1 Mbiri 23 BL92

Davide alonga Solomo m'ufumu, nakonza cigawo ca Alevi

1 Atakalamba tsono Davide ndi kucuruka masiku, iye analonga mwana wace Solomo akhale mfumu ya Israyeli.

2 Ndipo anasonkhanitsa akuru onse a Israyeli, ndi ansembe ndi Alevi.

3 Ndipo anawerengedwa Alevi oyambira zaka makumi atatu ndi mphambu, ndipo ciwerengo cao kuwawerenga mmodzi mmodzi ndico amuna zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu.

4 A iwowa zikwi makumi awiri mphambu zinai anayang'anira nchito ya nyumba ya Yehova, ndi zikwi zisanu ndi cimodzi ndiwo akapitao ndi oweruza,

5 ndi zikwi zinai odikira; ndi zikwi zinai analemekeza Yehova ndi zoyimbira zimene ndinazipanga, anati Davide, kuti alemekeze nazo.

6 Ndipo Davide anawagawa magawo monga mwa ana a Levi: Gerisomu, Kohati, ndi Merari.

7 A Agerisomu: Ladani ndi Simeyi,

8 Ana a Ladani: wamkuru ndi Yehieli, ndi Zethamu, ndi Yoeli; atatu.

9 Ana a Simeyi: Selomoti, ndi Hazieli, ndi Hanani; atatu. Ndiwo akuru a nyumba za makolo a Ladani.

10 Ndi ana a Simeyi: Yahati, Zina, ndi Yeusi, ndi Beriya. Awa anai ndiwo ana a Simeyi.

11 Wamkuru wa iwo ndi Yahati, mnzace ndi Ziza; koma Yeusi ndi Beriya analibe ana ambiri, potero anakhala nyumba ya kholo yowerengedwa pamodzi.

12 Ana a Kohati: Amiramu, Izara, Hebroni, ndi Uzieli; anai.

13 Ana a Amiramu: Aroni, ndi Mose; ndipo Aroni anasankhidwa kuti apatule zopatulikitsa, iye ndi ana ace, kosalekeza, kufukiza pamaso pa Yehova, kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lace kosatha.

14 Kunena za Mose munthu wa Mulunguyo, ana ace anaehulidwa mwa pfuko la Levi.

15 Ana a Mose: Gerisomu, ndi Eliezeri.

16 Ana a Gerisomu: wamkuru ndi Sebuyeli.

17 Ndi ana a Eliezeri: wamkuru ndi Rehabiya. Ndipo Eliezeri analibe ana ena, koma ana a Rehabiya anacuruka kwambiri.

18 Ana a Izara: wamkuru ndiye Selomiti.

19 Ana a Hebroni: wamkuru ndi Yeriya, waciwiri ndi Amariya, wacitatu ndi Yehazieli, wacinai ndi Yekameamu,

20 Ana a Uzieli: wamkuru ndi Mika, waciwiri ndi Isiya.

21 Ana a Merari: Mali ndi Musi. Ndi ana a Mali: Eleazara ndi Kisi.

22 Nafa Eleazara wopanda ana amuna, koma ana akazi ndiwo; ndi asuweni ao ana a Kisi anawatenga akhale akazi ao.

23 Ana a Musi: Mali, ndi Ederi, ndi Yeremoti; atatu.

24 Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akuru a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa ciwerengo ca maina mmodzi mmodzi, akugwira nchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.

25 Pakuti Davide anati, Yehova Mulungu wa Israyeli wapumulitsa anthu ace; ndipo akhala m'Yerusalemu kosatha;

26 ndiponso Alevi asasenzenso kacisi ndi zipangizo zace zonse za utumiki wace.

27 Pakuti monga mwa mau ace otsiriza a Davide, ana a Levi anawerengedwa kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.

28 Pakuti nchito yao ndiyo kuimirira ana a Aroni, atumikire m'nyumba ya Yehova, m'mabwalo, ndi kuzipinda, ndi kuyeretsa zopatulika zonse; inde nchito za utumiki wa nyumba ya Mulungu;

29 ya mkate woonekera womwe, ndi ya ufa wosalala wa nsembe yaufa, ndi ya timitanda taphanthiphanthi topanda cotupitsa, ndi ya ciwaya, ndi yakukazinga, ndi ya miyeso iri yonse;

30 ndi kuimirira m'mawa ndi m'mawa kuyamika ndi kulemekeza Yehova, momwemonso madzulo;

31 ndi kupereka nsembe zopsereza zonse kwa Yehova, za masabata, za pokhala mwezi, za nyengo zoikika, kuwerenga kwace monga mwa lemba lace, kosalekeza pamaso pa Yehova;

32 ndi kuti asunge udikiro wa cihema cokomanako, ndi udikiro wa malo opatulika ndi udikiro wa ana a Aroni abale ao, potumikira nyumba ya Yehova.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29