1 Ndipo Davide ndi akazembe a gulu la nkhondo anapatulira utumikiwo ena a ana a Asafu, ndi a Hemani, ndi a Yedutuni, anenere ndi azeze, ndi zisakasa, ndi nsanje; ndi ciwerengo ca anchito monga mwa kutumikira kwao ndko:
2 a ana a Asafu: Zakuri, ndi Yosefe, ndi Netaniya, ndi Asarela, ana a Asafu; mwa cilangizo ca Asafu, wakunenera mwa cilangizo ca mfumu.
3 A Yedntuni, ana a Yedutuni: Gedaliya, ndi Zeri, ndi Yesaya, Hasabiya, ndi Matitiya, asanu ndi mmodzi; mwa cilangizo ca atate wao Yedutuni, ndiye wakunenera ndi kuyamika ndi kulemekeza Yehova ndi zeze.
4 A Hemani, ana a Hemani: Bukiya, Mataniya, Uziyeli, Sebuyeli, ndi Yerimoti, Hananiya, Hanani, Eliyata, Gidaliti, ndi Romamti-Ezeri, Yosibekasa, Maloti, Hotiri, Mahazioti;
5 awa onse ndiwo ana a Hemani mlauli wa mfumu m'mau a Mulungu, kuti akweze mphamvu yace. Ndipo Mulungu anapatsa Hemani ana amuna khumi ndi anai, ndi ana akazi atatu.
6 Onsewa anawalangiza ndi atate wao ayimbe m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, zisakasa ndi azeze; atumikire nazo m'nyumba ya Mulungu; ndipo Asafu, Yedutuni, ndi Hemani, anawalangiza ndi mfumu.
7 Ndipo ciwerengo cao, pamodzi ndi abale ao ophunzitsidwa ayimbire Yehova, onse anthetemya, ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu.
8 Ndipo anacita maere pa udikiro wao, analingana onse, ang'ono ndi akuru, mphunzitsi ndi wophunzira.
9 Maere oyamba tsono anagwera a banja la Asafu ndiye Yosefe; waciwiri Gedaliya, iye ndi abale ace, ndi ana ace khumi ndi awiri;
10 wacitatu Zakuri, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
11 wacinai Izri, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
12 wacisanu Netaniya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
13 wacisanu ndi cimodzi Bukiya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
14 wacisanu ndi ciwiri Yesarela: ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
15 wacisanu ndi citatu Yesaya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
16 wacisanu ndi cinai Mataniya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri:
17 wakhumi Simeyi, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
18 wakhumi ndi cimodzi Azareli, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
19 wakhumi ndi ciwiri Hasabiya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
20 wakhumi ndi citatu Subaeli, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
21 wakhumi ndi cinai Matitiya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
22 wakhumi ndi cisanu Yeremoti, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
23 wakhumi ndi cisanu ndi cimodzi Hananiya, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
24 wakhumi ndi cisanu ndi ciwiri Yosibekasa, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
25 wakhumi ndi cisanu ndi citatu Hanani, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
26 wakhumi ndi cisanu ndi cinai Maloti, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
27 wa makumi awiri Eliyata, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
28 wa makumi awiri ndi cimodzi Hotiri, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
29 wa makumi awiri ndi ciwiri Gidaliti, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
30 wa makumi awiri ndi citatu Mahazioti, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri;
31 wa makumi awiri ndi cinai RomamtiEzeri, ana ace ndi abale ace khumi ndi awiri.