1 Ndipo Hiramu mfumu ya Turo anatumiza mithenga kwa Davide, ndi mikungudza, ndi amisiri omanga miyala, ndi amatabwa, kuti ammangire nyumba.
2 Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova adamkhazikitsa mfumu ya Israyeli; pakuti ufumu wace unakwezekadi, cifukwa ca anthu ace Israyeli.
3 Ndipo Davide anatenga akazi ena ku Yerusalemu, nabala Davide ana amuna ndi akazi ena.
4 Maina a ana anali nao m'Yerusalemu ndi awa: Samna, ndi Sobabu Natani, ndi Solomo,
5 ndi Ibara, ndi Elisua, ndi Elipeleti,
6 ndi Noga, ndi Nefegi, ndi Yafiya,
7 ndi Elisama, ndi Beliyada, ndi Elifeleti.
8 Pamene Afilisti anamva kuti anamdzoza Davide akhale mfumu ya Aisrayeli onse, Afilisti onse anakwera kufunafuna Davide; ndipo Davide anamva, nawaturukira.
9 Afilisti tsono anafika, nafalikira m'cigwa ca Refaimu.
10 Ndipo Davide anafunsira kwa Mulungu, kun, Ndikwere kodi kuyambana ndi Afilisti? mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova anati kwa iye, Kwera, pakuti ndidzawapereka m'dzanja lako.
11 Atafika tsono ku Baala Perazimu, Davide anawakantha komweko; nati Davide, Mulungu anapasula adani anga ndi dzanja langa, ngati pokhamulira madzi. Cifukwa cace analicha dzina la malowo Baala Perazimu.
12 Ndipo anasiyako milungu yao; nalamula Davide, ndipo anaitentha ndi moto.
13 Ndipo Afilisti anabwerezanso, nafalikira m'cigwamo.
14 Ndipo Davide anafunsiranso kwa Mulungu, nanena Mulungu naye, Usakwera kuwatsata, uwazungulire, nuwadzere pandunji pa mitengo ya mkandankhuku.
15 Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula kunsonga kwa mitengo ya mkandankhuku, pamenepo uturukire kunkhondo; pakuti Mulungu waturukira pamaso pako kukantha gulu la Afilisti.
16 Nacita Davide monga Yehova adamuuza, nakantha gulu la Afilisti kuyambira ku Gibeoni kufikira ku Gezeri.
17 Ndipo mbiri ya Davide inabuka m'maiko onse, nafikitsira Yehova kuopsa kwace pa amitundu onse.