1 Ana a Levi: Gerisomu, Kohati, ndi Merari.
2 Ndi ana a Kohati: Amramu, Izara, ndi Hebroni, ndi Uzieli.
3 Ndi ana a Amramu: Aroni, ndi Mose, ndi Miriamu. Ndi ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.
4 Eleazara anabala Pinehasi, Pinehasi anabala Abisua,
5 ndi Abisua anabala Buki, ndi Buki anabala Uzi,
6 ndi Uzi anabala Zerahiya, ndi Zerahiya anabala Merayoti,
7 Merayoti anabala Amariya, ndi Amariya anabala Ahitubu,
8 ndi Ahitubu anabala Zadoki, ndi Zadoki anabala Ahimaazi,
9 ndi Ahimaazi anabala Azariya, ndi Azariya anabala Yohanani,
10 ndi Yohanani anabala Azariya (ndiye amene anacita nchito ya nsembe m'nyumba anaimanga Solomo m'Yerusalemu),
11 ndi Azariya anabala Amariya, ndi Amariya anabala Ahitubu,
12 ndi Ahitubu anabala Zadoki, ndi Zadoki anabala Salumu,
13 ndi Salumu anabala Hilikiya, ndi Hilikiya anabala Azariya,
14 ndi Azariya anabala Seraya, ndi Seraya anabala Yehozadaki,
15 ndi Yehozadaki analowa undende muja Yehova anatenga ndende Yuda ndi Yerusalemu ndi dzanja la Nebukadinezara.
16 Ana a Levi: Gerisomu, Kohati ndi Merari.
17 Ndipo maina a ana a Gerisomu ndi awa: Libni, ndi Simei.
18 Ndipo ana a Kohati ndiwo Amramu, ndi lzara, ndi Hebroni, ndi Uzieli.
19 Ana a Merari: Mali ndi Musi. Ndi mabanja a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao ndi awa.
20 Wa Gerisomu: Libni mwana wace, Yahati mwana wace, Zina mwana wace,
21 Yowa mwana wace, Ido mwana wace, Zera mwana wace, Yeaterai mwana wace.
22 Ana a Kohati: Aminadabu mwana wace, Kora mwana wace, Asiri mwana wace,
23 Elikana mwana wace, ndi Ebiasafu mwana wace, ndi Asiri mwana wace,
24 Tahati mwana wace, Urieli mwana ware, Uziya mwana wace, ndi Sauli mwana wace.
25 Ndi ana a Elikana: Amasai, ndi Ahimoti.
26 Elikana: ana a Elikana Zofai mwana wace, ndi Nahati mwana wace,
27 Eliabu mwana wace, Yerohamu mwana wace, Elikana mwana wace.
28 Ndi ana a Samueli: woyamba Yoeli, ndi waciwiri Abiya.
29 Ana a Merari: Mali, Libni mwana wace, Simei mwana wace, Uza mwana wace,
30 Simeya mwana wace, Hagiya mwana wace, Asaya mwana wace.
31 Ndipo iwo aja Davide anawaimika a udindo wa nyimbo m'nyumba ya Yehova, litafikira kupumula likasalo, ndi awa.
32 Ndipo anatumikira ndi kuyimba pakhomo pa kacisi wa cihema cokomanako mpaka Solomo adamanga nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, naimirira m'utumiki wao monga mwa malongosoledwe ao.
33 Ndipo oimirirawo, ndi ana ao, ndi awa: a ana a Akohati, Hemani woyimbayo, mwana wa Yoeli, mwana wa Samueli,
34 mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu, mwana wa Elieli, mwana wa Towa,
35 mwana wa Zufi, mwana wa Elikana, mwana wa Mahati, mwana wa Amasai,
36 mwana wa Elikana, mwana wa Yoeli, mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya,
37 mwana wa Tahati, mwana wa Asiri, mwana wa Abiasafu, mwana wa Kora,
38 mwana wa Izara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, mwana wa Israyeli.
39 Ndi mbale wace Asafu wokhala ku dzanja lace lamanja, ndiye Asafu mwana wa Berekiya, mwana wa Simeya,
40 mwana wa Mikaeli, mwana wa Baaseya, mwana wa Malikiya,
41 mwana wa Etini, mwana wa Zera, mwana wa Adaya,
42 mwana wal Edani, mwana wa Zima, mwana wa Simeyi,
43 mwana wa Yabati, mwana wa Gerisomu, mwana wa Levi.
44 Ndi ku dzanja lamanzere abale ao ana a Merari: Etani mwana wa Kisi, mwana wa Abidi, mwana wa Maluki,
45 mwana wa Hasabiya, mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya,
46 mwana wa Amzi, mwana wa Bani, mwana wa Semeri,
47 mwana wa Mali, mwana wa Musi, mwana wa Merari, mwana wa Levi.
48 Ndi abale ao Alevi anaikidwa acite za utumiki ziti zonse za kacisi wa nyumba ya Mulungu.
49 Koma Aroni ndi ana ace adafofukiza pa guwa la nsembe yopsereza, ndi pa guwa la nsembe yofukiza, cifukwa ca nchito yonse ya malo opatulikitsa, ndi kucitira Israyeli cowatetezera, monga mwa zonse Mose mtumiki wa Mulungu adawauza.
50 Ndipo ana a Aroni ndiwo Eleazara mwana wace, Pinehasi mwana wace, Abisua mwana wace,
51 Buki mwana wace, Uzi mwana wace, Zerobiya mwana wace,
52 Merayoti mwana wace, Amariya mwana wace, Ahitubu mwana wace,
53 Zadoki mwana wace, Ahimaazi mwana wace.
54 Pokhala pao tsono monga mwa madera ao m'malire mwao ndi awa: kwa ana a Aroni a mabanja a Akobati, pakuti maere oyamba adagwera iwowa,
55 kwa iwo anapereka Hebroni m'dziko la Yuda, ndi podyetsa pace pozungulira pace;
56 koma minda ya mudzi ndi miraga yace anapatsa Kalebi mwana wa Yefune.
57 Ndi kwa ana a Aroni anapereka midzi yopulumukirako: Hebroni, ndi Libina ndi mabusa ace, ndi Yatiri, ndi Esitemowa ndi mabusa ace,
58 ndi Hileni ndi mabusa ace, ndi Debiri ndi mabusa ace,
59 ndi Asani ndi mabusa ace, ndi Betesemesi ndi mabusa ace;
60 ndi ku pfuko la Benjamini Geba ndi mabusa ace, ndi Alemeti ndi mabusa ace, ndi Anatoti ndi mabusa ace. Midzi yao yonse mwa mabanja ao ndiyo midzi khumi ndi itatu.
61 Ndipo otsala a ana a Kohati analandira mwa maere, motapa pa mabanja a pfuko, pa pfuko la Manase logawika pakati, midzi khumi.
62 Ndi kwa ana a Gerisomu monga mwa mabanja ao, motapa pa pfuko la Isakara, ndi pa pfuko la Aseri, ndi pa pfuko la Nafitali, ndi pa pfuko la Manase m'Basana, midzi khumi ndi itatu.
63 Ana a Merari analandira mwa maere monga mwa mabanja ao, motapa pa pfuko la Rubeni, ndi pa pfuko la Gadi, ndi pa pfuko la Zebuluni, midzi khumi ndi iwiri.
64 Ndipo ana a Israyeli anapatsa Alevi midzi ndi mabusa ao.
65 Ndipo anapatsa mwamaere, motapa pa pfuko la ana a Yuda, ndi pa pfuko la Simeoni, ndi pa pfuko la ana a Benjamini, midzi iyi yochulidwa maina ao.
66 Ndi mabanja ena a ana a Kohati anali nayo midzi ya malire ao, yotapa pa pfuko la Efraimu.
67 Ndipo anawapatsa midzi yopulumukiramo: Sekemu ndi mabusa ace ku mapiri a Efraimu, Gezeri ndi mabusa ace,
68 ndi Yokimeamu ndi mabusa ace, ndi Betihoroni ndi mabusa ace,
69 ndi Ayaloni ndi mabusa ace, ndi Gatirimoni ndi mabusa ace,
70 ndi motapa pa pfuko la Manase logawika pakati, Aneri ndi mabusa ace, ndi Bileamu ndi mabusa ace, kwa otsala a mabanja a ana a Kohati.
71 Ana a Gerisomu analandira motapa pa mabanja a pfuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basana ndi mabusa ace, ndi Asitaroti ndi mabusa ace;
72 ndi motapa pa pfuko la Isakara, Kedesi ndi mabusa ace, Daberati ndi mabusa ace,
73 ndi Ramoti ndi mabusa ace, ndi Anemu ndi mabusa ace;
74 ndi motapa pa pfuko la Aseri, Masala ndi mabusa ace, ndi Abidoni ndi mabusa ace,
75 ndi Hukoki ndi mabusa ace, ndi Rehobu ndi mabusa ace;
76 ndi motapa pa pfuko la Nafitali, Kadesi m'Galileya ndi mabusa ace, ndi Hamoni ndi mabusa ace, ndi Kiriyataimu ndi mabusa ace.
77 Otsala a Alevi analandira, motapa pa pfuko la Zebuluni, Rimono ndi mabusa ace, Tabora ndi mabusa ace;
78 ndi tsidya lija la Yordano kum'mawa kwa Yordano analandira, motapa pa pfuko la Rubeni, Bezeri m'cipululu ndi mabusa ace, ndi Yaza ndi mabusa ace,
79 ndi Kedemoti ndi mabusa ace, ndi Mefati ndi mabusa ace;
80 ndi motapa m'pfuko la Gadi, Ramoti m'Gileadi ndi mabusa ace, ndi Mahanaimu ndi mabusa ace,
81 ndi Hezboni ndi mabusa ace, ndi Yazeri ndi mabusa ace.