1 Mbiri 27 BL92

Ankhondo ndi akazembe ao

1 Ndipo ana a Israyeli monga mwa ciwerengo cao, kunena za akuru a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu nchito iri yonse ya magawidwe, akulowa ndi kuturuka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya caka, cigawo ciri conse nca amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai.

2 Woyang'anira cigawo coyamba ca mwezi, woyamba ndiye Yasobeamu mwana wa Zabidiyeli; m'cigawo mwace munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.

3 Ndiye wa ana a Perezi, mkuru wa akazembe onse a khamu mwezi woyamba.

4 Woyang'anira cigawo ca mwezi waciwiri ndiye Dodai M-ahohi ndi cigawo cace; ndi Mikiloti mtsogoleri, ndi m'cigawo cace munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.

5 Kazembe wacitatu wa khamu wa mwezi wacitatu ndiye Benaya mwana wa Yehoyada wansembe wamkuru; ndi m'cigawo mwacemunalinso zikwi makumi awiri mphambu zinai.

6 Benaya ameneyo ndiye wamphamvu uja wa makumi atatu aja, woyang'anira makumi atatu aja; woyang'anira cigawo cace ndi Amizabadi mwana wace.

7 Wacinai wa mwezi wacinai ndiye Asebeli mbale wa Yoabu, ndi pambuyo pace Zebadiya mwana wace; ndi m'cigawo mwace munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.

8 Kazembe wacisanu wa mwezi wacisanu ndiye Samuti M-izra; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.

9 Wacisanu ndi cimodzi wa mwezi wacisanu ndi cimodzi ndiye Ira mwana wa Ikesi Mtekoi; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.

10 Wacisanu ndi ciwiri wa mwezi wacisanu ndi ciwiri ndiye Helezi Mpeloni wa ana a Efraimu; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.

11 Wacisanu ndi citatu wa mwezi wacisanu ndi citatu ndiye Sibekai Mhusati wa Afera; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.

12 Wacisanu ndi cinai wa mwezi wacisanu ndi cinai ndiye Abiezeri M-anatoti wa Abenjamini; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.

13 Wakhumi wa mwezi wakhumi ndiye Maharai Mnetofati wa Azera; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.

14 Wakhumi ndi cimodzi wa mwezi wakhumi ndi cimodzi ndiye Benaya Mpiratoni wa ana a Efraimu; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.

15 Wakhumi ndi ciwiri wa mwezi wakhumi ndi ciwiri ndiye Heledai Mnetofati wa Otiniyeli; ndi m'cigawo mwace zikwi makumi awiri mphambu zinai.

Oyang'anira mafuko 12 a Israyeli

16 Koma oyang'anira mafuko a lsrayeli ndi awa: wa Arubeni mtsogoleri wao ndiye Eliezeri mwana wa Zikiri; wa Asimeoni, Sefatiya mwana wa Maaka;

17 wa Alevi, Hasabiya mwana wa Kemueli; wa Aroni, Zadoki;

18 wa Yuda, Elihu mbale wina wa Davide; wa Isakara, Omri mwana wa Mikaeli;

19 wa Zebuluni, Isimaya mwana wa Obadiya; wa Nafitali, Yeremoti mwana wa Azrieli;

20 wa ana a Efraimu, Hoseya mwana wa Azaziya; wa pfuko la Manase logawika pakati, Yoeli mwana wa Pedaya;

21 wa pfuko la Manase logawika pakati m'Gileadi, Ido mwana wa Zekariya; wa Benjamini, Yasiyeli mwana wa Abineri;

22 wa Dani, Azareli mwana wa Yerohamu. Awa ndi akazembe a mapfuko a Israyeli.

23 Koma Davide sanawerenga iwo a zaka makumi awiri ndi ocepapo, pakuti Yehova adati kuti adzacurukitsa Israyeli ngati nyenyezi za kuthambo.

24 Yoabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga, koma sanatsiriza; ndi mkwiyo unagwera Israyeli cifukwa ca ici, ndipo ciwerengo cao sicinalembedwa m'buku la mbiri ya mfumu Davide.

Oyang'anira a zace za Davide

25 Ndipo woyang'anira cuma ca mfumu ndiye Azimaveti mwana wa Adiyeli, ndi woyang'anira wa cuma ca m'minda, m'mizinda ndi m'miraga, ndi nyumba za nsanja, ndiye Yonatani mwana wa Uziya;

26 ndi woyang'anira iwo akugwira nchito ya m'munda yakulima nthaka ndiye Ezri mwana wa Kelubi;

27 ndi woyang'anira minda yamphesa ndiye Simeyi Mramati; ndi woyang'anira zipatso za minda yamphesa zisungike mosungiramo vinyo ndiye Zabidi Msifimi;

28 ndi woyang'anira mitengo yaazitona, ndi yamikuyu yokhala kuzidikha kunsi, ndiye Baala Hanani Mgederi; ndi woyang'anira zosungiramo mafuta ndiye Yoasi;

29 ndi woyang'anira ng'ombe zakudya m'Saroni ndiye Sitirai Msaroni; ndi woyang'anira ng'ombe za m'zigwa ndiye Safabi mwana wa Adilai;

30 ndi woyang'anira ngamira ndiye Obili M-israyeli; ndi woyang'anira aburu ndiye Yedeya Mmeronoti;

31 ndi woyang'anira zoweta zazing'ono ndiye Yazizi Mhagiri, Onsewa ndiwo akuru a zolemera zace za Davide.

32 Ndipo Yonatani atate wace wina wa Davide anali phungu, munthu wanzeru ndi mlembi; ndi Yehieli mwana wa Hakimoni anakhala ndi ana a mfumu;

33 ndi Ahitofeli anali phungu wa mfumu, ndi Husai M-ariki anali bwenzi la mfumu;

34 ndi wotsatana ndi Ahitofeli, Yehoyada mwana wa Benaya, ndi Abyatara; koma kazembe wa nkhondo ya mfumu ndiye Yoabu.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29