1 Ndipo Davide anadzimangira nyumba m'mudzi mwace, nakonzeratu malo likasa la Mulungu, naliutsira hema.
2 Pamenepo Davide anati, Sayenera ena kusenza likasa la Mulungu koma Alevi ndiwo; pakuti Yehova anawasankha iwo kusenza likasa la Mulungu, ndi kumtumikira iye kosatha.
3 Ndipo Davide anasonkhanitsira Aisrayeli onse ku Yerusalemu, akwere nalo likasa la Yehova kumalo kwace adalikonzera.
4 Ndipo Davide anasonkhanitsa ana a Aroni ndi Alevi;
5 a ana a Kohati, Urieli mkuru wao, ndi abale ace zana limodzi mphambu makumi awiri;
6 a ana a Merari, Adaya mkuru wao, ndi abale ace mazana awiri mphambu makumi awiri;
7 a ana a Gerisomu, Yoeli mkuru wao, ndi abale ace zana limodzi mphambu makumi atatu;
8 a ana a Elizafana, Semaya mkuru wao, ndi abale ace mazana awiri;
9 a ana a Hebroni, Elieli mkuru wao, ndi abale ace makumi asanu ndi atatu;
10 a ana a Uzieli, Aminadabu mkuru wao, ndi abale ace zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.
11 Ndipo anaitana Zadoki ndi Abyatara ansembe, ndi Alevi Urieli, Asaya, ndi Yoeli, Semaya, ndi Elieli, ndi Aminadabu, nanena nao,
12 Inu ndinu akuru a nyumba za makolo a Alevi, mudzipatule inu ndi abale anu omwe, kuti mukatenge ndi kukwera nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israyeli ku malo ndalikonzera.
13 Pakuti, cifukwa ca kusalinyamula inu poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anacita cotipasula, popeza sitinamfunafuma Iye monga mwa ciweruzo.
14 Momwemo ansembe ndi Alevi anadzipatula kuti akwere nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israyeli.
15 Ndipo ana a Alevi anasenza likasa la Mulungu pa mapewa ao, mphiko ziri m'mwemo, monga Mose anawauza, monga mwa mau a Yehova.
16 Ndipo Davide ananena ndi mkuru wa Alevi kuti aike abale ao oyimbawo ndi zoyimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi cimwemwe.
17 Ndipo Alevi anaika Hemani mwana wa Yoeli, ndi a abale ace Asafu mwana wa Berekiya, ndi a ana a Merari, abale ao, Etani mwana wa Kusaya;
18 ndi pamodzi nao abale ao a kulongosola kwaciwiri, Zekariya, Beni, ndi Yaazieli, ndi Semiramoti, ndi Yehieli, ndi Uni, Bliabu, ndi Benaya, ndi Maaseya, ndi Matitiya, ndi Blifelehu, ndi Mikineya, ndi Obedi Bdomu, ndi Yeieli, ndikirawo.
19 Oyimba tsono: Hemani, Asafu, ndi Btani, anayimba ndi nsanje zamkuwa;
20 ndi Zekariya, ndi Azieli, ndi Semiramod, ndi Yehieli, ndi Uni, ndi Bliabu, ndi Maaseya, ndi Benaya, ndi zisakasa kuyimbira mwa Alimoti;
21 ndi Matitiya, ndi Elifelehu, ndi Mikeya, ndi Obedi Edomu, ndi Yeieli, ndi Azaziya, ndi azeze akuyimbira mwa Seminiti, kutsogolera mayimbidwe.
22 Ndi Kenaniya mkuru wa Alevi anayang'anira kusenzako; anawalangiza za kusenza, pakuti anali waluso.
23 Ndi Berekiya ndi Elikana anali odikira likasa.
24 Ndi Sebaniya, ndi Yosafati, ndi Netaneli, ndi Amasai, ndi Zekariya, ndi Benaya, ndi Eliezere, ansembe, analiza malipenga ku likasa la Mulungu; ndi Obedi Edomu ndi Yehiya anali odikira a likasa.
25 Momwemo Davide, ndi akuru akuru a Israyeli, ndi atsogoleri a zikwi, anamuka kukwera nalo likasa la cipangano la Yehova, kucokera ku nyumba ya Obedi Edomu mokondwera.
26 Ndipo popeza Mulungu anathandiza Alevi akusenza likasa la cipangano la Yehova, iwo anapha nsembe ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri.
27 Ndipo Davide anabvala maraya abafuta, ndi Alevi onse akunyamula likasa, ndi oyimba, ndi Kenaniya woyang'anira kusenzaku, pamodzi ndi oyimba; Davide anabvalanso efodi wabafuta.
28 Momwemo Aisrayeli onse anakwera nalo likasa la cipangano la Yehova ndi kupfuula, ndi kumveka kwa lipenga, ndi mphalasa, ndi nsanje zomveketsa, ndi zisakasa, ndi azeze.
29 Ndipo polowa likasa la cipangano la Yehova m'mudzi wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli anasuzumira pazenera, naona mfumu Davide alikutumphatumpha ndi kusewera; ndipo anampeputsa mumtima mwace.