1 A magawidwe a odikira a Akora: Meselemiya mwana wa Kore wa ana a Asafu.
2 Ndipo Meselemiya anali ndi ana, woyamba Zekariya, waciwiri Yedyaeli, wacitatu Zebadiya, wacinai Yatiniyeli,
3 wacisanu Elamu, wacisanu ndi cimodzi Yohanana, wacisanu ndi ciwiri Elihunai.
4 Ndipo Obedi Edomu anali nao ana, woyamba Semaya, waciwiri Yozabadi, wacitatu Yowa, wacinai Sakara, wacisanu Netaneli,
5 wacisanu ndi cimodzi Amiyeli, wacisanu ndi ciwiri Isakara, wacisanu ndi citatu Peuletai; pakuti Mulungu adamdalitsa.
6 Kwa Semaya mwana wace yemwe kunabadwa ana, akulamulira nyumba ya atate wao; pakuti anali ngwazi zamphamvu.
7 Ana a Semaya: Otini, ndi Refaeli, ndi Obedi, Elzabadi, amene abale ao ndiwo odziwa mphamvu, Elihu, ndi Semakiya.
8 Onsewa ndiwo a ana a Obedi Edomu; iwo ndi ana ao, ndi abale ao, anthu odziwa mphamvu yakutumikira, makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri a Obedi Edomu.
9 Ndi Meselemiya anali ndi ana, ndi abale odziwa mphamvu khumi mphambu asanu ndi atatu.
10 Hosa yemwe wa ana a Merari anali ndi ana, wamkuru ndi Simri; pakuti ngakhale sanali wobadwa woyamba, atate wace anamuyesa wamkuru;
11 waciwiri Hilikiya, wacitatu Tebaliya, wacinai Zekariya; ana ndi abale onse a Hosa ndiwo khumi ndi atatu.
12 Mwa iwowa munali magawidwe a odikira, mwa akulu a amuna akucita udikiro wao, monga abale ao, kutumikira m'nyumba ya Yehova.
13 Ndipo anacita maere ang'ono ndi akuru, monga mwa nyumba za makolo ao, kucitira zipata zonse.
14 Ndi maere a kum'mawa anagwera Selemiya. Ndipo anacitira maere Zekariya mwana wace, phungu wanzeru, ndi maere anamgwera kumpoto;
15 Obedi Edomu kumwela, ndi ana ace nyumba ya akatundu.
16 Supimu ndi Hosa kumadzulo, ku cipata ca Saleketi, ku mseu wokwerapo, udikiro pandunji pa udikiro.
17 Kum'mawa kunali Alevi asanu ndi mmodzi, kumpoto anai tsiku ndi tsiku, kumwela anai tsiku ndi tsiku, ndi a nyumba ya akatundu awiri ndi awiri.
18 Ku Parabara kumadzulo anai kumseu, ndi awiri ku Parabara.
19 Awa ndi magawidwe a odikira; a ana a Akora, ndi a ana a Merari.
20 Ndipo wa Alevi, Ahiya anayang'anira cuma ca nyumba ya Mulungu, ndi cuma ca zopatulika.
21 Ana a Ladani: ana a Ladani a Agerisoni, akuru a nyumba za makolo a Ladani Mgerisoni, Yehieli.
22 Ana a Yehieli: Zetamu ndi Yoeli mbale wace, oyang'anira cuma ca nyumba ya Yehova.
23 A Amirami, a Aizari, a Ahebroni, a Auziyeli;
24 ndi Sebueli mwana wa Gerisomu, mwana wa Mose, ndiye mkuru woyang'anira zuma.
25 Ndi abale ace a Eliezeri: Rehabiya mwana wace, ndi Yesava mwana wace ndi Yorramu mwana wace, ndi Zikiri mwana wace, ndi Selomoti mwana wace.
26 Selomoti amene ndi abale ace anayang'anira cuma conse ca zinthu zopatulika, zimene Davide mfumu ndi akuru a nyumba za akulu, akuru a zikwi ndi mazana, adazipatula.
27 Kutenga pa zofunkha kunkhondo, anapatulako kukonzera nyumba ya Yehova.
28 Ndipo zonse adazipatula Samueli mlauli, ndi Sauli mwana wa Kisi, ndi Abineri mwana wa Neri, ndi Yoabu mwana wa Zeruya; ali yense anapatula kanthu kali konse, anazisunga Selomoti ndi abale ace.
29 A Aizara: Kenaniya ndi ana ace anacita nchito ya pabwalo ya Israyeli, akapitao ndi oweruza mirandu.
30 A Ahebroni: Hasabiya ndi abale ace odziwa mphamvu cikwi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri anayang'anira Israyeli tsidya lino la Yordano kumadzulo, kuyang'anira nchito yonse ya Yehova, ndi kutumikira mfumu.
31 Yeriya ndiye mkuru wa Ahebroni, wa Ahebroni monga mwa mibadwo ya nyumba za makolo. Caka ca makumi anai ca ufumu wa Davide anafunafuna, napeza mwa iwowa ngwazi zamphamvu ku Yazeri wa ku Gileadi.
32 Ndi abale ace ngwazi ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri, akuru a nyumba za makolo, amene mfumu Davide anaika akhale oyang'anira a Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, pa zinthu zonse za Mulungu ndi zinthu za mfumu.