1 Mbiri 2 BL92

Ana a Israyeli, adzukulu a Yuda

1 Ana a Israyeli ndi awa: Rubeni, Simeoni, Levi, ndi Yuda, Isakara, ndi Zebuluni,

2 Dani, Yosefe, ndi Benjamini, Nafitali, Gadi, ndi Aseri.

3 Ana a Yuda ndiwo Eri, ndi Onani, ndi Sela; Batisua Mkanani anambalira atatu amenewa. Koma Eri mwana woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova, ndi iye anamupha.

4 Ndi Tamari mpongozi wace anambalira Perezi ndi Zera. Ana amuna onse a Yuda ndiwo asanu.

5 Ana a Perezi: Hezironi, ndi Hamuli.

6 Ndi ana a Zera: Zimri, ndi Etani, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Dara; onse pamodzi ndi asanu.

7 Ndi ana a Karmi: Akari wobvuta Israyeliyo, amene analakwira coperekedwa ciperekereco.

8 Ndi mwana wa Etani: Azariya.

9 Ndi ana a Hezironi anambadwirawo: Yerameli, ndi Ramu, ndi Kelubai.

10 Ndi Ramu anabala Aminadabu; ndi Aminadabu anabala Nasoni kalonga wa ana a Yuda;

11 ndi Nasoni anabala Salima, ndi Salima anabala Boazi,

12 ndi Boazi anabala Obedi, ndi Obedi anabala Jese,

13 ndi Jese anabala mwana wace wamwamuna woyamba Eliabu, ndi Abinadabu waciwiri, ndi Simeya wacitatu,

14 Netaneli wacinai, Radai wacisanu,

15 Ozemu wacisanu ndi cimodzi, Davide wacisanu ndi ciwiri;

16 ndi alongo ao ndiwo Zeruya ndi Abigaili. Ndi ana a Zeruya: Abisai ndi Yoabu, ndi Asaheli; atatu.

17 Ndi Abigaili anabala Amasa; ndi atate wa Amasa ndiye Yeteri M-ismayeli.

18 Ndi Kalebi mwana wa Hezroni anabala ana ndi Azuba mkazi wace, ndi Yerioti; ndipo ana ace ndiwo Yeseri, ndi Sobabu, ndi Aridoni.

19 Namwalira Azuba, ndi Kalebi anadzitengera Efrati, amene anambalira Huri.

20 Ndi Huri anabala Uri, ndi Uri anabala Bezaleli.

21 Ndipo pambuyo pace Hezroni analowa kwa mwana wamkazi wa Makiri atate wa Gileadi, amene anamtenga akhale mkazi wace, pokhala wa zaka makumi asanu ndi Gmodzi mwamunayo; ndipo mkaziyo anambalira Segubu.

22 Ndi Segubu anabala Yairi, amene anali nayo midzi makumi awiri mphambu itatu m'dziko la Gileadi.

23 Ndi Gesuri ndi Aramu analanda midzi ya Yairi, pamodzi ndi Kenati ndi miraga yace; ndiyo midzi makumi asanu ndi limodzi. Iwo onse ndiwo ana a Makiri atate wa Gileadi.

24 Ndipo atafa Hezroni m'Kalebi-Efrata, Abiya mkazi wa Hezroni anambalira Asini atate wa Tekoa.

25 Ndi ana a Yerameli mwana woyamba wa Hezroni ndiwo: woyamba Ramu, ndi Buna, ndi Oreni, ndi Ozemu, ndi Ahiya.

26 Ndipo Yerameli anali naye mkazi wina dzina lace ndiye Atara, ndiye mace wa Onamu.

27 Ndipo ana a Ramu mwana woyamba wa Yerameli ndiwo Maazi, ndi Yamini, ndi Ekeri.

28 Ndi ana a Onamu ndiwo Samai, ndi Yada; ndi ana a Samai: Nadabu, ndi Abisuri.

29 Ndipo dzina la mkazi wa Abisuri ndiye Abihaili; ndipo anambalira Abani, ndi Molidi.

30 Ndi ana a Nadabu: Seledi ndi Apaimu; koma Seledi anamwalira wopanda ana.

31 Ndi mwana wa Apaimu: lsi. Ndi mwana wa lsi: Sesani. Ndi mwana wa Sesani: Alai.

32 Ndi ana a Yada mbale wa Samai: Yeteri, ndi Yonatani; namwalira: Yeteri wopanda ana.

33 Ndi ana a, Yonatani: Peleti, ndi Zaza. Ndiwo ana a Yerameli.

34 Ndipo Sesani analibe ana amuna, koma ana akazi. Ndi Sesani anali naye mnyamata M-aigupto dzina lace ndiye Yara.

35 Ndipo Sesani anampatsa Yara mnyamata wace mwana wace wamkazi akhale mkazi wace, ndipo anambalira Atai.

36 Ndipo Atai anabala Natani, ndi Natani anabala Zabadi,

37 ndi Zabadi anabala Efilali, ndi Efilali anabala Obedi,

38 ndi Obedi anabala Yehu, ndi Yehu anabala Azariya,

39 ndi Azariya anabala Helezi, ndi Helezi anabala Eleasa,

40 ndi Eleasa anabala Sismai, ndi Sismai anabala Salumu,

41 ndi Salumu anabala Yekamiya, ndi Yekamiya anabala Elisama.

42 Ndi ana a Kalebi mbale wa Yerameli ndiwo Mesa mwana wace woyamba, ndiye atate wa Zifi; ndi ana a Maresa atate wa Hebroni.

43 Ndi ana a Hebroni: Kora, ndi Tapuwa, ndi Rekemu, ndi Sema.

44 Ndi Sema anabala Rahamu atate wa Yorikeamu, ndi Rekemu anabala Samai.

45 Ndi mwana wa Samai ndiye Maoni; ndipo Maoni ndiye atate wa Betizuri.

46 Ndi Efa mkazi wamng'ono wa Kalebi anabala Harani, ndi Moza, ndi Gazezi; ndi Harani anabala Gazezi.

47 Ndi ana a Yadai: Regemu, ndi Yotamu, ndi Gesam, ndi Peleti, ndi Efa, ndi Safa.

48 Maka mkazi wamng'ono wa Kalebi anabala Seberi, ndi Tirana.

49 Iyeyu anabalanso Safa atate wa Madimana, Seva atate wa Makibena, ndi atate wa Gibeya; ndi mwana wamkazi wa Kalebi ndiye Akisa.

50 Ana a Kalebi ndi awa: mwana wa Huri, mwana woyamba wa Efrata, Sobali atate wa Kiriate Yearimu.

51 Salma atate wa Betelehemu, Harefi atate wa Betigaderi.

52 Ndipo Sobali atate wa Kiriati-Yearimu anali ndi ana: Haroe, ndi Hazi Hamenukoti.

53 Ndi mabanja a Kiriati-Yearimu: Aitiri, ndi Aputi, ndi Asumati, ndi Amisrai; Aforati ndi Aestaoli anafuma kwa iwowa.

54 Ana a Salma: Betelehemu, ndi Anetofati, Atroti Beti Yoabu, ndi Hazi Hamanahati, ndi Azori.

55 Ndi mabanja a alembi okhala ku Yabezi: Atirati, Asimeati, Asukati. Iwo ndiwo Akeni ofuma ku Hamati, kholo la nyumba ya Rekabu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29