1 Mbiri 7 BL92

Adzukulu a Isakara

1 Ana a Isakara ndiwo Tola, ndi Pua, Yasubu ndi Simironi; anai.

2 Ndi ana a Tola: Uzi, ndi Repaya, ndi Yerieli, ndi Yamai, ndi Ibsamu, ndi Semueli, akuru a nyumba za makolo; ao ndiwo a Tola, ngwazi zamphamvu, m'mibadwo yao; kuwerenga kwao masiku a Davide ndiko zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi limodzi.

3 Ndi mwana wa Uzi: Izrahiya; ndi ana a Izrahiya: Mikaeli, ndi Obadiya, ndi Yoeli, ndi Isiya; onse asanuwa ndiwo akuru.

4 Ndi pamodzi nao mwa mibadwo yao, mwa nyumba za makolo ao, panali magulu a nkhondo zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi, popeza anacuruka akazi ao ndi ana ao.

5 Ndi abale ao mwa mabanja onse a Isakara, ngwazi zamphamvu, oyesedwa mwa cibadwidwe cao, onsewa ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu zisanu ndi ziwiri.

Adzukulu a Benjamini ndi Nafitali

6 Ana a Benjamini ndiwo Bela, ndi Bekeri, ndi Yedyaeli, atatu.

7 Ndi ana a Bela: Ezboni, ndi Uzi, ndi Uzieli, ndi Yerimoti, ndi hi, asanu; akuru a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu, owerengedwa m'mabuku a cibadwidwe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza makumi atatu ndi anai.

8 Ndi ana a Bekeri: Zemira, ndi Yoasi, ndi Eliezeri, ndi Eliunai, ndi Omri, ndi Yeremoti, ndi Abiya, ndi Anatoti, ndi Alemeti. Onsewa ndiwo ana a Bekeri.

9 Ndipo anayesedwa mwa cibadwidwe cao, mwa mibadwo yao, akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu zikwi makumi awiri mphambu mazana awiri.

10 Ndi mwana wa Yedyaeli: Bilani; ndi ana a Bilani: Yeusi, ndi Benjamini, ndi Ehudi, ndi Kenana, ndi Zetani, ndi Tarasisi, ndi Ahisabara.

11 Onsewa ndiwo ana a Yedyaeli; ndiwo akuru a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu zikwi khumi mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana awiri akuturuka kugulu kunkhondo.

12 Sufimu yemwe ndi Hupimu ana a Iri, ndi Husimu mwana wa Aheri.

13 Ana a Nafuali: Yazieli, ndi Guni, ndi Yezeri, ndi Salumu, ana a Bila.

Adzukulu a Manase

14 Ana a Manase ndiwo Asrieli amene mkazi wace anambala, Koma mkazi wace wamng'ono Maramu anabala Makiri atate wa Gileadi;

15 ndi Makiri anadzitengera mkazi, mlongo wace wa Hupimu ndi Supimu, dzina lace ndiye Maaka. Ndipo dzina la mwana waciwiri wa Manase ndiye Tselofekadi. Ndi Tselofekadi anali ndi ana akazi.

16 Ndi Maaka mkazi wa Makiri anabala mwana, namucha dzina lace Peresi, ndi dzina la mbale wace ndiye Seresi, ndi ana ace ndiwo Ulamu, ndi Rakemu.

17 Ndi mwana wa Ulamu: Bedani; ndiwo ana a Gileadi mwana wa Makiri mwana wa Manase.

18 Ndi mlongo wace Hamoleketi anabala Isodi, ndi Abiezeri, ndi Mala.

19 Ndi ana a Semida ndiwo Ahiani, ndi Sekemu, ndi Liki, ndi Aniamu.

A Efraimu

20 Ndi ana a Efraimu: Sutera, ndi Beredi mwana wace, ndi Tahati mwana wace, ndi Ekada mwana wace, ndi Tahati mwana wace,

21 ndi Zabadi mwana wace, ndi Sutela mwana wace, ndi Ezeri, ndi Eleadi, amene anthu a Gadi obadwa m'dziko anamupha, popeza anatsikira kukalanda zoweta zao.

22 Ndipo Efraimu atate wao, anacita maliro masiku ambiri, ndi abale ace anadza kudzamtonthoza mtima.

23 Ndipo analowa kwa mkazi wace, naima iye, nabala mwana, namucha dzina lace Beriya, popeza m'nyumba mwace mudaipa.

24 Ndipo mwana wace wamkazi ndiye Seera, amene anamanga Beti-horoni wa kunsi, ndi Beti-horoni wa kumtunda, ndi Uzeniseera.

25 Ndipo Refa anali mwana wace, ndi Resefe, ndi Tela mwana wace, ndi Tahani mwana wace,

26 Ladana mwana wace, Amihudi mwana wace, Elisamu mwana wace,

27 Nuni mwana wace, Yoswa mwana wace.

28 Ndipo dziko lao, ndi pokhala pao ndizo Beteli ndi miraga yace, ndi kum'mawa Narani, ndi kumadzulo Gezeri ndi miraga yace, ndi Sekemu ndi miraga yace, mpaka Aza ndi miraga yace;

29 ndi kumalire a ana a Manase; Beteseani ndi miraga yace, Taanaki ndi miraga yace, Megido ndi miraga yace, Dora ndi miraga yace. M'menemo anakhala ana a Yosefe mwana wa Israyeli.

30 Ana a Aseri: Imna, ndi Isva, ndi Isvi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao.

31 Ndi ana a Beriya: Heberi, ndi Malikieli, ndiye atate wa Birizaiti.

32 Ndi Heberi anabala Yafteti, ndi Someri, ndi Hotamu, ndi Suwa mlongo wao.

33 Ndi ana a Yafteti: Pasaki, ndi Bimali, ndi Asvati. Awa ndi ana a Yafteti.

34 Ndi ana a Semeri: Ahi, ndi Roga, Yehuba, ndi Aramu.

35 Ndi ana a Helemu mbale wace: Zofa, ndi Imna, ndi Selesi, ndi Amali.

36 Ana a Zofa: Suwa, ndi Harineferi, ndi Sauli, ndi Beri, ndi Imra,

37 Bezeri, ndi Hndi, ndi Sama, ndi Silisa, ndi Itirani, ndi Beera.

38 Ndi ana a Yeteri: Yefune, ndi Pisipa, ndi Ara.

39 Ndi ana a Ula: Ara, ndi Hanieli, ndi Rizya.

40 Awa onse ndiwo ana a Aseri, akuru a nyumba za makolo ao, ngwazi zosankhika ndi zamphamvu, akuru mwa akalonga. Oyesedwa mwa cibadwidwe cao otumikira kunkhondo ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29