wa Yoabu, Elanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,

27 Samoti Mharori, Helezi Mpeloni,

28 Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekoi, Abiezeri wa ku Anatoti,

29 Sibekai Mhusati, liai M-ahohi,

30 Maharai Mnetofati, Heledi mwana wa Bana Mnetofati,

31 Itai mwana wa Ribai wa Gibeya wa ana a Benjamini, Benaya Mpiratoni,

32 Horai wa ku mitsinje ya Gaasi, Abiyeli M-ariba,

33 Azmaveti Mbaharumi, Eliaba Mshaliboni;

34 ana a Hasemu Mgizoni; Yonatani mwana wa Sage Mharari,

35 Ahiamu mwana wa Sakari Mharari, Elifali mwana wa Uri,

36 Heferi Mmekerati, Ahiya Mpeloni,

37 Hezro wa ku Karimeli, Naarai mwana wa Ezbai,

38 Yoeli mbale wa Natani, Mibari mwana wa Hagiri,

39 Zeleki M-amoni, Naharai Mberoti wonyamula zida za Yoabu mwana wa Zeruya,

40 Ira M-itiri, Garebi M-itiri,

41 Uriya Mhiti, Zabadi mwana wa Alai,

42 Adina mwana wa Siza Mrubeni mkuru wa Arubeni, ndi makumi atatu pamodzi naye,

43 Hanani mwana wa Maaka, ndi Yosafati Mmitini,

44 Uziya M-asterati, Sama ndi Yeieli ana a Hotamu wa ku Aroeri,

45 Yedyaeli mwana wa Simri, ndi Yoha mbale wace Mtizi,

46 Elieli Mmahavi, ndi Yeribai ndi Yosaviya ana a Elinaamu, ndi Itima Mmoabu,

47 Elieli, ndi Obedi, ndi Yasiyeli Mmezobai.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29