1 Ndipo ana a Rubeni mwana woyamba wa Israyeli, (pakuti ndiye mwana woyamba; koma popeza anaipsa kama wa atate wace ukulu wace unapatsidwa kwa ana a Yosefe mwana wa Israyeli, koma m'buku la cibadwidwe asayesedwe monga mwa ukulu wace.
2 Pakuti Yuda anakula mphamvu mwa abale ace, ndi mtsogoleri anafuma kwa iyeyu, koma ukulu ngwa Yosefe);
3 ana a Rubeni mwana woyamba wa Israyeli: Hanoki, ndi Palu, Hezroni, ndi Karmi.
4 Ana a Yoeli: Semaya mwana wace, Gogi mwana wace, Simei mwana wace,
5 Mika mwana wace, Reaya mwana wace, Baala mwana wace,
6 Beera mwana wace, amene Tigilati Pilesere wa ku Asuri anamtenga ndende; ndiye kalonga wa Arubeni.
7 Ndi abale ace monga mwa mabanja ao, powerenga cibadwidwe ca mibadwo yao: akuru ndiwo Yeyeli, ndi Zekariya,
8 ndi Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yoeli, wokhala ku Aroeri, ndi kufikira ku Nebo ndi Baala-meoni;
9 ndi kum'mawa anakhala mpaka polowera kucipululu kuyambira mtsinje wa Firate; pakuti zoweta zao zinacuruka m'dziko la Gileadi.
10 Ndipo masiku a Sauli anagwirana nkhondo ndi Ahagiri, amene adagwa ndi dzanja lao; ndipo anakhala m'mahema mwao kum'mawa konse kwa Gileadi.
11 Ndi ana a Gadi anakhala pandunji pao m'dziko la Basana mpaka Saleka:
12 Yoeli mkuru wao, ndi Safamu waciwiri, ndi Yanai, ndi Safati m'Basana;
13 ndi abale ao a; nyumba za makolo ao: Mikaeli, ndi Mesulamu, ndi Seba, ndi Yorai, ndi Yakani, ndi Ziya, ndi Eberi; asanu ndi awiri.
14 Awa ndi ana a Abihaili, mwana wa Huri, mwana wa Yarowa, mwana wa Gileadi, mwana wa Mikaeli, mwana wa Yesisai, mwana wa Yado, mwana wa Buzi,
15 Ahi mwana wa Abdieli, mwana wa Guni, ndiye mkulu wa nyumba za makolo ao.
16 Ndipo anakhala m'Gileadi m'Basana, ndi m'midzi yace, ndi podyetsa pace ponse pa Saroni, mpaka malire ao.
17 Onsewo anawerengedwa monga mwa mabuku a cibadwidwe cao, masiku a Yotamu mfumu ya Yuda, ndi m'masiku a Yerobiamu mfumu ya Israyeli.
18 Ana a Rubeni, ndi a Gadi, ndi limodzi la magawo awiri a pfuko la Manase, ngwazi, amuna akugwira cikopa ndi lupanga, ndi kuponya mibvi, ozerewera nkhondo, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zinai mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi akuturuka kunkhondo.
19 Ndipo anagwirana nkhondo ndi Ahagari, ndi Yet uri, ndi Nafisi, ndi Nodabu.
20 Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagari anaperekedwa m'dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anapfuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira iye.
21 Ndipo analanda zoweta zao, ngamila zao zikwi makumi asanu, ndi nkhosa zikwi mazana awiri ndi makumi asanu, ndi aburu zikwi ziwiri, ndi amuna zikwi zana limodzi.
22 Pakuti adagwa, nafa ambiri, popeza nkhondoyi nja Mulungu. Ndipo anakhala m'malo mwao mpaka anatengedwa ndende.
23 Ndi ana a limodzi la magawo awiri a pfuko la Manase anakhala m'dziko; anacuruka kuyambira Basana kufikira Baala Herimoni, ndi Seniri, ndi phiri la Herimoni.
24 Ndipo akuru a nyumba za makolo ao ndi awa: Eferi, ndi lsi, ndi Elieli, ndi Azrieli, ndi Yeremiya, ndi Hodaviya, ndi Yadieli, anthu amphamvu ndithu, anthu omveka, akulu a nyumba za makolo ao.
25 Koma analakwira Mulungu wa makolo ao, nacita cigololo, ndi kutsata milungu ya mitundu ya anthu a m'dziko, amene Mulungu adaononga pamaso pao.
26 Ndipo Mulungu wa Israyeli anautsa mzimu wa Puli mfumu ya Asuri, ndi mzimu wa Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, ndiye anawatenga ndende; ndiwo Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, nafika nao ku Hala, ndi Habori, ndi Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, mpaka lero lino.