1 Mbiri 12 BL92

Amphamvu anadza kwa Davide namtsata pomlonda Sauli

1 Anadzawo kwa Davide ku Zikilaga, akali citsekedwere cifukwa ca Sauli mwana wa Kisi, ndi awa; ndiwo mwa amphamvuwo omthandiza kunkhondo.

2 Anakoka mauta; naponya miyala, naponya mibvi ndi uta ndi dzanja lamanja ndi lamanzere lomwe; ndiwo a abale ace a Sauli, Abenjamini.

3 Mkuru wao ndiye Ahiezeri, ndi Yoasi, ana a Semaa wa ku Gibeya; ndi Yezieli, ndi Peleti, ana a Azmaveti; ndi Beraka, ndi Yehu wa ku Anatoti,

4 ndi Ismaya wa ku Gibeoni, wamphamvu mwa makumi atatuwo ndi woyang'anira makumi atatuwo, ndi Yeremiya, ndi Yahazieli, ndi Yohanani, ndi Yozabadi wa ku Gedera,

5 Eluzai, ndi Yerimoti, ndi Bealiya, ndi Semariya, ndi Sefatiya wa ku Harupi,

6 Elikana, ndi Isiya, ndi Azereli, ndi Yoezeri, ndi Yasobeamu ndiwo Akora;

7 ndi Yoda, ndi Zebadiya, ana a Yerohamu wa ku Gedoro.

8 Ndi Agadi ena anapambukira kwa Davide ku liogala m'cipululu, ngwazi zamphamvu zozerewera nkhondo, zogwira cikopa ndi mkondo; nkhope zao zikunga nkhope za mikango, ndi liwiro lao longa la ngoma kumapiri:

9 Ezeri mkuru wao, waciwiri Obadiya, wacitatu Eliabu,

10 wacinai Misimana, wacisanu Yeremiya,

11 wacisanu ndi cimodzi Atai, wacisanu ndi ciwiri Elieli,

12 wacisanu ndi citatu Yohanani, wacisanu ndi cinai Elzabadi,

13 wakhumi Yeremiya, wakhumi ndi cimodzi Makibanai.

14 Awa a ana a Gadi, anali atsogoleri a nkhondo; wamng'ono wa iwo anayang'anira zana limodzi, ndi wamkuru wa iwo anayang'anira cikwi cimodzi.

15 Awa ndi omwe aja anaoloka Yordano mwezi woyamba, atadzala kusefukira magombe ace onse; nathawitsa onse okhala m'zigwa kum'mawa ndi kumadzulo.

16 Ndipo anadza ena a ana a Benjamini ndi Yuda kulinga kwa Davide.

17 Ndipo Davide anaturuka kukomana nao, nayankha, nanena nao, Ngati mwandidzera mwamtendere kundithandiza, mtima wanga udzalumikizana nanu; koma ngati mwafika kundipereka kwa adani anga, popeza m'manja mwanga mulibe ciwawa, Mulungu wa makolo athu acione ndi kucilanga.

18 Pamenepo mzimu unabvala Amasai, ndiye wamkuru wa makumi atatuwo, nati iye, Ndife anu, Davide, tibvomerezana nanu mwana wa Jese inu: mtendere, mtendere ukhale ndi inu, ndi mtendere ukhale ndi athandizi anu; pakuti Mulungu wanu akuthandizani. Ndipo Davide anawalandira, nawaika akuru a magulu.

19 Ena a Manase omwe anapambukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Sauli, koma sanawathandiza; popeza akalonga a Afilisti, atacita upo, anamuuza acoke, ndi kuti, Adzapambukira kwa mbuye wace Sauli ndi kutisandulikira.

20 Pomuka iye ku Zikilaga anapambukira kwa iye a Manase: Adina, ndi Yozabadi, ndi Yedyaeli, ndi Mikaeli, ndi Yozabadi, ndi Elihu, ndi Ziletai, akuru a zikwi a ku Manase.

21 Ndipo anathandiza Davide aponyane nalo gulu la acifwamba, pakuti onse ndiwo ngwazi zamphamvu, nakhala atsogoleri m'khamu la nkhondo.

22 Pakuti nthawi yomweyo anadza kwa Davide kumthandiza, mpaka kunali nkhondo yaikuru; ngati nkhondo ya Mulungu.

Akuru omponya Davide mfumu: ku Hebroni

23 Ndipo kuwerenga kwa akuru okonzekeratu kunkhondo, anadzawo kwa Davide ku Hebroni, kupambukitsa ufumu wa Sauli ukhale wace, monga mwa mau a Yehova, ndi: uku.

24 Ana a Yuda akunyamula zikopa ndi mikondo ndiwo zikwi zisanu ndi cimodzi mphambu mazana asanu ndi atatu, okonzekeratu kunkhondo.

25 A ana a Simeoni ngwazi zamphamvu za nkhondo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu zana liimodzi.

26 A ana a Levi zikwi zinai mphambu mazana asanu ndi limodzi.

27 Ndipo Yehoyada, ndiye mtsogoleri wa Aaroni, ndi pamodzi nave zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi awiri;

28 ndi Zadoki, ndiye mnyamata, ngwazi yamphamvu, ndi a nyumba ya kholo lace, akuru makumi awiri mphambu awfri.

29 Ndi a ana a Benjamini, abale a Sauli, zikwi zitatu; pakuti mpaka pomwepo ocuruka a iwowa anaumirira nyumba ya Sauli.

30 Ndi a ana a Efraimu zikwi makumi awiri mphambu mazana asanu ndi atatu, ngwazi zamphamvu, anthu omveka m'nyumba za makolo ao.

31 Ndipo a pfuko la Manase logawika pakati zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ochulidwa maina ao kuti adzalonge Davide mfumu.

32 Ndi a ana a Isakara, anthu akuzindikira nyengo, akudziwa zoyenera Israyeli kuzicita, akuru ao ndiwo mazana awiri; ndi abale ao onse anapenyerera pakamwa pao.

33 A Zebuloni akuturuka kukhamu, opangira nkhondo, monga mwa zida ziri zonse za nkhondo, zikwi makumi asanu, akusunga malongosoledwe a nkhondo ndi mtima wosatekeseka.

34 Ndi a Nafitali atsogoleri cikwi cimodzi, ndi pamodzi nao ogwira zikopa ndi mikondo zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri.

35 Ndi a Adani akupangira nkhondo zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu kudza mazana asanu ndi limodzi.

36 Ndi a Aseri akuturuka kukhamu, akupangira nkhondo, zikwi makumi anai.

37 Ndi tsidya lga la Yordano a Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la: Manase logawika pakati, ndi zida: ziri zonse za khamu kucita nazo nkhondo, zikwi zana limodzi ndi makumi awiri.

38 Onsewa, ndiwo anthu a nkhondo akusunga malongosoledwe a nkhondo, anadza ku Hebroni ndi mtima wangwiro kudzamlonga Davide mfumu ya Aisraeli onse; ndi onse otsala a Israyeli omwe anali a mtima umodzi kumlonga Davide ufumu.

39 Ndipo anali komweko kwa Davide masiku atatu kudya ndi kumwa, popeza abale ao-anazikonzeratu.

40 Ndiponso akuyandikizana nao mpaka Isakara ndi Zebuloni ndi Nafitali anabwera nao mkate osenzetsa aburu, ndi ngamira, ndi nyuru, ndi ng'ombe, zakudya zaufa, ndi ncinci zankhuyu, ndi ncinci zamphesa, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ng'ombe, ndi nkhosa zocuruka; pakuti munali cimwemwe m'Israyeli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29