1 Mbiri 4 BL92

Adzukulu a Yuda

1 Ana a Yuda: Perezi, Hezroni, ndi Karmi, ndi Huri, ndi Sobala.

2 Ndipo Reaya mwana wa Sobala anabala Yahati; ndi Yahati anabala Ahumai, ndi Lahadi. Iwo ndiwo mabanja a Azorati.

3 Iwo ndiwo a atate wa Etamu: Yezreeli, ndi Isma, ndi Idibasi; ndipo dzina la mlongo wao ndiye Hazeleleponi,

4 ndi Penueli atate wa Gedoro, ndi Ezeri atate wa Husa. Awa ndi ana a Huri woyamba wa Efrata atate wa Betelehemu.

5 Ndipo Asuri atate wa Tekowa anali nao akazi awiri: Hela, ndi Naara.

6 Ndi Naara anambalira Ahuzamu, ndi Heferi, ndi Temeni, ndi Hahastario Iwo ndiwo ana a Naara.

7 Ndi ana a Hela ndiwo Zereti, lzara, ndi Etinani.

8 Ndipo Hakozi anabala Anubu, ndi Zobeba, ndi mabanja a Ahareli mwana wa Harumu.

9 Ndipo Yabezi analemekezedwa koposa abale ace; ndi mace anamucha dzina lace Yabezi, ndi kuti, Popeza ndambala mwaululu.

10 Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israyeli, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti coipa cisandibvute. Ndipo Mulungu anafikitsa copempha iye.

11 Ndipo Kelubu mbale wa Sua anabala Mehiri, ndiye atate wa Esitoni.

12 Ndi Esitoni anabala Betirafa, ndi Paseya, ndi Tehina atate wa Irinahasi. Awa ndi anthu a Reka.

13 Ndi ana a Kenazi: Otiniyeli, ndi Seraya; ndi mwana wa Otmiyeh: Hatati.

14 Ndipo Meonotai anabala Ofra; ndi Seraya anabala Yoabu atate wa Geharasimu; popeza iwo ndiwo amisiri.

15 Ndi ana a Kalebi mwana wa Yefune: Iru, Ela, ndi Naamu; ndi ana a Ela, ndi Kenazi.

16 Ndi ana a Yehaleleli: Ziti, ndi Zifa, Tiriya, ndi Asareli.

17 Ndi ana a Ezra: Yeteri, ndi Meredi, ndi Eferi, ndi Yaloni; ndipo anabala Miriamu, ndi Samai, ndi Isba atate wa Esitemowa.

18 Ndi mkazi wace Myuda anabala Yeredi atate wa Gedoro, ndi Heberi atate wa Soko, ndi Yekutiyeli atate wa Zanowa. Ndipo awa ndi ana a Bitiya mwana wamkazi wa Farao, amene Meredi anamtenga.

19 Ndi ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wace wa Nahamu, ndiwo atate a Kula Mgarimi ndi Esitemowa Mmaaka.

20 Ndi ana a Simoni; Amnoni, ndi Rina, Benehanana, ndi Tiloni. Ndi ana a lsi: Zoheti, ndi Benzoheti.

21 Ana a Sela mwana wa Yuda: Eri atate wa Leka, ndi Laada atate wa Maresa, ndi mabanja a nyumba ya iwo oomba bafuta wa thonje losansitsa a nyumba ya Asibeya,

22 ndi Yokimu, ndi amuna a Kozeba, ndi Yoasi, ndi Sarafa wolamulira m'Moabu, ndi Yasubilehemu; koma mau awa ndiwo a kale lomwe.

23 Iwo ndiwo oumba mbiya, ndi okhala m'Netaimu, ndi m'Gedera; anakhala komweko ndi mfumu m'nchito yace.

Adzukulu a Simeoni

24 Ana a Simeoni: Nemueli, ndi Yamini, Yaribi, Zera, Sauli,

25 Salumu mwana wace, Mibsamu mwana wace, Misma mwana wace.

26 Ndi ana a Misma: Hamueli mwana wace, Zakuri mwana wace, Simei mwana wace.

27 Ndipo Simei anali nao ana amuna khumi mphambu asanu ndi mmodzi, ndi ana akazi asanu ndi mmodzi; koma abale ace analibe ana ambiri, ndi banja lao lonse silinacurukitsa ngati ana a Yuda.

28 Ndipo anakhala ku Beereseba, ndi Molada, ndi Hazarasuala,

29 ndi ku Bila, ndi ku Ezemu, ndi ku Toladi,

30 ndi ku Betueli, ndi ku Horima, ndi ku Zikilaga,

31 ndi ku Betimarikaboti, ndi ku Hazarasusimu, ndi ku Betibiri, ndi ku Saraimu. Iyi ndi midzi yao, mpaka ufumu wa Davide, pamodzi ndi miraga yao.

32 Etamu, ndi Aini, Rimoni, ndi Tokeni, ndi Asani, midzi isanu;

33 ndi miraga yao yonse pozungulira pace pa midzi yomweyi, mpaka Baala. Apo ndi pokhala pao ndipo ali nao mawerengedwe a maina ao.

34 Ndi Mesobabu, ndi Yamleki, ndi Yosa mwana wa Amaziya,

35 ndi Yoeli, ndi Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asieli;

36 ndi Eliunai, ndi Yaakoba, ndi Yesohaya, ndi Asaya, ndi Adieli, ndi Yesimieli, ndi Benaya,

37 ndi Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simri, mwana wa Semaya;

38 awa ochedwa maina ndiwo akalonga m'mabanja ao, ndi nyumba za makolo ao zinacuruka kwambiri.

39 Ndipo anamuka mpaka polowera ku Gedoro kum'mawa kwa cigwa, kufunafuna podyetsa zoweta zao.

40 Ndipo anapeza podyetsa ponenepetsa ndi pabwino, ndipo dzikoli ndi lacitando ndi lndikha ndi losungikamo, pakuti okhalako kale ndiwo a Hamu.

41 Iwo tsono olembedwa maina anadza masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda, nakantha mahema ao ndi zokhalamo zao, naziononga konse mpaka lero, nakhala m'malo mwao; popeza panali podyetsa zoweta zao pamenepo.

42 Ndipo ena a iwowa a ana a Simeoni, amuna mazana asanu, anamka ku phiri la Seiri; akuwatsogolera ndiwo Pelatiya, ndi Neariya, ndi Refaya, ndi Uzieli; ana a lsi.

43 Nakantha otsala a Aamaleki adapulumukawo, nakhala komweko mpaka lero lino.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29