1 Ndipo magawidwe a ana a Aroni ndi awa. Ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.
2 Koma Nadabu ndi Abihu anafa, atate wao akali ndi moyo, opanda ana; momwemo Eleazara ndi ltamara anacita nchito ya nsembe.
3 Ndipo Davide pamodzi ndi Zadoki wa ana a Eleazara, ndi Ahimeleke wa ana a Itamara, anawagawa, monga mwa malongosoledwe ao m'utumiki wao.
4 Ndipo anapeza kuti amuna akuru a ana a Eleazara anacuruka, a ana a Itamara anacepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akuru a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu.
5 Ndipo anawagawa ndi maere, awa ndi aja; pakuti panali akalonga a malo opatulika, ndi akalonga a kwa Mulungu, a ana a Eleazara ndi a ana a Itamara omwe.
6 Ndi Semaya mwana wa Netaneli mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleke mwana wa Abyatara, a akuru a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lace ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara.
7 Ndipo maere oyamba anamgwera Yehoyaribu, waciwiri Yedaya,
8 wacitatu Harimu, wacinai Seorimu,
9 wacisanu Malikiya, wacisanu ndi cimodzi Miyamini,
10 wacisanu ndi ciwiri Hakozi, wacisanu ndi citatu Abiya,
11 wacisanu ndi cinai Yesuwa, wakhumi Sekaniya,
12 wakhumi ndi cimodzi Eliyasibu, wakhumi ndi ciwiri Yakimu,
13 wakhumi ndi citatu Hupa, wakhumi ndi cinai Yesebeabu,
14 wakhumi ndi cisanu Biliga, wakhumi ndi cisanu ndi cimodzi Imeri,
15 wakhumi ndi cisanu ndi ciwiri Heziri, wakhumi ndi cisanu ndi citatu Hapizezi,
16 wakhumi ndi cisanu ndi cinai Petahiya, wa makumi awiri Yehezikeli,
17 wa makumi awiri ndi cimodzi Yakini, wa makumi awiri ndi ciwiri Gamuli,
18 wa makumi awiri ndi citatu Delaya, wa makumi awiri ndi cinai Miziya.
19 Awa ndi malongosoledwe ao m'utumiki wao kulowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa ciweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu wa Israyeli anamlamulira.
20 Ndipo wa ana otsala a Levi: wa ana a Amiramu, Subaeli; wa ana a Subaeli, Yedeya.
21 Wa Rehabiya: wa ana a Rehabiya, mkuru ndi Isiya.
22 Wa Aizari: Selomoti; wa ana a Selomoti, Yahati.
23 Ndi wa ana a Hebroni: mkuru ndi Yeriya, waciwiri Amariya, wacitatu Yahazieli, wacinai Yekameamu.
24 Wa ana a Uziyeli, Mika; wa ana a Mika, Samiri.
25 Mbale wa Mika, Isiya; a ana a Isiya, Zekariya,
26 Ana a Merari: Mali ndi Musi; mwana wa Yaziya, Beno.
27 Ana a Merari: wa Yaziya, Beno, ndi Sohamu, ndi Sakuri, ndi Ibri.
28 Wa Mali: Eleazara, ndiye wopanda ana.
29 Wa Kisi: mwana wa Kisi, Yerameli.
30 Ndi ana a Musi: Mali, ndi Ederi, ndi Yerimoti, Awa ndi ana a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao.
31 Awanso anacita maere monga abale ao ana a Aroni, pamaso pa Davide mfumu, ndi Zadoki, ndi Ahimeleki, ndi akuru a nyumba za makolo za ansembe ndi Alevi; mkuru wa nyumba za makolo monga mng'ono wace.