1 Mbiri 21 BL92

Davide awerenga anthu; mliri ugwera Israyeli

1 Pamenepo Satana anaukira Israyeli, nasonkhezera Davide awerenge Israyeli.

2 Ndipo Davide anati kwa Yoabu ndi kwa akuru a anthu, Kawerengeni Israyeli kuyambira ku Beereseba kufikira ku Dani; nimundibwezere mau, kuti ndidziwe ciwerengo cao.

3 Nati Yoabu, Yehova aonjezere pa anthu ace monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? nanga afuniranji cinthuci mbuyanga, adzaparamulitsa Israyeli bwanji?

4 Koma mau a mfumu anamlaka Yoabu. Naturuka Yoabu, nakayendayenda mwa Aisrayeli onse, nadza ku Yerusalemu.

5 Ndipo Yoabu anapereka kwa Davide ciwerengo ca anthu owerengedwa. Ndipo Aisrayeli onse anali zikwi mazana khumi ndi limodzi osolola lupanga, ndi Yuda anali zikwi mazana anai mphambu makumi asanu ndi awiri akusolola lupanga,

6 Koma sanawerenga Alevi ndi Abenjamini pakati pao; pakuti mau a mfumu anamnyansira Yoabu.

7 Ndipo Mulungu anaipidwa naco cinthuci, cifukwa cace iye anakantha Israyeli.

8 Pamenepo Davide anati kwa Mulungu, Ndacimwa kwakukuru ndi kucita cinthu ici; koma tsopano, mucotse mphulupulu ya kapolo wanu, pakuti ndacita kopusa ndithu.

9 Ndipo Yehova ananena ndi Gadi mlauli wa Davide, ndi kuti,

10 Kanene kwa Davide kuti, Atero Yehova, Ndikuikira zitatu; dzisankhireko cimodzi ndikucitire ici.

11 Nadza Gadi kwa Davide, nanena naye, Atero Yehova, Dzitengereko;

12 kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la Yehova, ndilo mliri m'dzikomo, ndi mthenga wakuononga wa Yehova mwa malire onse a Israyeli, Ulingirire tsono, ndimbwezere mau anji iye amene anandituma ine?

13 Ndipo Davide anati kwa Gadi, Ndipsinjika kwambiri; ndigwere m'dzanja la Yehova, pakuti zifundo zace zicurukadi; koma ndisagwere m'dzanja la munthu.

14 Momwemo Yehova anatumiza mliri pa Israyeli; ndipo adagwapo amuna zikwi makumi asanu ndi awiri a Israyeli.

Davide amangira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Orinani

15 Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka coipaci; nati kwa mthenga wakuononga, Cakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi,

16 Ndipo Davide anakweza maso ace, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati pa dziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m'dzanja lace, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akuru obvala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.

17 Ndipo Davide anati kwa Mulungu, Si ndine nanga ndalamulira kuti awerenge anthu? Inde, ndine amene ndacimwa ndi kucita coipa ndithu; koma nkhosa izi zinacitanji? dzanja lanu, Yehova Mulungu wanga, Gnditsutse ine ndi nyumba ya atate wanga, koma Gsatsutse anthu anu ndi kuwacitira mliri.

18 Pamenepo mthenga wa Yehova anauza Gadi kuti anene ndi Davide, akwere Davideyo kuutsira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Orinani Myebusi,

19 Ndipo Davide anakwera monga mwa mau a Gadi adawanena m'dzina la Yehova.

20 Poceuka Orinani anaona wamthengayo; ndi ana ace amuna anai anali naye anabisala. Koma Orinani analikupuntha tirigu.

21 Ndipo pofika Davide kwa Orinani, Orinaniyo anapenyetsa, naona Davide, naturuka kudwale, nawerama kwa Davide, nkhope yace pansi.

22 Davide tsono anati kwa Orinani, Ndipatse padwale pano kuti ndimangepo guwa la nsembe la Yehova; undipatse gi pa mtengo wace wonse, kuti mliri ulekeke pa anthu.

23 Ndipo Orinani anati kwa Davide, Mulitenge, ndi mbuye wanga mfumu icite comkomera m'maso mwace; taonani, ndikupatsani ng'ombe za nsembe zopsereza; ndi zipangizo zopunthira zikhale nkhuni, ndi tirigu wa nsembe yaufa; ndizipereka zonse.

24 Koma mfumu Davide anati kwa Orinani, lai, koma ndidzaligula pa mtengo wace wonse; pakuti sindidzatengera Yehova ciri cako, kapena kupereka nsembe yopsereza yopanda mtengo wace.

25 Momwemo Davide anapatsa Orinani cogulira malowa golidi wa masekeli mazana asanu ndi limodzi kulemera kwace.

26 Ndipo Davide anamangira Yehova guwa la nsembe komweko; napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika, naitana kwa Yehova; ndipo anamyankha ali m'Mwamba ndi mota pa guwa la nsembe yopsereza.

27 Ndipo Yehova anauza wamthenga kuti abweze lupanga lace m'cimace.

28 Nthawi yomweyi, pakuona Davide kuti Yehova anambvomereza pa dwale la Orinani Myebusi, anaphera nsembe pomwepo.

29 Pakuti kacisi wa Yehova amene Mose anapanga m'cipululu, ndi guwa la nsembe yopsereza, zinali pa msanje wa ku Gibeoni nthawi yomweyi.

30 Kama Davide sanathe kumuka kukhomo kwace kufunsira kwa Mulungu, pakuti anaopa lupanga la mthenga wa Yehova.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29