1 Mbiri 8 BL92

Adzukulu a Benjamini ndi Sauli

1 Ndipo Benjamini anabala Bela mwana wace vyoyamba, Asibeli waciwiri, ndi Ahara wacitatu,

2 Noha wacinai, ndi Rafa wacisanu.

3 Ndi Bela anali ndi ana: Adara, ndi Gera, ndi Abihudi,

4 ndi Abisuwa, ndi Namani, ndi Ahowa,

5 ndi Gera, ndi Sefufani, ndi Huramu.

6 Ndi ana a Ehudi ndi awa: ndiwo akuru a nyumba za makolo ao a iwo okhala ku Geba, ndipo anawatenga ndende kumka ku Manahati,

7 natenga ndende Namani, ndi Ahiya, ndi Gera, ndipo, anabala Uza, ndi Ahihudi.

8 Ndipo Saharaimu anabala ana ku dziko la Moabu, atacotsa akazi ace Husimu ndi Baara.

9 Ndipo Hodesi mkazi wace anambalira Yohabu, ndi Zibiya, ndi Mesa, ndi Malikamu,

10 ndi Yeuzi, ndi Sakiya, ndi Mirima. Awa ndi ana ace akurua nyumbazamakolo ao.

11 Ndi Husimu anambalira Abitubu, ndi Elipaala.

12 Ndi ana a Elipaala: Eberi, ndi Misamu, ndi Semedi, amene anamanga Ono, ndi Ludi ndi miraga yace,

13 ndi Beriya, ndi Sema; ndiwo akuru a nyumba za makolo a iwo okhala m'Ayaloni, amene anathawitsa okhala m'Gati;

14 ndi Ahio, Sasaki, ndi Yeremoti,

15 ndi Zebadiya, ndi Aradi, ndi Ederi,

16 ndi Mikaeli, ndi Isipa, ndi Yoha, ana a Beriya;

17 ndi Zebadiya, ndi Mesulamu, ndi Hiziki, ndi Heberi,

18 ndi Ismerai, ndi Izliya, ndi Yobabu, ana a Elipaala;

19 ndi Yakimu, ndi Zikiri, ndi Zabidi,

20 ndi Elianai, ndi Ziletai, ndi Elieli,

21 ndi Adaya, ndi Beraya, ndi Simirati, ana a Simei;

22 ndi Isipani, ndi Eberi, ndi Elieli,

23 ndi Abidoni, ndi Zikiri, ndi Hanani,

24 ndi Hananiya, ndi Elamu, ndi Antotiya,

25 ndi Ifideya, ndi Penueli, ana a Sasaki;

26 ndi Samserai, ndi Sehariya, ndi Ataliya,

27 ndi Yaaresiya ndi Eliya, ndi Zikiri, ana a Yerohamu.

28 Awa ndi akuru a nyumba za makolo mwa mibadwo yao, ndiwo akuru anakhala m'Yerusalemu awa.

29 Ndipo m'Gibeoni anakhala atate a Gibeoni, dzina la mkazi wace ndiye Maaka;

30 ndi mwana wace woyamba ndiye Abidoni, opondana naye ndi Zuri, ndi Kisi, ndi Baala, ndi Nadabu,

31 ndi Gedoro, ndi Ahiyo, ndi Zekeri.

32 Ndipo Mikiloti anabala Simeya. Ndi iwonso anakhala pamodzi ndi abale ao m'Yerusalemu, popenyana ndi abale ao.

33 Ndipo Neri anabala Kisi, ndi Kisi anabala Sauli, ndi Sauli anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esibaala.

34 Ndi mwana wa Yonatani ndiye Meri-baala; ndi Meri-baala anabala Mika.

35 Ndi ana a Mika: Pitoni, ndi Meleki, ndi Tareya, ndi Ahazi.

36 Ndi Ahazi anabala Yehoada, ndi Yehoada anabala Alemeti, ndi Azimaveti, ndi Zimri; ndi Zimri anabala Moza;

37 ndi Moza anabala Bineya, mwana wace ndiye Rafa, mwana wace Eleasa, mwana wace Azeli;

38 ndipo Azeli anali nao ana asanu ndi mmodzi, maina ao ndiwo Azrikamu, Bokeru, ndi Ismayeli, ndi Seariya, ndi Obadiya, ndi Hanani. Onsewa ndiwo ana a Azeli.

39 Ndi ana a Ezeki mbale wace: Ulamu mwana wace woyamba, Yeusi waciwiri, ndi Elifeleti wacitatu.

40 Ndipo ana a Ulamu ndiwo ngwazi zamphamvu, ndiwo oponya mibvi, nakhala nao ana ambiri ndi zidzukulu zana limodzi. Onsewa ndiwo a ana a Benjamini.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29