1 Mbiri 22 BL92

Davide akonzeratu mirimo yakumanga kacisi

1 Ndipo Davide anati, Pano padzakhala nyumba ya Yehova Mulungu, ndi pano padzakhala guwa la nsembe yopsereza la Israyeli.

2 Ndipo Davide anati asonkhanitse alendo okhala m'dziko la Israyeli; iye naika osema miyala afukule miyala, aiseme kuti amange nayo nyumba ya Mulungu.

3 Nakonzeratu Davide citsulo cocuruka ca misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wocuruka wosauyesa kulemera kwace;

4 ndi mitengo yamikungudza yosaiwerenga; pakuti Asidoni ndi Aturo anabwera nayo kwa Davide mitengo yamikungudza yocuruka,

5 Ndipo Davide anati, Solomo mwana wanga ndiye mnyamata ndi wosakwima, ndi nyumba imene adzaimangira Yehova ikhale yaikuru yopambana, yomveka ndi ya ulemerero mwa maiko onse; ndiikonzeretu mirimo. Momwemo Davide anakonzeratu mocuruka asanamwalire.

Davide amlangiza Solomo ammangire Yehova nyumba

6 Pamenepo iye anaitana Solomo mwana wace, namlangiza ammangire Yehova Mulungu wa Israyeli nyumba.

7 Ndipo Davide anati kwa Solomo mwana wace, Kunena za ine, kumtima kwanga kudati, ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba.

8 Koma mau a Yehova anandidzera, kuti, Wakhetsa mwazi wocuruka, popeza wacita nkhondo zazikuru; sudzamangira dzina langa nyumba, popeza wakhetsa pansi mwazi wambiri pamaso panga;

9 taona, udzabala mwana, ndiye adzakhala munthu wa phe; ndipo nelidzampumulitsira adani ace onse pozungulirapo, pakuti dzina lace lidzakhala Solomo; ndipo ndidzapatsa Israyeli mtendere ndi bata masiku ace;

10 iyeyu adzamangira dzina langa nyumba; iye adzakhala mwana wanga, ndi Ine ndidzakhala Atate wace; ndipo ndidzakhazikitsa mpando wacifumu wa ufumu wace pa Israyeli kosalekeza.

11 Tsono, mwana wanga, Yehova akhale nawe; nulemerere, numange nyumba ya Yehova Mulungu wako monga ananena za iwe.

12 Cokhaci, Yehova akupatse nzeru ndi luntha, nakulangize za Israyeli, kuti usunge cilamulo ca Yehova Mulungu wako,

13 Momwemo udzalemerera, ukasamalira kucita malemba ndi maweruzo amene Yehova analangiza Mose za Israyeli; limbikatu, nulimbike mtima, usaope, usade mtima.

14 Taona tsono, m'kuzunzika kwanga ndinakonzeratu nyumba ya Yehova matalente zikwi zana limodzi a golidi, ndi matalente zikwi zikwi a siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, osayesa kulemera kwace, pakuti zidacurukaeli; mitengo yomwe ndi miyala ndakonzeratu; nuonjezereko.

15 Uli naonso anchito ocuruka ofukula miyala, ndi amisiri a miyala ndi a mitengo, ndi amuna onse aluso akucita nchito ziri zonse;

16 golidi, ndi siliva, ndi mkuwa, ndi citsulo, nzosawerengeka; nyamuka, nucite, Yehova akhale nawe.

17 Davide analangizanso akalonga a Israyeli athanelize Solomo mwana wace, ndi kuti,

18 Kodi Yehova Mulungu wanu sali nanu? sanakupumulitsani pambali ponse? pakuti anapereka nzika za m'dziko m'dzanja mwanga, ndi dziko lagonjetsedwa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa anthu ace.

19 Perekani tsono mtima ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu; ndipo nyamukani ndi kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti abwere nalo likasa la cipangano la Yehova, ndi zipangizo zopatulika za Mulungu, ku nyumba imene idzamangidwira dzina la Yehova.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29