1 Ndipo kunali, pofikanso caka, nyengo yakuturuka mafumu, Yoabu anatsogolera khamu lamphamvu, napasula dziko la ana a Amoni, nadza, naumangira misasa Raba. Koma Davide anakhala ku Yerusalemu. Ndipo Yoabu anakantha Raba, naupasula.
2 Ndipo Davide anatenga korona wa mfumu yao kumcotsa pamutu pace, napeza kulemera kwace talente wa golidi; panalinso miyala ya mtengo wace pamenepo; ndipo anamuika pamutu pa Davide, naturutsa zankhondo za m'mudzimo zambiri ndithu.
3 Naturutsanso anthu anali m'mwemo, nawaceka ndi mipeni ya mana mano, ndi zipangizo zocekera zacitsulo, ndi nkhwangwa. Anatero Davide ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwera ku Yerusalemu.
4 Ndipo zitatha izi, inauka nkhondo ku Gezeri ndi Afilisti; pamenepo Sibekai Mhusati anapha Sipai wa ana a cimphona; ndipo anawagonjetsa.
5 Ndipo panalinso nkhondo ndi Afgisti; ndi Elihanani mwana wa Yairi anapha Lami mbale wa Goliati Mgiti, amene luti la mkondo wace linanga mtanda woombera nsaru.
6 Ndipo panalinso nkhondo ku Gati; kumeneko kunali munthu wa msinkhu waukuru, amene zala zace za kumanja ndi kumapazi ndizo makumi awiri mphambu zinai; zisanu ndi cimodzi ku dzanja liri lonse, ndi zisanu ndi cimodzi ku phazi liri lonse; nayenso anabadwa mwa cimphonaco.
7 Ndipo potonza Israyeli iyeyu Yonatani mwana wa Simeya mbale wace wa Davide anamkantha.
8 Awa anabadwa mwa cimphonaco ku Gati, koma anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ace.