1 Mbiri 16 BL92

1 Ndipo analowa nalo likasa la Mulungu, nalgka pakati pa hemalo Davide adaliutsira; ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Mulungu.

2 Ndipo atatha Davide kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika, anadalitsa anthu m'dzina la Yehova.

3 Nagwira ali yense wa Israyeli, wamwamuna ndi wamkazi, yense mtanda wa mkate, ndi nthuli ya nyama, ndi ncinci ya mphesa zouma.

4 Ndipo anaika Alevi ena atumikire ku likasa la Yehova, nalalikire, nayamike, nalemekeze Yehova Mulungu wa Israyeli.

5 Asafu ndiye mkuru wao, ndi otsatana naye Zekariya, Yeieli, ndi Semiramoti, ndi Yehieli, ndi Matitiya, ndi Eliabu, ndi Benaya, ndi Obedi Edomu, ndi Yeieli, ndi zisakasa ndi azeze; koma Asafu ndi nsanje zomvekatu;

6 ndi Benaya ndi Yahazieli ansembe ndi malipenga kosalekeza, ku likasa la cipangano la Mulungu.

Salmo la Davide

7 Tsiku limenelo tsono Davide anayamba kuwapatsa nyimbo ya kuyamika nayo Yehova; ocita ndiwo Asafu ndi abale ace.

8 Yamikani Yehova, itanani dzina lace;Bukitsani mwa mitundu ya anthu zocita iye.

9 Myimbireni, myimbireni zomlemekeza;Fotokozerani zodabwiza zace zonse.

10 Mudzitamandire ndi dzina lace lopatulika;Mitima yao ya iwo ofuna Yehova ikondwere.

11 Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yace;Funani nkhope yace nthawi zonse.

12 Kumbukilani zodabwiza zace adazicita,Zizindikilo zace, ndi maweruzo a pakamwa pace;

13 Inu mbeu ya Israyeli mtumiki wace,Inu ana a Yakobo, osankhika ace.

14 Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;Maweruzo ace akhala pa dziko lonse lapansi,

15 Kumbukilani cipangano cace kosatha,Mauwo anawalamulira mibadwo zikwi;

16 Cipanganoco anapangana ndi Abrahamu,Ndi lumbiro lace ndi Isake;

17 Ndipo anacitsimikizirakwa Yakobo cikhale malemba,Cikhale cipangano cosatha kwa Israyeli;

18 Ndi kunena kuti, Ndidzakupatsa iwe dziko la Kanani,Gawo la colandira cako;

19 Pokhala inu anthu owerengeka,Inde anthu pang'ono, ndi alendo m'mwemo;

20 Nayendayenda kucokera mtundu wina kufikira mtundu wina,Kucokera ufumu wina kufikira anthu ena.

21 Sanalola munthu awasautse;Ndipo anadzudzula mafumu cifukwa ca iwowa;

22 Ndi kuti, Musamakhudza odzozedwa anga,Musamacitira coipa aneneri anga,

23 Myimbireni Yehova, inu dziko lonse lapansi,Lalikirani cipulumutso cace tsiku ndi tsiku,

24 Fotokozerani ulemerero wace mwa amitundu,Zodabwiza zace mwa mitundu yonse ya anthu.

25 Pakuti Yehova ali wamkuru, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;Ayenera amuope koposa milungu yonse.

26 Pakuti milungu ya mitundu ya anthu ndiyo mafano;Koma Yehova analenga zakumwamba.

27 Pamaso pace pali ulemu ndi ukulu,M'malo mwace muli mphamvu ndi cimwemwe.

28 Mcitireni Yehova, inu mafuko a mitundu ya anthu,Mcitireni Yehova ulemerero ndi mphamvu.

29 Mcitireni Yehova ulemerero wa dzina lace;Bwerani naco copereka, ndipo fikani pamaso pace;Lambirani Yehova m'ciyero cokometsetsa,

30 Njenjemerani pamaso pace, inu dziko lonse lapansi,Dziko lokhalamo anthu lomwe lakhazikika, kuti silingagwedezeke.

31 Kukondwerere kumwamba, ndi dziko lapansi lisekerere;Anene mwa amitundu, Yehova acita ufumu.

32 Nyanja ikukume m'kudzala kwace,Munda ukondwerere, ndi zonse ziri m'mwemo;

33 Pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzapfuula mokondwera pamaso pa Yehova;Pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi,

34 Yamikani Yehova; pakuti iye ndiye wabwino;Pakuti cifundo cace ncosatha.

35 Nimunene, Tipulumutseni, Mulungu wa cipulumutso cathu;Mutisokolotse ndi kutilanditsa kwa amitundu,Kuti tiyamike dzina lanu loyera,Ndi kudzitamandira naco cilemekezo canu.

36 Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli,Kuyambira kosayamba kufikira kosatha.Ndipo anthu onse anati, Amen! nalemekeza Yehova.

Cihema cosonkhanako cikhala ku Gibeoni

37 Ndipo anasiyako ku likasa la cipangano la Yehova Asafu ndi abale ace, atumikire kulikasa kosalekeza, monga umo mudzafunika tsiku ndi tsiku;

38 ndi Obedi Edomu, ndi abale ace makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi atatu; ndi Obedi Edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa akhale odikira;

39 ndi Zadoki wansembe, ndi abale ace ansembe, ku kacisi wa Yehova, pa msanje unali ku Gibeoni;

40 kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa la nsembe zopsereza, kosalekeza, m'mawa ndi madzulo, monga mwa zonse zilembedwa m'cilamulo ca Yehova adacilamulira Israyeli;

41 ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi osankhika otsalawo, ochulidwa maina, kuyamika Yehova; pakuti cifundo cace ncosatha;

42 ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi malipenga ndi nsanje za iwo akumveketsadi, ndi zoyimbira nyimbo za Mulungu; ndi ana a Yedutuni anakhala kucipata.

43 Ndipo anacoka anthu onse, yense ku nyumba yace, nabwera Davide kudalitsa nyumba yace.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29