1 Mbiri 9 BL92

Okhala m'Yerusalemu atabwera kucokera ku Babulo

1 Ndipo Aisrayeli onse anawerengedwa mwa cibadwidwe cao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israyeli; ndipo Yuda anatengedwa ndende kumka ku Babulo cifukwa ca kulakwa kwao.

2 Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwao mwao m'roidzi mwao, ndiwo Israyeli, ansembe, Alevi, ndi Anetini.

3 Ndipo m'Yerusalemu munakhala a ana a Yuda, ndi a ana a Benjamini, ndi a ana a Efraimu ndi Manase:

4 Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omri, mwana wa Imri, mwana wa Bani, wa ana a Perezi mwana wa Yuda.

5 Ndipo a Asiloni: Asaya woyamba, ndi ana ace.

6 Ndi a ana a Zera: Yeueli ndi abale ao mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi anai.

7 Ndi a ana a Benjamini: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodavia, mwana wa Hasenuwa;

8 ndi Ibineya mwana wa Yerohamu, ndi Ela mwana wa Uzi, mwana-wa Mikiri, ndi Mesulamu mwana wa Sefatiya, mwana wa Reueli, mwana wa Ibniya,

9 ndi abale ao monga mwa mibadwo yao mazana asanu ndi anai mphambu makumi asanu kudza asanu ndi mmodzi. Onsewa ndiwo akuru a nyumba za makolo ao m'nyumba za makolo ao.

10 Ndi a ansembe: Yedaya, ndi Yehoyaribu, ndi Yakini,

11 ndi Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubu, mtsogoleri wa m'nyumba ya Mulungu;

12 ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya, ndi Maasai mwana wa Adieli, mwana wa Yazera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemiti, mwana wa Imeri,

13 ndi abale ao, akuru a nyumba za makolo ao cikwi cimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi, anthu odziwitsitsa Debito ya utumiki wa nyumba ya Mulungu.

14 Ndi a Alevi: Semaya mwana wal Hasubu, mwana wa Azrikamu, mwana wa Hasabiya, a ana a Merari;

15 ndi Bakabakara, Heresi, ndi Galala, ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu;

16 ndi Obadiya mwana wa Semaya, mwana wa Galala, mwana wa Yedutuni, ndi Berekiya mwana wa Asa, mwana wa Elikana, wokhala m'midzi ya Anetofati.

17 Ndi odikira pakhomo: Salumu, ndi Akubu, ndi Talimoni, ndi Ahimani ndi abate ao; Salumu ndi mkuru wao,

18 amene adadikira pa cipata ca mfumu kum'mawa mpaka pomwepo, ndiwo odikira pakhomo a tsasa la ana a Levi.

19 Ndipo Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiasafu; mwana wa Kora, ndi abale ace a nyumba ya atate wace; Akora anayang'anira nchito ya utumiki, osunga zipata za kacisi monga makolo ao; anakhala m'cigono ca Yehova osunga polowera;

20 ndi a Pinehasi mwana wa Eleazara anali mtsogoleri wao kale, ndipo Yehova anali naye.

21 Zekariya mwana wa Meselemiya anali wodikira pakhomo pa cihema cokomanako.

22 Iwo onse osankhidwa akhale odikira kuzipata ndiwo mazana awiri mphambu khumi ndi awiri. Iwo anawerengedwa monga mwa cibadwidwe cao, m'midzi mwao, amene Davide ndi Samueli mlauli anawaika m'udindo wao.

23 Momwemo iwo ndi ana ao anayang'anira zipata za ku nyumba ya Yehova, ndiyo nyumba ya kacisi, m'udikiro wao.

24 Pa mbali zinai panali odikira kum'mawa, kumadzulo, kumpoto, ndi kumwela.

25 Ndi abale ao m'midzi mwao akafikafika, atapita masiku asanu ndi awiri masabata onse, kuti akhale nao;

26 pakuti odikira anai akuru, ndiwo Alevi, anali m'udindo wao, nayang'anira zipinda ndi mosungiramo cuma m'nyumba ya Mulungu.

27 Ndipo amagona usiku m'zipinda zozinga nyumba ya Mulungu, popeza udikiro wace ndi wao; kuitsegula m'mawa ndi m'mawa ndi kwaonso.

28 Ndi ena a iwo anayang'anira zipangizo za utumikiwo, pakuti analowa nazo ataziwerenga, naturuka nazo ataziwerenga.

29 Ndi ena a iwo anaikidwa ayang'anire zipangizo ziti zonse, ndi zipangizo zonse za malo opatulika, ndi ufa wosalala, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi libano, ndi zonunkhira.

30 Ndi ana ena a, ansembe anasanganiza cisanganizo ca zonunkhira,

31 Ndi Matitiya wina wa Alevi, ndiye mwana woyamba wa Salumu Mkora, anaikidwa ayang'anire zokazingidwa m'ziwaya.

32 Ndi ena a abale ao, a ana a Akohati, anayang'anira mkate woonekera, kuukonza masabata onse.

33 Ndipo awa ndi oyimba akuru a nyumba za makolo a Alevi, okhala m'zipinda, omasuka ku nchito zina; pakuti anali nayo nchito yao usana ndi usiku.

34 Awa ndi akuru a nyumba za makolo a Alevi mwa mibadwo yao, ndiwo akuru; anakhala ku Yerusalemu awa.

35 Ndipo m'Gibeoni munakhala atate wa Gibeoni Yeieli, dzina la mkazi wace ndiye Maaka;

36 ndi mwana wace woyamba ndiye Abidoni, opandana naye ndi Zuri, ndi Kisi, ndi Baala, ndi Neri, ndi Nadabu,

37 ndi Gedoro, ndi Ahiya, ndi Zekariya, ndi Mikiloti.

38 Ndi Mikiloti anabala Simeamu. Ndipo iwonso anakhala pamodzi ndi abale ao m'Yerusalemu, pandunji pa abale ao.

39 Ndipo Neri anabala Kisi, ndi Kisi anabala Sauli, ndi Sauli anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esbaala.

40 Ndipo mwana wa Yonatani ndiye Meribaala; ndi Meribaala anabala Mika.

41 Ndi ana a Mika: Pitoni, ndi Meleki, ndi Tareya, ndi Ahazi.

42 Ndi Ahazi anabala Yara, ndi Yara anabala Ameleti, ndi Azmaveti, ndi Zimri; ndi Zimri anabala Moza,

43 ndi Moza anabala Bineya, ndi Refaya mwana wace, Eleasa mwana wace; Azeli mwana wace;

44 ndi Azeli anali nao ana asanu ndi mmodzi, maina ao ndi awa; Azrikamu, Bokeru, ndi Ismayeli, ndi Seariya, ndi Obadiya, ndi Hanani; awa ndi ana a Azeli.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24 25 26 27 28 29